Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 78

Woyang’anira Nyumba Wokhulupirika Ayenera Kukhala Wokonzeka

Woyang’anira Nyumba Wokhulupirika Ayenera Kukhala Wokonzeka

LUKA 12:35-59

  • WOYANG’ANIRA NYUMBA WOKHULUPIRIKA AYENERA KUKHALA WOKONZEKA

  • YESU ANABWERA KUTI ADZAGAWANITSE ANTHU

Yesu anafotokoza kuti a “kagulu ka nkhosa” okha ndi amene ali ndi malo mu Ufumu wakumwamba. (Luka 12:32) Koma munthu amene wapatsidwa mwayi umenewu sayenera kuuona mopepuka. Ndipotu Yesu anafotokoza kufunika koti munthu amene wasankhidwa kuti akalamulire nawo mu Ufumu aziona zinthu moyenera.

Chifukwa cha mfundo imeneyi, Yesu analimbikitsa ophunzira ake kuti azikonzekera za kubwera kwake. Iye ananena kuti: “Mangani m’chiuno mwanu ndipo nyale zanu zikhale chiyakire. Inuyo mukhale ngati anthu amene akuyembekezera kubwera kwa mbuye wawo kuchokera ku ukwati, kuti akafika ndi kugogoda amutsegulire mwamsanga. Odala ndi akapolo amene mbuye wawo pofika adzawapeza akudikira!”—Luka 12:35-37.

Yesu atafotokoza fanizoli, ophunzira ake anazindikira kuti ayenera kuona zinthu moyenera. Atumiki amene anatchulidwa m’fanizoli anali okonzeka ndipo ankadikira kuti mbuye wawo abwera nthawi iliyonse. Yesu ananena kuti: “Iwo ndi odala ndithu ngati [mbuyeyo] atawapeza akudikirabe ngakhale atafika pa ulonda wachiwiri [womwe unkayamba 9 koloko usiku mpaka 12 koloko] kapenanso wachitatu [womwe unkayamba 12 koloko usiku mpaka 3 koloko m’bandakucha]!”—Luka 12:38.

Pamenepatu sikuti nkhani inali yongolimbikitsa anthu ogwira ntchito panyumba kapena ogwira ntchito iliyonse kuti azilimbikira ntchito. Mfundo ya Yesu, yemwe anali Mwana wa munthu, inaonekera bwino atafotokoza kugwirizana komwe kunalipo pakati pa iyeyo ndi fanizoli. Iye anauza ophunzira akewo kuti: “Inunso khalani okonzeka, chifukwa pa ola limene simukuliganizira, Mwana wa munthu adzafika.” (Luka 12:40) Zimenezi zinasonyeza kuti pa nthawi ina Yesu adzabwera ndipo pa nthawiyo adzafuna kuti otsatira ake, makamaka a “kagulu ka nkhosa” adzakhale okonzeka.

Petulo ankafuna kumvetsa zimene Yesu ankatanthauza, choncho anamufunsa kuti: “Ambuye, kodi mukunena fanizoli kwa ife tokha kapenanso kwa ena onse?” M’malo mongomuyankha Petulo kuti eya kapena ayi, Yesu ananenanso fanizo lina lofananako ndi loyamba lija. Iye anati: “Ndani kwenikweni amene ali mtumiki woyang’anira nyumba wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake adzamuika kuyang’anira gulu la atumiki ake, kuti aziwapatsa chakudya chokwanira pa nthawi yake? Kapolo ameneyo ndi wodala, ngati mbuye wake pobwera adzam’peze akuchita zimenezo! Ndithu ndikukuuzani, Adzamuika kukhala woyang’anira zinthu zake zonse.”—Luka 12:41-44.

Mu fanizo loyamba lija, “mbuye” akuimira Yesu, yemwe ndi Mwana wa munthu. Choncho “mtumiki woyang’anira nyumba wokhulupirika” ayenera kuti ndi amuna amene ali mu “kagulu ka nkhosa” amene adzapatsidwa Ufumu. (Luka 12:32) Pamenepatu Yesu ankatanthauza kuti ena mwa amuna a mu ‘kagulu ka nkhosaka’ azidzayang’anira “gulu la atumiki ake, kuti aziwapatsa chakudya chokwanira pa nthawi yake.” Choncho Petulo komanso ophunzira ena amene Yesu ankawaphunzitsa ndiponso kuwapatsa chakudya chauzimu, anazindikira kuti pa nthawi inayake Mwana wa munthu adzabwera. Ndipo pa nthawi imeneyo padzakhala njira yomwe izidzathandiza kuti otsatira a Yesu, omwe ndi “gulu la atumiki” la Ambuye, azidzalandira chakudya chauzimu.

Yesu anafotokozanso chifukwa china chimene ophunzira ake ayenera kukhalira okonzeka komanso kusamala mmene amaonera zinthu. Iye ananena zimenezi chifukwa n’zotheka munthu kuyamba kunyalanyaza malangizo a Yehova n’kufika poyamba kutsutsana ndi abale komanso alongo. Yesu ananena kuti: “Koma ngati kapoloyo anganene mumtima mwake kuti, ‘Mbuye wanga akuchedwa kubwera.’ Ndiyeno n’kuyamba kumenya antchito anzake aamuna ndi aakazi, kudya, kumwa ndi kuledzera, mbuye wa kapoloyo adzabwera pa tsiku limene iye sakuyembekezera, ndi pa ola limene sakulidziwa, ndipo adzam’patsa chilango choopsa ndi kum’patsa gawo pamodzi ndi anthu osakhulupirika.”—Luka 12:45, 46.

Yesu ananenanso kuti anabwera “kudzakoleza moto padziko lapansi.” Ndipotu zimenezi n’zoonadi, chifukwa Yesu ankayambitsa nkhani zomwe zinkachititsa kuti anthu azitsutsana koma nkhanizi zinkathandiza kuti anthu azindikire ziphunzitso komanso miyambo yabodza n’kusiya kuitsatira. Zinkachititsanso kuti anthu omwe ankayenera kukhala ogwirizana asamagwirizane. Anthu ankagawanika, “bambo kutsutsana ndi mwana wake wamwamuna, ndipo mwana wamwamuna kutsutsana ndi bambo ake. Mayi kutsutsana ndi mwana wake wamkazi, ndipo mwana wamkazi kutsutsana ndi mayi ake. Mpongozi kutsutsana ndi mkazi wa mwana wake, ndipo mkazi wokwatiwa kutsutsana ndi apongozi ake aakazi.”—Luka 12:49, 53.

Mfundo zonsezi zinkapita kwa ophunzira ake. Kenako Yesu anatembenukira ku gulu la anthu lija. Anthu ambiri ankakaniratu kuvomereza kuti Yesu anali Mesiya ngakhale kuti panali umboni wokwanira. Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Mukaona mtambo ukukwera chakumadzulo, nthawi yomweyo mumanena kuti, ‘Kukubwera chimvula,’ ndipo chimabweradi. Ndipo mukaona mphepo ya kum’mwera ikuwomba, mumanena kuti, ‘Lero kutentha kwambiri,’ ndipo zimachitikadi. Onyenga inu! Mumatha kuzindikira maonekedwe a dziko lapansi ndi kuthambo. Nanga zimakukanikani bwanji kuzindikira tanthauzo la zimene zikuchitika pa nthawi ino?” (Luka 12:54-56) Pamenepatu anthuwo anasonyezeratu kuti sanali okonzeka.