MUTU 71
Yehova Anateteza Yesu
M’dziko lina lakum’mawa kwa Isiraeli, kunali anthu amene ankakhulupirira kuti nyenyezi zingawathandize kudziwa zinthu. Tsiku lina, anthu ena ochokera kudzikoli anaona chinthu chokhala ngati nyenyezi chikuyenda m’mwamba ndipo anayamba kuchitsatira. Iwo anatsatira “nyenyezi” imeneyo mpaka kukafika ku Yerusalemu. Atafika anayamba kufunsa anthu kuti: ‘Kodi mwana amene adzakhale mfumu ya Ayuda ali kuti? Tabwera kuti tidzamugwadire.’
Herode atamva zimenezi anada nkhawa kwambiri. Iye anafunsa ansembe aakulu kuti: ‘Paja mfumu imeneyi ikuyenera kubadwira kuti?’ Ansembewo anamuyankha kuti: ‘Aneneri ananena kuti adzabadwira ku Betelehemu.’ Ndiyeno Herode anauza anthu ochokera kum’mawawo kuti: ‘Pitani ku Betelehemu mukafufuze mwanayo. Mukakamupeza mubwere mudzandiuze. Nanenso ndikufuna ndikamugwadire.’ Koma sikuti Herode ankafunadi kuti akamugwadire mwanayo.
“Nyenyezi” ija inayambanso kuyenda ndipo anthu aja anapitiriza kuitsatira. Ndiyeno inakaima panyumba inayake. Atalowa m’nyumbayo anapeza Yesu ndi amayi ake. Iwo anagwada n’kuweramira mwanayo ndipo anapereka mphatso za golide, lubani ndi mule. Kodi ndi zoona kuti Yehova ndi amene anatuma anthuwa kuti akaone Yesu? Ayi.
Usiku womwewo, Yehova analankhula ndi Yosefe m’maloto. Anamuuza kuti: ‘Herode akufuna kupha Yesu. Tenga mkazi wako ndi mwanayo ndipo muthawire ku Iguputo. Mukakhale komweko mpaka nthawi imene ndidzakuuzeni kuti mubwerere.’ Nthawi yomweyo, Yosefe ananyamuka ndi banja lake kupita ku Iguputo.
Ndiyeno Yehova anauza anthu ochokera kum’mawa aja kuti asadzere kwa Herode. Herodeyo atazindikira zoti anthuwo adutsa njira ina, anakwiya kwambiri. Popeza zinali zovuta kuti apeze Yesu, analamula kuti ana aamuna amsinkhu wa Yesu ku Betelehemu aphedwe. Pamene izi zinkachitika, n’kuti Yesu ali ku Iguputo ndipo anali wotetezeka.
Patapita nthawi, Herode anamwalira. Ndiyeno Yehova anauza Yosefe kuti: ‘Tsopano ukhoza kubwerera.’ Yosefe, Mariya ndi Yesu anabwerera ku Isiraeli ndipo anakafikira ku Nazareti.
“Ndi mmenenso adzakhalire mawu otuluka pakamwa panga . . . . zimene ndinawatumizira kuti achite zidzachitikadi.”—Yesaya 55:11