Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 8

Abulahamu ndi Sara Anamvera Mulungu

Abulahamu ndi Sara Anamvera Mulungu

Pafupi ndi mzinda wa Babele panali mzinda wina wotchedwa Uri. Anthu a mumzinda umenewu ankalambira milungu ina yambiri koma sankalambira Yehova. Koma mumzindawu munali munthu wina amene ankalambira Yehova yekha. Dzina lake anali Abulahamu.

Tsiku lina Yehova anauza Abulahamu kuti: ‘Samuka mʼdziko lako ndi kuchoka pakati pa abale ako ndipo upite kudziko limene ndidzakuonetse.’ Kenako Mulungu anamulonjeza kuti: ‘Ndidzapangitsa kuti ukhale mtundu waukulu, ndipo anthu ambiri padziko lonse lapansi ndidzawachitira zinthu zabwino chifukwa cha iwe.’

Abulahamu sankadziwa kumene Yehova ankafuna kuti apite, koma ankakhulupirira kwambiri Yehovayo. Choncho iye ndi mkazi wake, Sara analongedza katundu n’kuyamba ulendo wautali. Pa ulendowu ananyamukanso ndi bambo ake, dzina lawo a Tera komanso Loti yemwe anali mwana wa mng’ono wake.

Pa nthawiyi n’kuti Abulahamu ali ndi zaka 75. Ndipo iye ndi banja lake atayenda kwa nthawi yaitali, anafika m’dziko limene Yehova anawauza. Dziko lake linali la Kanani. Ali kumeneko, Mulungu analankhula ndi Abulahamu n’kumulonjeza kuti: ‘Dziko lonseli ndidzalipereka kwa ana ako.’ Komatu pa nthawiyi Abulahamu ndi Sara n’kuti ali okalamba ndipo analibe ana. Ndiye kodi Yehova akanakwaniritsa bwanji lonjezo lakeli?

“Chifukwa cha chikhulupiriro, Abulahamu . . . anamvera nʼkupita kumalo amene ankayembekezera kuwalandira ngati cholowa. Iye anapitadi, ngakhale kuti sankadziwa kumene akupita.”​—Aheberi 11:8