Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 101

Paulo Anatumizidwa ku Roma

Paulo Anatumizidwa ku Roma

Ulendo wachitatu wa Paulo unakathera ku Yerusalemu. Atafika kumeneko anamangidwa. Ndiyeno usiku anaona masomphenya. Yesu anamuuza kuti: ‘Udzapita ku Roma ndipo ukalalikira kumeneko.’ Paulo anatengedwa ku Yerusalemu kupita ku Kaisareya komwe anakakhala m’ndende zaka ziwiri. Pa nthawi imene mlandu wake unkazengedwa ndi bwanamkubwa wina dzina lake Fesito, Paulo ananena kuti: ‘Ndikupempha kuti mlandu wangawu ukaweruzidwe kwa Kaisara.’ Ndiyeno Fesito anati: “Popeza wachita apilo kuti ukaonekere kwa Kaisara, udzapitadi kwa Kaisara.” Popita ku Romako Paulo anatengedwa pa sitima yapamadzi ndipo abale awiri, Luka ndi Arisitako anapita nawo.

Ali panyanja kunachitika chimphepo choopsa kwa masiku ambiri. Aliyense ankaganiza kuti palibe amene apulumuke. Koma Paulo ananena kuti: ‘Anthu inu, mngelo wandiuza m’maloto kuti: “Usaope Paulo. Ukafika ku Roma ndipo aliyense musitimayi saafa.” Choncho musachite mantha. Palibe amene afe.’

Chimphepocho chinawomba kwa masiku 14. Kenako anayamba kuona chilumba cha Melita. Koma sitimayo inatitimira mumchenga ndipo inayamba kusweka chifukwa cha mafunde. Ngakhale zinali choncho, anthu onse 276 amene anali mmenemo anakafika kumtunda. Ena anasambira pomwe ena anagwiritsa ntchito zidutswa za sitimayo zomwe zinkayandama. Atafika, anthu apachilumbapo anawalandira bwino n’kuwayatsira moto kuti awothe.

Patapita miyezi itatu, asilikali anatenga Paulo pa sitima ina n’kupita naye ku Roma. Atafika, abale anabwera kudzamuona. Paulo atawaona anathokoza Yehova ndipo analimba mtima. Ngakhale kuti anali mkaidi, ankaloledwa kukhala m’nyumba ina ya lendi ndipo ankalonderedwa ndi msilikali. Iye anakhala kumeneko zaka ziwiri. Anthu akabwera kudzamuona, ankawalalikira za Ufumu wa Mulungu ndiponso za Yesu. Komanso iye analemba makalata opita kumipingo ya ku Asia Minor ndi ku Yudeya. Apatu Yehova anagwiritsa ntchito Paulo kuti uthenga wabwino ufike kwa anthu a mitundu ina.

“Tikusonyeza mʼnjira iliyonse kuti ndife atumiki a Mulungu. Tikuchita zimenezi popirira zinthu zambiri, pokumana ndi mavuto, pokhala opanda zinthu zofunika, pokumana ndi zinthu zovuta.”​—2 Akorinto 6:4