Kodi Zonsezi Zikutanthauzanji?
Kodi Zonsezi Zikutanthauzanji?
MUTATI muone miyezo yamakhalidwe m’zaka zaposachedwapa, mudzaona kuti pali kusintha kwakukulu. Mosakayikira, anthu ambiri akuponderezabe miyezo ya makhalidwe abwino. Kodi zimenezi zikutanthauzanji kwenikweni?
Monga momwe ena amanenera, kodi zikutanthauza kuti kutukuka kwathu konse ndiponso anthu onse ndi oipa ofunika kuwonongedwa? Kapena kodi kusintha kumeneku ndi mbali chabe yozoloŵereka ya kusinthasintha kwa zochitika m’mbiri?
Mfundo yomalizayi ndiyo mmene anthu ambiri amaganizira. Amaona kuloŵa pansi kwa makhalidwe abwino m’nthaŵi yathu ino monga chochitika chimodzi mwa zimene zakhala zikuchitika kenako n’kutha m’mbiri yonse. Iwo amayembekezera kuti zochitika zimenezi zidzabwerera m’chimake ndikuti miyezo yapamwamba yamakhalidwe abwino idzabwereranso. Kodi akunena zoona?
“Masiku Otsiriza”
Tiyeni tipende mfundo mogwirizana ndi Mawu a Mulungu, Baibulo—buku limene kwa zaka mazana ambiri lakhala likupereka malamulo amakhalidwe abwino. N’kwanzeru kwambiri kuyerekeza dziko lalerolino ndi zimene mawu aulosi amene Baibulo limanena okhudza nyengo yotsiriza yeniyeni m’mbiri ya anthu. Ino ndiyo nyengo imene Baibulo limatcha “masiku otsiriza” kapena “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano.” (2 Timoteo 3:1; Mateyu 24:3) Monga momwe mawu ameneŵa akusonyezera, nyengo imeneyi imasonyeza mapeto enieni a nyengo ina ndi chiyambi cha nyengo yatsopano.
Mawu a Mulungu ananeneratu kuti masiku otsiriza adzakhala “nthaŵi zoŵaŵitsa.” Kuti lithandize anthu atcheru kuzindikira masiku otsiriza, Baibulo linatchula zinthu zingapo zimene zonse pamodzi zimapereka malongosoledwe omveka, kapena zizindikiro za nyengo yapadera imeneyi.
Anthu a Makhalidwe Oipa
Onani mbali ya chizindikiro chimenechi chimene chatenga malo lerolino: “Pakuti anthu adzakhala . . . nawo maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana.” (2 Timoteo 3:2, 5) Palibe nyengo ina m’mbiri imene yakhala ndi mphamvu yotereyi ndiponso anthu achikunja ochuluka ngati inoyi. Anthu ambiri amakana zoti Mulungu ndiye ali ndi ulamuliro wonse, ndipo anthu ambiri saona Baibulo monga magwero okha a choonadi. Zoona, zipembedzo zilipodi, koma zambiri zilibe mphamvu kwenikweni. Zangokhala ndi maonekedwe onyenga chabe.
Baibulo limatchulanso mbali ina ya chizindikiro chimenechi kuti: “Anthu adzakhala . . . osakhoza kudziletsa, aukali,” ndipo “chifukwa cha kuchuluka kwa kusayeruzika, chikondano cha anthu aunyinji chidzazirala.” (2 Timoteo 3:2, 3; Mateyu 24:12) Liwu lachigiriki lotanthauza ‘ukali’ mwa matanthauzo ake ena ndi “kupanda chisoni ndiponso kusakhudzidwa mtima kwaumunthu.” Masiku ano, nthaŵi zonse ana aang’ono akusonyeza kukhala “aukali” ndipo akuchita zipolowe zaupandu zambiri.
Komanso, kuwonjezereka kwa tekinoloje ndiponso kutukuka m’zachuma ndiponso dyera limene zimenezi zabweretsa, lapangitsa anthu ambiri kusiya makhalidwe akale. Popanda kulingalira ena, iwo amagwiritsa ntchito njira iliyonse imene angathe, ngakhale yachinyengo, kuti akwaniritsa zolinga zawo zadyera. Kuwonjezereka kwa juga ndi umboni wina wadyera, ndi ziŵerengero zaupandu m’zaka mazana angapo
apitawa uli umboni wamphamvu ndi woonekeratu wa zimenezi.Mbali imene makamaka ili yofala m’nthaŵi yathu ino ndi iyi: “Anthu adzakhala . . . okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.” (2 Timoteo 3:2, 4) Chitsanzo chimodzi cha zimenezi n’chakuti anthu amafuna zosangalatsa thupi, koma safuna lamulo lokhala ndi mkazi kapena mwamuna mmodzi kwa moyo wawo wonse. Zotsatira zake n’zakuti pakhala zochitika zambiri zedi zowononga mabanja, ana omvetsa chisoni ndiponso osoŵa chikondi cha makolo awo, mabanja a kholo limodzi, ndiponso matenda opatsirana mwa kugonana.
Mbali ina ya chizindikiro chimenechi ndiyakuti “anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama” (2 Timoteo 3:2) Malinga ndi zomwe inanena magazini ya ku Germany yotchedwa Die Zeit kuti, “chimene chikusonkhezera [kukwera kwa chuma masiku ano] ndi kudzikonda.” Kuposa kale lonse, kukonda ndalama ndi chinthu chofunika kwambiri m’miyoyo ya anthu ambiri. N’kudzikonda kwawoko, makhalidwe ena amanyalanyazidwa.
Zochitika za Dziko
Kuphatikiza pa kuloŵa pansi kwa makhalidwe a anthu, Baibulo linaneneratu kuti masiku otsiriza adzakhala ndi zochitika zachilendo zimene zidzakhudza anthu onse. Mwachitsanzo, limanena kuti “mtundu wa anthu udzaukira pa mtundu wina, ndipo ufumu pa ufumu wina: ndipo kudzakhala zivomezi zazikulu, ndi njala.”—Luka 21:10, 11.
Kuchotsapo zaka za m’ma 1900, palibe nyengo ina m’mbiri imene anthu ambiri aona masoka aakulu m’nthaŵi yochepa ngati imeneyi. Mwachitsanzo, anthu oposa 100 miliyoni anaphedwa mu nkhondo m’nthaŵi imeneyo, chiŵerengero chimenechi n’chachikulu zedi poyerekeza ndi chiŵerengero chonse cha anthu ophedwa pankhondo zaka mazana angapo apitawo. Zaka za ma 1900 zinali ndi nkhondo
ziŵiri zapadera zimene anazitcha kuti nkhondo za dziko lonse. Nkhondo zapadziko lonse zangati zimenezo zinali zisanachitikepo.Kusonkhezeredwa ndi Mphamvu Yoipa
Baibulo limavumbulanso kukhalapo kwa cholengedwa chauzimu choipa n’champhamvu, “iye wotchedwa mdyerekezi ndi Satana,” amene cholinga chake ndi kunyengerera anthu kuti asiye makhalidwe abwino n’kuwaloŵetsa m’makhalidwe oipa. Limanena kuti mu masiku otsiriza, iye watsikira ku dziko lapansi, “wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kam’tsalira kanthaŵi.”—Chivumbulutso 12:9, 12.
Baibulo limatcha Mdyerekezi kukhala “mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera.” (Aefeso 2:2) Izi zikutanthauza kuti Mdyerekezi ali ndi chisonkhezero champhamvu pa anthu ambiri, moti nthaŵi zambiri anthu sazindikira zimenezi, monga mmene nthaŵi zina sitizindikira zinthu zoipa zopezeka mu mpweya.
Mwachitsanzo, chisonkhezero cha Satana chimaoneka m’njira zambiri zamakono zimene timagwiritsa ntchito polankhulana: mavidiyo, mafilimu apakanema, wailesi yakanema, intaneti, otsatsa malonda, mabuku, magazini, ndi manyuzipepala. Nkhani zambiri, makamaka za achinyamata osazindikira, zimakhala ndi uthenga woipitsitsa, monga kusankhana mafuko, zolaula, chisembwere, ndi chipolowe chosaneneka.
Anthu ambiri oona mtima achita chidwi ndi kufanana kwa malongosoledwe a Baibulo a masiku otsiriza ndi mmene zinthu zilili m’dziko m’masiku athu ano. N’zoonadi kuti, kunachitika zinthu zina kalekale zisanafike zaka za ma 1900 zimene pang’ono zinkaoneka ngati zikufanana ndi zimene Baibulo limalongosola. Koma ndi m’zaka za m’ma 1900 zokha, ndiponso pakalipano m’zaka za ma 2000 zokha, pamene mbali zonse za chizindikiro zingaoneke.
Nyengo Yatsopano Ikudzayo
Palibe akulondola pakati pa amene amakhulupirira kuti anthu adzawonongedwa ndi amene amanena kuti zinthu zidzapitirira kukhala mmene zililimu. M’malo mwake, Baibulo mosapita m’mbali limasonyeza kuti ulamuliro wadziko umene ulipowu udzaloŵedwa m’malo ndi chinthu china chatsopano kwambiri.
Yesu atatchula mbali zingapo za chizindikiro cha masiku otsiriza, anati: “Inde chotero inunso, pakuona zinthu izi zilikuchitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi.” (Luka 21:31) Ufumu wakumwamba wa Mulungu ndiwo unali mutu wankhani wa ulaliki wa Yesu. (Mateyu 6:9, 10) Ndipo Mulungu anam’sankha iye kukhala Mfumu ya Ufumu umenewu, lomwe ndi boma limene lidzalamulira posachedwapa padziko lonse lapansi.—Luka 8:1; Chivumbulutso 11:15; 20:1-6.
Kumapeto a masiku otsiriza, Ufumu wakumwamba wa Mulungu umene uli m’manja mwa Kristu udzachotsa adani ake onse—Mdyerekezi ndi amene amam’chirikiza, ndipo udzabweretsa dziko lapansi latsopano lolungama kuloŵa m’malo mwa dziko lalero la makhalidwe oipali. (Danieli 2:44) Mu dziko latsopano limeneli, anthu amitima yabwino adzasangalala ndi moyo wosatha padziko losandutsidwa paradaiso.—Luka 23:43; 2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4.
Amene amadana ndi kuloŵa pansi kwa makhalidwe abwino lerolino ndiponso amene akuzindikira kuti chizindikiro chachiungwe cha masiku otsiriza chikukwaniritsidwa mu zochitika za masiku ano angayembekezere m’tsogolo mwabwino zedi. Pachifukwa chimenechi tikuthokoza Mulungu Wamphamvuyonse, amene amasamala za ife ndiponso amene ali ndi cholinga chaulemerero kaamba ka chilengedwe chake, dziko lapansi.—Salmo 37:10, 11, 29; 1 Petro 5:6, 7.
Mboni za Yehova zikukupemphani kuti muphunzire zambiri za Mlengi wathu wachikondi ndiponso chiyembekezo cha moyo m’dziko la makhalidwe abwino, limene wasungira anthu onse amene amaphunzira zimenezi. Monga momwe Baibulo limanenera kuti, “koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.”—Yohane 17:3.
[Chithunzi patsamba 10]
Anthu amitima yabwino adzasangalala ndi moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso