GAWO 4
“Mulungu Ndi Chikondi”
Pa makhalidwe onse a Yehova, khalidwe lake lalikulu kwambiri ndi chikondi. Khalidweli ndi limene limatichititsanso kuti tizifuna kuti akhale mnzathu. Tikamaphunzira zambiri zokhudza mmene amasonyezera khalidwe lapaderali, tiona chifukwa chake Baibulo limanena kuti “Mulungu ndi chikondi.”—1 Yohane 4:8.
M'CHIGAWO ICHI
MUTU 23
“Mulungu Ndi Amene Anayamba Kutikonda”
Kodi mawu akuti “Mulungu ndi chikondi” amatanthauza chiyani?
MUTU 24
Palibe Chimene ‘Chingatisiyanitse ndi Chikondi cha Mulungu’
Muzichotsa maganizo abodza akuti Mulungu sangakukondeni kapena akuti amakuonani kuti ndinu osafunika.
MUTU 25
“Chifundo Chachikulu cha Mulungu Wathu”
Kodi mmene Mulungu amakusonyezerani chifundo zikufanana bwanji ndi mmene mayi amasonyezera chifundo mwana wake?
MUTU 26
Mulungu “Wokonzeka Kukhululuka”
Popeza Mulungu amakumbukira zonse, kodi amakhululuka ndipo sakumbukiranso machimo a munthu m’njira yotani?
MUTU 28
‘Inu Nokha Ndinu Wokhulupirika’
Kodi kukhulupirika kwa Mulungu kumaposa bwanji kudalirika kwake?
MUTU 29
“Mudziwe Chikondi cha Khristu”
Njira zitatu zimene Yesu anasonyezera chikondi zimasonyeza bwino chikondi cha Yehova.
MUTU 30
“Pitirizani Kusonyeza Chikondi”
Buku la 1 Akorinto limafotokoza njira zosiyanasiyana zomwe tingasonyezere chikondi.