Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 122

Pemphero Lomaliza la Yesu Ali M’chipinda Chapamwamba

Pemphero Lomaliza la Yesu Ali M’chipinda Chapamwamba

YOHANE 17:1-26

  • MADALITSO AMENE ANTHU ADZAPEZE CHIFUKWA CHODZIWA MULUNGU KOMANSO MWANA WAKE

  • ZIMENE MALEMBA AMATANTHAUZA PONENA KUTI YEHOVA, YESU NDI OPHUNZIRA NDI AMODZI

Yesu atatsala pang’ono kupita kumwamba, anakonzekeretsa maganizo a ophunzira ake. Iye anachita zimenezi chifukwa chakuti ankawakonda kwambiri. Atamaliza kuwapatsa malangizo anayang’ana kumwamba n’kuyamba kupemphera kwa Atate wake kuti: “Lemekezani mwana wanu, kuti mwana wanu akulemekezeni. Inu mwamupatsa ulamuliro pa anthu onse, kuti onse amene inu mwamupatsa, awapatse moyo wosatha.”—Yohane 17:1, 2.

Zimene Yesu ananenazi zinasonyeza kuti ankaona kuti kulemekeza Yehova ndi nkhani yofunika kwambiri. Koma ndi zolimbikitsa kwambiri kuti ananenanso za chiyembekezo cha moyo wosatha. Poti Yesu ali ndi “ulamuliro pa anthu onse,” anthuwo akhoza kudzalandira madalitso chifukwa cha nsembe yake. Koma ndi anthu ochepa okha amene adzalandire madalitsowo. N’chifukwa chiyani zili choncho?Chifukwa chakuti Yesu adzapereka madalitso kwa anthu okhawo amene amachita zimene iye ananena. Iye anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.”—Yohane 17:3.

Kuti munthu adzapeze moyo wosatha ayenera kudziwa komanso kukhala pa ubwenzi ndi Atate komanso Mwana wake. Ayenera kumaona zinthu mmene Atate komanso Mwana amazionera. Ayeneranso kuyesetsa kusonyeza makhalidwe abwino amene Atate ndiponso Mwanayo ali nawo pochita zinthu ndi anthu ena. Ndipo ayenera kukumbukira kuti kulemekeza Mulungu ndi kofunika kwambiri poyerekeza ndi kupulumuka. Kenako Yesu anapitiriza kufotokoza mfundo yonena za kulemekeza Mulungu. Iye ananena kuti:

“Ndakulemekezani padziko lapansi, popeza ndatsiriza kugwira ntchito imene munandipatsa. Ndipo tsopano Atate, ndiloleni kuti ndikhale pambali panu, ndipo mundipatse ulemerero umene ndinali nawo pambali panu dziko lisanakhalepo.” (Yohane 17:4, 5) Pamenepatu Yesu ankapempha Atate wake kuti akadzamuukitsa adzamupatsenso ulemelero umene anali nawo kumwamba.

Komabe ponena mawu amenewa, sikuti Yesu sankakumbukira zimene anachita pa nthawi ya utumiki wake. Tikutero chifukwa iye anapemphera kuti: “Anthu amene munawatenga m’dziko ndi kundipatsa ine ndawadziwitsa dzina lanu. Anali anu, koma munawapereka kwa ine, ndipo iwo asunga mawu anu.” (Yohane 17:6) Yesu ankatchula dzina la Mulungu, lomwe ndi Yehova, polalikira. Kuwonjezera pamenepo anathandizanso atumwi ake kudziwa makhalidwe a Mulungu ndiponso mmene amachitira zinthu ndi anthu.

Atumwiwo anafika pomudziwa bwino Yehova, anadziwa udindo wa Mwana wake komanso anadziwa zimene Yesu anawaphunzitsa. Yesu ananena modzichepetsa kuti: “Mawu amene munandipatsa ndawapereka kwa iwo. Iwo awalandira ndipo adziwa ndithu kuti ine ndinabwera monga nthumwi yanu, ndipo akhulupirira kuti ndinu amene munandituma.”—Yohane 17:8.

Kenako zimene Yesu ananena zinasonyeza kuti pali kusiyana pakati otsatira ake ndi anthu ena onse. Iye anati: “Choncho ndikupempha m’malo mwa iwo, sindikupemphera dziko, koma awo amene mwandipatsa, chifukwa iwo ndi anu. . . . Atate Woyera, ayang’anireni chifukwa cha dzina lanu limene mwandipatsa, kuti akhale amodzi mmene ife tilili. . . . Ine ndawasunga moti palibe aliyense wa iwo amene wawonongeka kupatulapo mwana wa chiwonongeko,” yemwe ndi Yudasi Isikariyoti. Pa nthawiyi Yudasi anali akukonza chiwembu kuti apereke Yesu.—Yohane 17:9-12.

Yesu anapitiriza kupemphera kuti: “Dziko likudana nawo. . . . Sindikupempha kuti muwachotse m’dziko, koma kuti muwayang’anire kuopera woipayo. Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.” (Yohane 17:14-16) Atumwi komanso ophunzira ena anali akadali m’dziko lomwe wolamulira wake ndi Satana koma ankayenera kukhala osiyana ndi anthu a m’dzikoli komanso kupewa makhalidwe oipa. Kodi akanachita bwanji zimenezi?

Iwo ankayenera kukhala oyera kapena kuti opatulika kuti azitumikira Mulungu. Iwo akanachita zimenezi potsatira choonadi chopezeka m’Malemba Achiheberi komanso choonadi chimene Yesu anawaphunzitsa. Yesu anapempheranso kuti: “Ayeretseni ndi choonadi. Mawu anu ndiwo choonadi.” (Yohane 17:17) Patapita nthawi, Mulungu anagwiritsa ntchito atumwi ena kulemba mabuku omwe anakhala mbali ya “choonadi” chomwe chimathandiza kuti munthu akhale woyera komanso wopatulika pamaso pa Mulungu.

Koma patapita nthawi panapezeka anthu enanso omwe anavomereza “choonadi.” N’chifukwa chake Yesu sanangopempherera “awa okha, [kutanthauza anthu omwe anali nawo pa nthawiyo] komanso amene amakhulupirira [Yesu] kudzera m’mawu awo.” Kodi Yesu anawapempherera chiyani anthu onsewa? Iye anapempha Atate ake kuti: “Onsewa akhale amodzi, mmene inu Atate ndi ine tilili ogwirizana, kuti iwonso akhale ogwirizana ndi ife.” (Yohane 17:20, 21) Zimenezi sizikutanthauza kuti Yesu ndi Atate wake ndi munthu mmodzi. Koma ndi amodzi chifukwa chakuti amachita zinthu zonse mogwirizana. Choncho Yesu ankapemphera kuti otsatira ake akhale ogwirizana ngati mmene iyeyo ndi Atate wake alili.

Yesu anali atangouza kumene Petulo komanso atumwi enawo kuti akupita kukawakonzera malo. Yesu ankatanthauza kuti akawakonzera malo kumwamba. (Yohane 14:2, 3) Kenako Yesu ananenanso mfundo imeneyi m’pemphero. Iye anati: “Atate, ine ndikufuna kuti amene mwandipatsawa adzakhale limodzi ndi ine kumene ine ndidzakhale, kuti adzaone ulemerero wanga umene inu mwandipatsa, chifukwa munandikonda musanayale maziko a dziko.” (Yohane 17:24) Ponena mawu amenewa, Yesu ankatanthauza kuti zaka zambiri m’mbuyomo Adamu ndi Hava asanabereke ana, Mulungu ankakonda kwambiri Mwana wake wobadwa yekha amene kenako anadzakhala Yesu Khristu.

Pomaliza pempheroli, Yesu ananenanso za dzina la Atate wake komanso za chikondi chimene Mulungu anali nacho pa atumwi komanso anthu ena amene adzalandire “choonadi.” Iye anati: “Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzinalo kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo, inenso ndikhale wogwirizana ndi iwo.”—Yohane 17:26.