MUTU 4
‘Yehova Ali Ndi Mphamvu Zambiri’
1, 2. (a) Kodi ndi zinthu zodabwitsa ziti zimene Eliya anali ataonapo kale? (b) Ndi zinthu zodabwitsa kwambiri ziti zimene anaona ali kuphanga m’phiri la Horebe?
ELIYA anali ataonapo kale zinthu zodabwitsa. Anali ataona akhwangwala akumubweretsera chakudya kawiri pa tsiku pa nthawi imene ankabisala. Pa nthawi ya njala yomwe inachitika kwa nthawi yaitali, iye anaona kuti ufa komanso mafuta zomwe zinali m’mitsuko iwiri sizinathe. Analinso ataona moto ukugwa kuchokera kumwamba poyankha pemphero lake. (1 Mafumu, chaputala 17 ndi 18) Koma Eliya anali asanaonepo zinthu zodabwitsa ngati zimene anali atatsala pang’ono kuona pa nthawiyi.
2 Ataima mwamantha pafupi ndi khomo la phanga paphiri la Horebe, anaona zinthu zingapo zodabwitsa kwambiri. Choyamba kunawomba mphepo. Iyenera kuti inali yamphamvu kwambiri chifukwa panali chiphokoso chogonthetsa m’khutu, moti inang’amba mapiri ndi kuphwanya matanthwe. Kenako panachitika chivomerezi champhamvu kwambiri. Ndiyeno panabwera moto. Pamene motowu unkayandikira pamene Eliya anaima, ayenera kuti anamva kutentha kwake koopsa.—1 Mafumu 19:8-12.
3. Kodi Eliya anaona umboni wakuti Mulungu ali ndi khalidwe liti, nanga ifeyo tingapeze kuti umboni woti Mulungu ali ndi khalidweli?
3 Zinthu zonse zimene Eliya anaonazi zinkafanana pa chinthu chimodzi. Zonsezi zinkasonyeza kuti Yehova Mulungu ali ndi mphamvu zambiri. Koma sikuti timafunika kuchita kuona zinthu zodabwitsa kuti tidziwe kuti Mulungu ndi wamphamvu. Timatha kuona mphamvu zake mosavuta. Baibulo limatiuza kuti chilengedwe chimapereka umboni wa ‘mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu wake.’ (Aroma 1:20) Taganizirani za kuwala koopsa kwa mphezi, kugunda kwamphamvu kwa mabingu, mathithi osangalatsa komanso kuchuluka kwa nyenyezi kumwamba. Kodi simuona umboni wakuti Mulungu ali ndi mphamvu zambiri? Komatu ndi anthu ochepa masiku ano amene amazindikira mphamvu za Mulungu ndipo ndi ochepa kwambiri amene amaona mphamvuzo moyenera. Komabe kumvetsa mfundo yoti Yehova ndi wamphamvu kumatithandiza kuti tikhale ndi zifukwa zambiri zoti tizifuna kuti akhale mnzathu. M’chigawochi tiphunzira mwatsatanetsatane mphamvu zopanda malire za Yehova.
“Yehova anadutsa”
Mphamvu Zimachokera kwa Yehova
4, 5. (a) Kodi Baibulo limafotokoza zotani zokhudza dzina la Yehova? (b) N’chifukwa chiyani n’zoyenera kuti Yehova anasankha ng’ombe kuti iziimira mphamvu zake?
4 Palibe amene ali ndi mphamvu zambiri kuposa Yehova. Lemba la Yeremiya 10:6 limati: “Palibe aliyense amene angafanane ndi inu Yehova. Inu ndinu wamkulu ndipo dzina lanu ndi lalikulu komanso lamphamvu.” Monga taonera, lembali likunena kuti dzina la Yehova ndi lalikulu komanso lamphamvu. Paja dzinali limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhala.” Kodi n’chiyani chimachititsa kuti Yehova azitha kupanga chilichonse chimene akufuna ndiponso kukhala chilichonse chimene wasankha? Chifukwa chimodzi n’choti ali ndi mphamvu. Yehova angathe kuchita chilichonse ndipo palibe chimene chingamulepheretse kuchita zimene akufuna. Mphamvu zoterezi ndi limodzi mwa makhalidwe ake ofunika kwambiri.
5 Popeza sitingamvetse zonse zokhudza mphamvu za Yehova, iye amagwiritsa ntchito mafanizo potithandiza kuti timvetse. Monga taonera, amanena kuti ng’ombe imaimira mphamvu zake. (Ezekieli 1:4-10) Pamenepa anasankha nyama yoyenera chifukwa ng’ombe, ngakhalenso zoweta, ndi nyama zikuluzikulu komanso zamphamvu. Kale anthu amene ankakhala ku Palestina nthawi zambiri sankaona nyama zina zamphamvu kuposa ng’ombe. Koma ankadziwa ng’ombe zinazake zoopsa kwambiri zam’tchire zotchedwa aurochs, zimene panopa zinatha. (Yobu 39:9-12) Juliasi Kaisara, yemwe anali mfumu ya Roma, ananena kuti ng’ombe zimenezi kukula kwake sizinkasiyana kwenikweni ndi njovu. Iye analemba kuti: “N’gombezi ndi zamphamvu komanso zimathamanga kwambiri.” Mutaima pafupi ndi nyama imeneyi mukhozatu kudziona kuti ndinu kamunthu kakang’ono komanso kopanda mphamvu.
6. N’chifukwa chiyani Yehova yekha ndi amene amatchedwa kuti “Wamphamvuyonse”?
6 Mofanana ndi zimenezi, munthu ndi wamng’ono kwambiri komanso wopanda mphamvu tikamuyerekezera ndi Yehova yemwe ndi Mulungu wa mphamvu. Kwa iye, ngakhale mitundu yamphamvu ya anthu ili ngati fumbi pasikelo. (Yesaya 40:15) Mosiyana ndi cholengedwa chilichonse, Yehova ali ndi mphamvu zopanda malire, chifukwa iye yekha ndi amene amatchedwa kuti “Wamphamvuyonse.” a (Chivumbulutso 15:3) Yehova ali ndi ‘mphamvu zoopsa komanso ali ndi mphamvu zambiri zochitira zinthu.’ (Yesaya 40:26) Kwa iye kumachokera mphamvu zambiri ndipo sizichepa kapena kutha. Sadalira aliyense kuti amupatse mphamvu, chifukwa “mphamvu ndi za Mulungu.” (Salimo 62:11) Koma kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji mphamvu zake?
Mmene Yehova Amagwiritsira Ntchito Mphamvu Zake
7. Kodi mzimu woyera wa Yehova n’chiyani, nanga mawu a zilankhulo zoyambirira omwe anawagwiritsa ntchito m’Baibulo amanena za chiyani?
7 Mphamvu ya mzimu woyera imene imachokera kwa Yehova ndi yopanda malire. Mzimuwu ndi mphamvu ya Mulungu imene imagwira ntchito. Ndipotu pa Genesis 1:2, Baibulo limautchula kuti “mphamvu ya Mulungu.” Mawu a Chiheberi ndi a Chigiriki amene anawamasulira kuti “mzimu” m’mavesi ena anawamasulira kuti “mphepo,” “mpweya” ndiponso “nthunzi.” Mogwirizana ndi zimene akatswiri a Baibulo ananena, mawu a zilankhulo zoyambirirawa amanena za mphamvu yosaoneka yomwe ikugwira ntchito. Mofanana ndi mphepo, mzimu wa Mulungu sitingauone ndi maso, koma zinthu zimene umachita tingathe kuzizindikira.
8. M’Baibulo, kodi mzimu wa Mulungu umatchedwa kuti chiyani mophiphiritsa, nanga n’chifukwa chiyani zimenezi zili zoyenera?
8 Yehova amagwiritsa ntchito mzimu wake woyera m’njira zosiyanasiyana kuti achite chilichonse chimene akufuna. Choncho m’pake kuti m’Baibulo mzimu wa Mulungu umatchulidwa mophiphiritsa kuti “chala” chake, ‘dzanja lake lamphamvu’ kapenanso ‘mkono wake wotambasula.’ (Luka 11:20; Deuteronomo 5:15; Salimo 8:3) Munthu amagwiritsa ntchito manja ake pochita zinthu zosiyanasiyana zofuna mphamvu kapenanso luso. Mofanana ndi zimenezi Mulungu nayenso amagwiritsa ntchito mzimu wake kukwaniritsa cholinga chake chilichonse. Mwachitsanzo, anagwiritsa ntchito mzimuwo kulenga maatomu omwe ndi aang’ono kwambiri, kugawa madzi pa Nyanja Yofiira komanso kuchititsa Akhristu oyambirira kuti alankhule zilankhulo zina.
9. Fotokozani njira ina imene Yehova amasonyezera mphamvu zake.
9 Yehova amasonyezanso mphamvu zake pogwiritsa ntchito udindo wake monga Wolamulira wa Chilengedwe Chonse. Taganizirani mfundo iyi: Iye amalamulira angelo mamiliyoni ambirimbiri omwe amakhala ofunitsitsa kuchita zimene wanena. Palinso anthu omwe ndi atumiki ake ndipo m’Malemba nthawi zambiri amawatchula kuti ndi gulu lalikulu. (Salimo 68:11; 110:3) Komabe anthu ndi ochepa mphamvu poyerekezera ndi angelo. Mwachitsanzo, pamene gulu la nkhondo la Asuri linaukira anthu a Mulungu, mngelo mmodzi yekha anapha asilikali a Asuri 185,000 usiku umodzi wokha. (2 Mafumu 19:35) Angelo a Mulungu ndi “amphamvu” kwambiri.—Salimo 103:19, 20.
10. (a) N’chifukwa chiyani Mulungu Wamphamvuyonse amatchedwa kuti Yehova wa magulu ankhondo akumwamba? (b) Pa zinthu zonse zomwe Yehova analenga, kodi ndi ndani amene ndi wamphamvu kwambiri?
10 Kodi angelo alipo angati? M’masomphenya akumwamba, mneneri Danieli anaona angelo oposa 100 miliyoni ataimirira kumpando wachifumu wa Yehova, koma palibe umboni wosonyeza kuti iye anaona angelo onse. (Danieli 7:10) Choncho n’kutheka kuti angelo alipo mamiliyoni mahandiredi mahandiredi. N’chifukwa chake Mulungu amatchedwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. Dzina la udindo limeneli limatithandiza kumvetsa kuti iye ndi Mtsogoleri wa gulu lalikulu la angelo komanso lochita zinthu mwadongosolo. Iye anaika Mwana wake wokondedwa, “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse,” kuti aziyang’anira angelo onsewa. (Akolose 1:15) Pokhala mkulu wa angelo, yemwe amayang’anira angelo, aserafi ndi akerubi onse, Yesu ndi wamphamvu kwambiri kuposa zinthu zonse zimene Yehova analenga.
11, 12. (a) Kodi mawu a Mulungu amasonyeza kuti ndi amphamvu m’njira zotani? (b) Kodi Yesu ananena chiyani zokhudza mphamvu za Yehova?
11 Pali njira inanso imene Yehova amasonyezera mphamvu zake. Lemba la Aheberi 4:12 limati: “Mawu a Mulungu ndi amoyo komanso amphamvu.” Kodi inuyo mwaonapo umboni wosonyeza kuti mawu a Mulungu, kapena kuti uthenga wouziridwa ndi mzimu umene uli m’Baibulo, ndi amphamvu? Mawuwa angatilimbikitse ndiponso angatithandize kukhala ndi chikhulupiriro cholimba komanso kusintha kwambiri moyo wathu. Mtumwi Paulo anachenjeza okhulupirira anzake zokhudza anthu a makhalidwe oipa kwambiri. Kenako anawonjezera kuti: “Ndipo ena a inu munali otero.” (1 Akorinto 6:9-11) Inde, “mawu a Mulungu” anasonyeza kuti ndi amphamvu ndipo anathandiza anthuwo kuti asinthe.
12 Mphamvu za Yehova n’zambiri ndiponso amazigwiritsa ntchito m’njira yabwino kwambiri moti palibe chilichonse chimene chingamulepheretse kuzigwiritsa ntchito. Yesu ananena kuti: “Zinthu zonse n’zotheka kwa Mulungu.” (Mateyu 19:26) Koma kodi Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zake pa zolinga ziti?
Mulungu Amagwiritsa Ntchito Mphamvu Zake ndi Cholinga
13, 14. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti sikuti Yehova wangokhala malo enaake kumene kumachokera mphamvu? (b) Kodi Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zake m’njira ziti?
13 Mzimu wa Yehova ndi wamphamvu kwambiri kuposa mphamvu ina iliyonse. Sikuti Yehova wangokhala malo enaake kumene kumachokera mphamvu, koma ndi Mulungu amene amaganiza ndipo amasangalala kapenanso kukhumudwa ndi zinthu. Komanso iye amatha kulamulira bwinobwino mphamvu zake. Koma kodi n’chiyani chimamuchititsa kuti azigwiritsa ntchito mphamvu zakezo?
14 Monga mmene tionere, Mulungu amagwiritsa ntchito mphamvu zake polenga, powononga, poteteza komanso pobwezeretsa zinthu. Mwachidule tingoti pochita chilichonse chimene chikufunika kuti akwaniritse zolinga zake. (Yesaya 46:10) Pa zochitika zina, Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zake pofuna kutiphunzitsa zinthu zofunika zokhudza iyeyo komanso mfundo zake. Chofunika kwambiri n’chakuti iye amagwiritsa ntchito mphamvu zake pofuna kukwaniritsa chifuniro chake, chomwe ndi kuyeretsa dzina lake pogwiritsa ntchito Ufumu wa Mesiya. Zimenezi zimasonyeza kuti ulamuliro wake ndi wabwino kwambiri. Ndipotu palibe chimene chingalepheretse cholinga chakechi.
15. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji mphamvu zake pothandiza atumiki ake, nanga anasonyeza bwanji zimenezi kwa Eliya?
15 Yehova amagwiritsanso ntchito mphamvu zake potithandiza aliyense payekha. Taonani zimene lemba la 2 Mbiri 16:9 limanena: “Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu odzipereka ndi mtima wonse kwa iye.” Chitsanzo cha zimenezi ndi zomwe zinachitikira Eliya, zimene zatchulidwa koyambirira kwa mutuwu. N’chifukwa chiyani Yehova anamuonetsa mphamvu zake mochititsa mantha choncho? Yezebeli yemwe anali mfumukazi yoipa anali atalumbira kuti apha Eliya. Mneneriyu ankathawa pofuna kupulumutsa moyo wake. Iye ankaona kuti ali yekhayekha, ankachita mantha komanso ankaganiza kuti ntchito yaikulu yomwe anagwira siinaphule kanthu. Kuti alimbikitse Eliya, yemwe anali ndi nkhawa, Yehova anamukumbutsa kuti iye ndi wamphamvu kwambiri. Mphepo, chivomerezi ndiponso moto zinasonyeza kuti Mulungu yemwe ndi wamphamvu kwambiri m’chilengedwe chonse anali naye. Panalibe chifukwa choti aziopera Yezebeli popeza Mulungu wamphamvuyonse anali kumbali yake.—1 Mafumu 19:1-12. b
16. N’chifukwa chiyani n’zolimbikitsa kuganizira mozama mphamvu za Yehova zomwe ndi zambiri?
16 Ngakhale kuti masiku ano Yehova sachita zodabwitsa, kuchokera mu nthawi ya Eliya mpaka pano iye sanasinthe. (1 Akorinto 13:8) Amafunitsitsabe kugwiritsa ntchito mphamvu zake kuti athandize anthu amene amamukonda. N’zoona kuti iye amakhala kumwamba, koma sikuti ali nafe kutali. Mphamvu zake n’zopanda malire choncho zikhoza kufika kulikonse. Ndipotu “Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuitana.” (Salimo 145:18) Pamene mneneri Danieli ankapempha Yehova kuti amuthandize, mngelo anafika kwa iye asanamalize n’komwe kupemphera. (Danieli 9:20-23) Palibe chomwe chingalepheretse Yehova kuti athandize komanso kulimbikitsa anthu amene amawakonda.—Salimo 118:6.
Kodi Tizichita Mantha Kuyandikira Mulungu Chifukwa Ndi Wamphamvu?
17. Kodi mphamvu za Yehova zimatithandiza kuti tizimuopa mwanjira iti, nanga sitiyenera kukhala ndi mantha ati?
17 Kodi tiyenera kumaopa Mulungu chifukwa choti ali ndi mphamvu? Tingayankhe kuti inde komanso ayi. Tinganene kuti inde chifukwa khalidweli limatichititsa kuti tizimuopa moyenera komanso tizimulemekeza kwambiri monga taonera m’mutu wapitawu. Baibulo limatiuza kuti mantha amenewa, ndi “chiyambi cha nzeru.” (Salimo 111:10) Koma tingayankhenso kuti ayi chifukwa palibe chifukwa chilichonse choti tizinjenjemera ndi mantha kapena tizilephera kumuyandikira chifukwa choti iye ali ndi mphamvu.
18. (a) N’chifukwa chiyani ambiri sakhulupirira anthu amene ali ndi mphamvu? (b) Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova sangakhale ndi makhalidwe oipa ngakhale kuti ali ndi mphamvu?
18 Mu 1887 wolemba mbiri wina wa ku England, dzina lake Acton analemba kuti: “Mphamvu zimapangitsa munthu kukhala ndi makhalidwe oipa ndipo mphamvu zambiri zimapangitsa munthu kukhala ndi makhalidwe oipa kwambiri.” Mawu amenewa akhala akubwerezedwa ndi anthu ambiri mwina chifukwa choti amaona kuti mfundo imeneyi ndi yosatsutsika. Popeza anthu si angwiro, nthawi zambiri amagwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika ndipo zimenezi n’zimene zakhaladi zikuchitika kuyambira kalekale. (Mlaliki 4:1; 8:9) Chifukwa cha zimenezi, ambiri sakhulupirira anthu omwe ali ndi mphamvu ndipo safuna kukhala nawo pafupi. Yehova ali ndi mphamvu kuposa aliyense. Koma kodi mphamvu zimenezi zimamuchititsa kukhala ndi makhalidwe oipa? Ayi ndithu. Paja taona kuti iye ndi woyera ndipo sangakhale ndi makhalidwe oipa. Yehova ndi wosiyana ndi amuna ndi akazi omwe si angwiro amene ali ndi mphamvu m’dziko loipali. Iye sanagwiritsepo ntchito molakwika mphamvu zake, ndipo sangachite zimenezi.
19, 20. (a) Kodi nthawi zonse Yehova akamasonyeza mphamvu zake amasonyezanso makhalidwe ena ati, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zili zolimbikitsa? (b) Fotokozani chitsanzo chosonyeza kuti Yehova ndi wodziletsa, nanga n’chifukwa chiyani mukuona kuti zimenezi n’zosangalatsa?
19 Kumbukirani kuti mphamvu si khalidwe lokhalo limene Yehova ali nalo. Kutsogoloku tiphunziranso za chilungamo, nzeru ndiponso chikondi chake. Koma tisaganize kuti Yehova amasonyeza khalidwe lililonse palokhapalokha. Monga mmene tionere m’mitu yotsatirayi, nthawi zonse Yehova akamasonyeza mphamvu zake, amasonyezanso chilungamo, nzeru ndiponso chikondi. Komanso taganizirani za khalidwe lina limene Mulungu ali nalo, limene atsogoleri ambiri a m’dzikoli alibe. Khalidwe limeneli ndi kudziletsa.
20 Tiyerekeze kuti mwakumana ndi chimunthu chachikulu ndiponso champhamvu moti mukuchita mantha. Koma kenako mukuzindikira kuti munthu wake ndi wodekha. Iye ndi wofunitsitsa kugwiritsa ntchito mphamvu zakezo pothandiza ndiponso kuteteza anthu, makamaka amene alibe wowathandiza. Munthuyo sagwiritsa ntchito mphamvu zake molakwika. Anthu akumunenera zoipa pa zifukwa zosamveka, koma iye sakutekeseka ndipo akukhalabe wodekha. Mukuyamba kukayikira ngati inuyo mukanakwanitsa kuchita zimenezi, makamaka mukanakhala wamphamvu ngati iyeyo. Pamene mukupitiriza kumudziwa bwino, n’zosachita kufunsa kuti mungayambenso kufuna kuti akhale mnzanu. Tili ndi chifukwa chomveka chotichititsa kuti tizifuna kuti Yehova wamphamvuyonse akhale mnzathu. Taganizirani chiganizo chonse pamene pachokera mutu wa nkhaniyi: “Yehova sakwiya msanga ndipo ali ndi mphamvu zambiri.” (Nahumu 1:3) Yehova safulumira kugwiritsa ntchito mphamvu zake polanga anthu, ngakhale anthu oipa. Iye safulumira kukwiya ndipo ndi wokoma mtima. Ngakhale kuti nthawi zambiri anthu amamukhumudwitsa, iye wasonyeza kuti “sakwiya msanga.”—Salimo 78:37-41.
21. N’chifukwa chiyani Yehova sakakamiza anthu kuti azimutumikira, ndipo kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani zokhudza iyeyo?
21 Yehova amasonyeza kudziletsa m’njira inanso. Kodi inuyo mukanakhala ndi mphamvu zambiri, bwenzi nthawi zina mukufuna kuti anthu achite zinthu m’njira imene inuyo mukuganiza? Yehova ali ndi mphamvu zonse, koma sakakamiza anthu kuti azimutumikira. Ngakhale kuti kutumikira Mulungu n’kumene kudzachititse kuti tidzapeze moyo wosatha, Yehova satikakamiza kumutumikira. M’malomwake, iye amalemekeza munthu aliyense pomupatsa ufulu wosankha. Amatichenjeza kuti ngati munthu sanasankhe bwino, amakumana ndi mavuto ndipo amatiuzanso kuti munthu akasankha mwanzeru, zotsatira zake zimakhala zabwino. Koma amatisiya kuti tisankhe tokha. (Deuteronomo 30:19, 20) Yehova safuna kuti anthu azimutumikira chifukwa chokakamizika kapena chifukwa choopa kuti iye ali ndi mphamvu zambiri. Amafuna kuti anthu omwe amamutumikira mwa kufuna kwawo chifukwa choti amamukonda.—2 Akorinto 9:7.
22, 23. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova amasangalala kupatsa ena mphamvu? (b) Kodi tiphunzira chiyani m’mutu wotsatira?
22 Tiyeni tione chifukwa chomaliza chotichititsa kuti tisamachite mantha ndi Mulungu Wamphamvuyonse. Anthu omwe ali ndi mphamvu amaopa kugawirako ena mphamvu zawo. Komatu Yehova amasangalala kupereka mphamvu kwa atumiki ake okhulupirika. Amapatsakonso ena mphamvu zake. Mwachitsanzo, anapereka mphamvu zambiri ndithu kwa Mwana wake. (Mateyu 28:18) Yehova amapatsa mphamvu atumiki ake m’njira inanso. Baibulo limati: “Inu Yehova, ukulu, mphamvu, kukongola, ulemerero ndi ulemu ndi zanu, chifukwa zinthu zonse zakumwamba ndi zapadziko lapansi ndi zanu. . . . M’dzanja lanu muli mphamvu ndi nyonga ndipo dzanja lanu limatha kukweza ndiponso kupereka mphamvu kwa onse. “—1 Mbiri 29:11, 12.
23 Izitu zikusonyeza kuti Yehova amasangalala kukupatsani mphamvu. Iye amaperekanso “mphamvu yoposa yachibadwa” kwa anthu amene akufuna kumutumikira. (2 Akorinto 4:7) Kodi kudziwa zimenezi sikukukuchititsani kufuna kuti Mulungu ameneyu, yemwe amagwiritsa ntchito mphamvu zake mokoma mtima ndi mwachikondi, akhale mnzanu? M’mutu wotsatira, tiona mmene Yehova anagwiritsira ntchito mphamvu zake polenga zinthu.
a Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “Wamphamvuyonse” amatanthauza kuti “Wolamulira Zinthu Zonse; Amene Ali ndi Mphamvu Zonse.”
b Baibulo limati ‘Yehova sanali mumphepoyo, m’chivomerezicho ndiponso m’motowo.’ Atumiki a Yehova sali ngati anthu amene amalambira mphamvu zam’chilengedwe. Yehova ndi wamkulu kwambiri moti sangakwane m’chilichonse chimene analenga.—1 Mafumu 8:27.