“Ufa!”
“Ufa!”
YOSIMBIDWA NDI LEANNE KARLINSKY
Ulendo wanga wofuna kulandira chithandizo chabwino kwambiri chopanda magazi ku Spain
MUTAKHALA kuti mungathe kupita kulikonse padziko lapansi, kodi mungasankhe kupita kuti? Kwa ine yankho linali losavuta. Ndine mphunzitsi wa Chisipanya, ndipo pamodzi ndi mwamuna wanga Jay, komanso mwana wanga Joel, timapita ku mpingo wa Mboni za Yehova wachisipanya ku Galax, m’boma la Virginia, ku U.S.A. Choncho, ndinali kulakalaka nditadzapita ku Spain. Choncho mungaone mmene ndinasangalalira pamene makolo anga anadzipereka kuti anditenga popita kumeneko! Ngakhale kuti mwamuna wanga ndi mwana wanga sanali kupita nawo, chikhumbo changa chinali pafupi kukhutiritsidwa pamene makolo anga ndi ine tinakwera ndege yosaima paliponse yopita ku Madrid. Titafika pa 12 April, tinaganiza zoti tiyende pagalimoto kupita ku Estella, katauni kakang’ono m’boma la Navarre, kumpoto kwa Spain. Ndinakhala momasuka pampando wakumbuyo. Mosakhalitsa ndinagona.
Kuchokera pamenepo zomwe ndikukumbukira n’zakuti ndinagona chagada pamunda, dzuŵa likundithobwa m’maso. ‘Kodi ndili kuti? Ndafika kuno bwanji? Kodi ndikulota?’ Pamene ndinali kuganiza mafunso ameneŵa, ndinayamba kuona kuti zinthu zinaipa kwabasi. Chilipo chinachitika, ndipo uku sikunali kulota ayi. Mkono wakumanzere wa malaya anga unali utang’ambika kungokhala nsanza zokhazokha, ndipo sindinathe kusuntha mikono kapena miyendo yanga. Kenako, ndinauzidwa kuti galimoto lathu linaomba zitsulo zotetezera m’mphepete mwa msewu ndipo ndinagwera pansi pamene galimoto limagubudukira kuphompho lakuya mamita 20. Ubwino wake, ine ndi makolo anga omwe sitikukumbukira chilichonse cha ngoziyo.
Ndinafuula kuti andithandize, ndipo dalaivala wina wa galimoto yaikulu anathamangira kunali ineko. Kenako anatsikira kumene kunali galimoto, komwe kunatsakamira makolo anga. “Kaitane ambulansi ibwere msanga. M’galimotomu anthu avulala kwambiri!” Anam’fuulira motero mnzake. Ndiyeno anabweranso kumene ndinagwera ndili kwalaa! Ndipo pofuna kundithandiza anayesa kuwongola mwendo wanga. Ndinakuwa ndi ululu, m’pomwe ndinadziŵa kuti ndavulala kwambiri.
Mosakhalitsa ndinali m’chipinda cha anthu ochita ngozi kuchipatala cha m’deralo ku Logroño. Mwachikondi apolisi anadziŵitsa Mboni za Yehova m’deralo za kumene ndinali ndi zimene zinachitika. Mosakhalitsa, anthu ambiri a m’mipingo ya ku Estella ndi Logroño anabwera m’chipinda chimene ndinagonekedwa, pamodzi ndi Komiti Yolankhulana ndi Chipatala ya m’deralo. Ndithudi, nthaŵi yonse imene ndinali kuvutika m’chipatala chimenechi, Akristu anzanga okondedwa amene sindimawadziŵa anali chire ndiponso ofunitsitsa kundisamalira, usana ndi
usiku. Anawasamaliranso bwino makolo anga, amene anayamba kupeza bwino mwakuti anatulutsidwa m’chipatala patangotha sabata imodzi chichitireni ngozi.Lachitatu, cha m’ma 1:00 usiku, madokotala anabwera kudzachita opaleshoni chiuno changa chimene chinathyoka. Ndinamuuza dokotalayo kuti sindikufuna kundiika magazi. * Anavomera monyinyirika pempho langalo, ngakhale kuti anandiuza kuti mosapeneka ndifa ndithu. Opaleshoni inayenda bwino, koma ndinadabwa kuti sanali kutsuka mabala anga, kapena kundisintha nsalu zomanga mabalawo.
Pofika Lachisanu magazi anga anachepa kufika pa 4.7, ndipo ndinali kufooka. Dokotala anavomera kundipatsa mankhwala ena—jakisoni wa erythropoietin (EPO) imene, pamodzi ndi iron komanso ndi mankhwala ena a magazi, zimawonjezera kupanga maselo ofira a magazi. * Apa n’kuti Jay ndi Joel atafika. Si mmene ndinasangalalira kuona mwamuna wanga ndi mwana wanga!
Cha m’ma 1:30 usiku, dokotala anamuuza Jay kuti chipatala chinali chitaloledwa kale ndi khoti kuti andiike magazi matenda anga akayamba kukula. Jay anamuuza dokotalayo kuti zofuna zanga n’zakuti sindikufuna kuikidwa magazi zivute zitani. “Ndiye afatu!” Dokotala anayankha motero.
Jay analankhula ndi Komiti Yolankhulana ndi Chipatala kuti andisamutsire ku chipatala china—chimene chingandithandize mmene ndikufunira. Sikuti onse pachipatala chimenechi samamva zonena zanga. Mwachitsanzo, dokotala wina, ananditsimikizira ine kuti ayesetsa kwambiri kundithandiza motsatira zofuna zanga zonse. Koma mosakhalitsa madokotala ena anali kundiwopseza. Anandifunsa kuti, “kodi ukufuna kufa n’kusiya banja lako?” Ndinawatsimikizira kuti ndikufuna chithandizo chabwino kwambiri chopanda magazi. Madokotala sanafune kundithandiza. “Ufa!” Dokotala wina ananena choncho mopanda chisoni.
Komiti Yolankhulana ndi Chipatala inapeza chipatala ku Barcelona chimene chinavomera kundithandiza popanda kundiika magazi. Zipatalazo zinali zosiyana bwanji! Ku Barcelona anamwino aŵiri anandisambitsa pang’onopang’ono n’kundiuza kuti ndikhale womasuka. Pondisintha nsalu zomanga mabala, mmodzi wa anamwinowo anapeza kuti zinali zothimbirira ndiponso zinali zitaumirira magazi. Anati anali wamanyazi popeza anzake a m’dzikomo anandichita zimenezi.
Mosakhalitsa ndinali kulandira chithandizo chimene ndinayenera kuyamba kulandira ku chipatala cha ku Logroño. Zotsatira zake zinali zodabwitsa. M’masiku oŵerengeka ziwalo zofunika zinali zili bwino, ndipo magazi anga anali atakwera n’kufika pa 7.3. Pamene ndimatuluka m’chipatala, anali atafika pa 10.7. Nthaŵi imene ndinakachitidwa opaleshoni ina pa chipatala china ku United States, magazi anga anali atafika pa 11.9.
Ndikuthokoza ntchito ya madokotala ndi anamwino amene amachita zimene odwala awo akufuna, ngakhale ngati iwo akugwirizana nazo kapena ayi. Pamene madokotala alemekeza zikhulupiriro za wodwala, ndiye kuti akuthandiza munthu yenseyo—ndiponso akupereka chithandizo chabwino koposa.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 8 Mboni za Yehova zimakana kuthiridwa magazi pazifukwa za m’Baibulo.—Onani Genesis 9:4; Levitiko 7:26, 27; 17:10-14; Deuteronomo 12:23-25; 15:23; Machitidwe 15:20, 28 29; 21:25.
^ ndime 9 Mkristu ayenera kusankha yekha ngati akufuna kulandira EPO kapena ayi.—Onani Nsanja ya Olonda ya October 1, 1994, tsamba 31.
[Chithunzi patsamba 26]
Ine ndi mwamuna wanga ndi mwana wanga
[Chithunzi patsamba 27]
Mamembala aŵiri a m’Komiti Yolankhulana ndi Chipatala