Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ku Namibia Kuli Zoumba Zosunthasuntha

Ku Namibia Kuli Zoumba Zosunthasuntha

Ku Namibia Kuli Zoumba Zosunthasuntha

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU SOUTH AFRICA

WOUMBAYO akungosinthasintha maumbidwe ake, koma zikukongolabe. Akuumba ndi mchenga. Kodi woumbayu ndani? Ndi mphepo imene imaunjika miyulu ya mchenga n’kumaoneka ngati zinthu zosiyanasiyana. Mwina chinthu chodziŵika kwambiri ndicho chooneka ngati mwezi umene wangokhala kumene. Mbali ya “choumbachi” imene kukuchokera mphepo imatundumuka pang’onopang’ono, koma mbali imene kukupita mphepo imapanga chiphedi chachifupi. Pamwamba pa mulu wa mchengapo pamaoneka pakuthwa kwambiri, ngakhale kuti pangabunthiretu mutangomenyapo theche pang’ono.

Malo abwino okaona zoumba zosunthasuntha zimenezi ndiwo chipululu cha Namib chomwe chili kumwera chakumadzulo kwa Africa. Kumeneku kuli miyulu ina yamchenga yaitali kwambiri padziko lonse ndipo imatalika kupitirira mamita 400. Komabe, chipululu cha Namib n’chaching’ono pochiyerekezera ndi zipululu zina zazikulu kwambiri padziko lonse. Chinayambira kunyanja ya Atlantic n’kuloŵera kumtunda makilomita 160 ndipo n’chachitali makilomita 1,900.

Amisiri Enanso Pantchito Yawo

Mphepo si m’misiri yekhayo amene amapezeka kumalo akutali ameneŵa ‘opezekako zaluso.’ Mukayang’anitsitsa miyuluyi mungathe kuona zinthu zina zosonyeza kuti kulidi amisiri ena. Mwachitsanzo, pamchengapo mungaone patalembekalembeka mkukuluzi wooneka ngati mzere wautali, wosalala ndiponso wolukanalukana. Ngati mutadikira ndithu, mungathe kuona amisiri ake ali pantchito yawo. “Mzere wolukanalukanawu” umalembedwa ndi miyendo ya nkhululu zikamayenda pamchengapo usiku. Mosatalikirana kwambiri ndi ‘mzere’ pali mzere wolingana wooneka ngati mabowo ang’onoang’ono okhala mumchenga. Uwunso ndi mzere wolembedwa ndi mapazi a mbewa. Mosayembekezera mumaona kuti malo akutali oonetsako zaumisiri ameneŵa omwe amakhala ngati kulibe zamoyo, ali nazo zamoyo zambirimbiri.

Chakumpoto, m’mphepete mwa chigwa choopsa chotchedwa Skeleton Coast, mungaone ntchito ya amisiri ena a m’chipululu. Iwo amamwalamwaza mchengawo, ndipo amapanga zinthu zosalongosoka m’maonekedwe. Taonani! Ndi amenewo ali jidigajidiga pamchengapo. N’zosalira kufunsa ngati iwo amasangalala ndi luso lawo. Nyama zazikulu zimenezi zimathamanga pamchengapa paliŵiro la mtondo wadooka, ndipo mchengawo umangoti koboo! Kuthamanga kokha sizikhutira nako, motero nthaŵi zina zimangogubuduka mumchengamo, n’kumakhwekhwereza miyendo yawo yam’mbuyo ndi kumasiya mikukuluzi mumchenga. Zimathamangira ku chitsime chapafupi, n’kudumphiramo, n’kumasangalala muja amachitira ana akakondwa. Amisiri ameneŵa, ndi njovu ndipo zimalemera matani 6 imodzi!

Mmisiri wina wopanga zinthu zaluso koma zoonekako bwino ndiye njoka ya mphiri yotchedwa Péringuey adder. Ikakhala pamchenga, mamba ake amaoneka ngati timitengo tokhotakhota. Njokayi imasiya mkukuluzi umenewu ikamadzikhwekhwereza uku ikukhota mwachifatse. Kenaka mkukuluziwu suonekanso, ndipo zoti panali njoka sizidziŵikanso. Kodi njokayo imakhala italoŵera kuti? Ngati mutayang’anitsitsa, mungathe kuona maso aŵiri otong’oka ali gaa pa inu ali mumchenga. Thupi lake lonse litakwiririka mumchenga. Ikabisala chonchi, imangokhala phee kudikirira kuti ipeze chakudya chake chimene nthaŵi zambiri chimakhala buluzi amene akudutsa pafupi.

Pamchengapa pamakhalanso mkukuluzi wina mwina wosakongola kwenikweni. Uwu ndi mkukuluzi waukulu womwe umapangidwa ndi matayala a njinga zamoto zamatayala atatu zopangidwa moyenererana ndi kuchipululu kuno. Umenewu tingati ndi mkukuluzi wopezeka chifukwa cha anthu.

Mmisiri Woyendera Mmene Kwachera

Amisiri ena ochuluka zedi, amasiya madindo a mapazi awo pamchengapa. Amisiriŵa ndi monga zipembere, mikango, akadyamsonga, ndi nkhandwe, zimene mungathe kuziona kumalo otetezera nyama a ku Skeleton Coast ndiponso kumalo ena.

Koma mmsiri amene tikum’vulira chipeŵa ndi mphepo. Imachititsa malo a zaumisiriwa kuoneka bwino ndipo imaumbanso zinthu malingana ndi mmene ikufunira. Nthaŵi zonse imakhala ikusintha zoumbidwazo. Ngati mutabwerera kumalo ameneŵa patatha chaka, mungakapeze kuti miyulu ina yamchenga yasuntha mamita okwana 30 inu kulibe! Izi n’zimene mphepo ya ku Namibia ingachite.

[Mapu patsamba 17]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

AFRICA

NAMIBIA

[Chithunzi patsamba 16]

Mbewa

[Mawu a Chithunzi patsamba 16]

Des ndi Jen Bartlett