Yandikirani Yehova

Mulungu akukupemphani kuti mukhale mnzake. Pogwiritsa ntchito Baibulo, bukuli likuthandizani kudziwa mmene mungachitire zimenezi.

Mawu Oyamba

Yehova Mulungu akhoza kukhala mnzanu ndipo ubwenzi umenewu sungathe.

MUTU 1

“Taonani! Uyu Ndi Mulungu Wathu”

N’chifukwa chiyani Mose anafunsa dzina la Mulungu ngakhale kuti ankalidziwa kale?

MUTU 2

Kodi N’zothekadi ‘Kuyandikira Mulungu’?

Yehova Mulungu, Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi akutiuza kuti timuyandikire ndipo nayenso adzatiyandikira.

MUTU 3

“Woyera, Woyera, Woyera Ndi Yehova”

N’chifukwa chiyani Baibulo limati pali kugwirizana pakati pa kukongola ndi kuyera?

MUTU 4

‘Yehova Ali Ndi Mphamvu Zambiri’

Kodi tiziopa Mulungu chifukwa choti ali ndi mphamvu? Tingayankhe kuti inde komanso ayi.

MUTU 5

Mphamvu za Kulenga​—“Amene Anapanga Kumwamba Komanso Dziko Lapansi”

Zinthu zimene Mulungu analenga, kuyambira dzuwa lamphamvu mpaka kambalame kakang’ono kotchedwa hummingbird, zingatiphunzitse mfundo zofunika zokhudza iye.

MUTU 6

Mphamvu Zowononga​—‘Yehova Ndi Msilikali Wamphamvu’

N’chifukwa chiyani “Mulungu wamtendere” amamenya nkhondo?

MUTU 7

Mphamvu Zoteteza​—“Mulungu Ndi Pothawira Pathu”

Mulungu amateteza atumiki ake m’njira ziwiri, koma njira inayo ndi yofunika kwambiri.

MUTU 8

Mphamvu Zobwezeretsa​—Yehova ‘Akupanga Zinthu Zonse Kuti Zikhale Zatsopano’

Yehova, wabwezeretsa kale kulambira koona. Kodi ndi zinthu ziti zomwe adzabwezeretse m’tsogolo?

MUTU 9

“Khristu Ndi Mphamvu ya Mulungu”

Kodi zodabwitsa za Yesu Khristu komanso zimene ankaphunzitsa zimasonyeza kuti Yehova ndi wotani?

MUTU 10

“Muzitsanzira Mulungu” Mukamagwiritsa Ntchito Mphamvu

N’kutheka kuti muli ndi mphamvu zambiri kuposa mmene mukuganizira. Kodi mungazigwiritse ntchito bwanji moyenera?

MUTU 11

“Njira Zake Zonse Ndi Zolungama”

N’chifukwa chiyani chilungamo cha Mulungu ndi khalidwe losangalatsa?

MUTU 12

“Kodi Mulungu Alibe Chilungamo?”

Ngati Yehova amadana ndi zinthu zopanda chilungamo, n’chifukwa chiyani zachuluka kwambiri m’dzikoli?

MUTU 13

‘Malamulo a Yehova Ndi Angwiro’

Kodi malamulo angathandize bwanji anthu kuti azisonyeza chikondi?

MUTU 14

Yehova Anapereka “Dipo Kuti Awombole Anthu Ambiri”

Mfundo yosavuta koma yofunika kwambiri ingathandize kuti Mulungu akhale mnzanu.

MUTU 15

Yesu ‘Akukhazikitsa Chilungamo Padziko Lapansi’

Kodi Yesu analimbikitsa bwanji chilungamo? Kodi panopa akukhazikitsa bwanji chilungamo? Nanga m’tsogolo adzakhazikitsa bwanji chilungamo?

MUTU 16

‘Muzichita Chilungamo’ Poyenda ndi Mulungu

Chilungamo chimaphatikizapo mmene timaonera chabwino ndi choipa komanso mmene timachitira zinthu ndi ena.

MUTU 17

‘Nzeru za Mulungu N’zozama’

N’chifukwa chiyani nzeru za Mulungu zimaposa ngakhale zinthu zimene amazidziwa komanso kuzimvetsa?

MUTU 18

“Mawu a Mulungu” Amasonyeza Kuti Iye Ndi Wanzeru

N’chifukwa chiyani Mulungu anagwiritsa ntchito anthu kuti alembe maganizo ake m’buku, nanga ndi zinthu ziti zomwe zinaikidwa m’bukuli komanso zomwe sizinaikidwemo?

MUTU 19

‘Nzeru ya Mulungu Imaonekera mu Chinsinsi Chopatulika’

Kodi chinsinsi chopatulika chimene Mulungu wakhala akuchiulula pang’onopang’ono n’chiyani?

MUTU 20

“Ali ndi Mtima Wanzeru” Koma Ndi Wodzichepetsa

Kodi zingatheke bwanji kuti Ambuye Wamkulu Koposa wa chilengedwe chonse akhale wodzichepetsa?

MUTU 21

Yesu Amatisonyeza “Nzeru za Mulungu”

Yesu ankaphunzitsa mwaluso kwambiri moti nthawi ina alonda omwe anatumidwa kuti akamugwire anabwerera chimanjamanja.

MUTU 22

Kodi Mumagwiritsa Ntchito “Nzeru Yochokera Kumwamba” pa Moyo Wanu?

Baibulo limatchula mfundo 4 zomwe zingakuthandizeni kukhala ndi nzeru za Mulungu.

MUTU 23

“Mulungu Ndi Amene Anayamba Kutikonda”

Kodi mawu akuti “Mulungu ndi chikondi” amatanthauza chiyani?

MUTU 24

Palibe Chimene ‘Chingatisiyanitse ndi Chikondi cha Mulungu’

Muzichotsa maganizo abodza akuti Mulungu sangakukondeni kapena akuti amakuonani kuti ndinu osafunika.

MUTU 25

“Chifundo Chachikulu cha Mulungu Wathu”

Kodi mmene Mulungu amakusonyezerani chifundo zikufanana bwanji ndi mmene mayi amasonyezera chifundo mwana wake?

MUTU 26

Mulungu “Wokonzeka Kukhululuka”

Popeza Mulungu amakumbukira zonse, kodi amakhululuka ndipo sakumbukiranso machimo a munthu m’njira yotani?

MUTU 27

“Ubwino Wake Ndi Waukulu Kwambiri!”

Kodi Mulungu amasonyeza bwanji kuti ndi wabwino?

MUTU 28

‘Inu Nokha Ndinu Wokhulupirika’

Kodi kukhulupirika kwa Mulungu kumaposa bwanji kudalirika kwake?

MUTU 29

“Mudziwe Chikondi cha Khristu”

Njira zitatu zimene Yesu anasonyezera chikondi zimasonyeza bwino chikondi cha Yehova.

MUTU 30

“Pitirizani Kusonyeza Chikondi”

Buku la 1 Akorinto limafotokoza njira zosiyanasiyana zomwe tingasonyezere chikondi.

MUTU 31

“Yandikirani Mulungu Ndipo Iyenso Adzakuyandikirani”

Kodi ndi funso lofunika kwambiri liti lomwe mungadzifunse? Ndiye kodi mungaliyankhe bwanji?