PHUNZIRO 4
Kodi Yesu Khristu Ndani?
1. Kodi moyo wa Yesu unayamba bwanji?
Mosiyana ndi munthu wina aliyense, Yesu anakhalapo kumwamba asanabwere padziko lapansi, ndipo anali ndi thupi lauzimu. (Yohane 8:23) Iye anali woyamba pa zinthu zonse zimene Mulungu analenga, ndipo anathandiza Mulungu pa ntchito yolenga zinthu zina zonse. Ndi Yesu yekha amene Yehova anamulenga mwachindunji, ndipo mpake kuti amatchedwa Mwana “wobadwa yekha” wa Mulungu. (Yohane 1:14) Pa nthawi ina Yesu ankalankhula m’malo mwa Mulungu, choncho amatchedwanso kuti “Mawu.”—Werengani Miyambo 8:22, 23, 30; Akolose 1:15, 16.
2. N’chifukwa chiyani Yesu anabwera padziko lapansi?
Mulungu anatumiza Mwana wake padziko lapansi posamutsa moyo wake kumwamba, n’kuuika m’mimba mwa namwali wina wachiyuda, dzina lake Mariya. Choncho Yesu analibe bambo womubereka. (Luka 1:30-35) Yesu anabwera padziko lapansi (1) kudzaphunzitsa anthu choonadi chokhudza Mulungu, (2) kudzatisonyeza chitsanzo cha mmene tingachitire chifuniro cha Mulungu ngakhale pamene tili m’mavuto, komanso (3) kudzapereka moyo wake wangwiro kuti ukhale “dipo.”—Werengani Mateyu 20:28.
3. N’chifukwa chiyani tikufunikira dipo?
Dipo ndi malipiro amene munthu amapereka pofuna kuwombola munthu wina kuti asaphedwe. (Ekisodo 21:29, 30) Pamene Mulungu ankalenga anthu, analibe cholinga choti anthuwo azikalamba komanso kufa. Tikudziwa bwanji zimenezi? Tikudziwa zimenezi chifukwa chakuti Mulungu anauza munthu woyamba, Adamu, kuti akadzachita “tchimo,” malinga n’kunena kwa Baibulo, adzafa. Choncho Adamu akanapanda kuchimwa, sakanafa. (Genesis 2:16, 17; 5:5) Malinga ndi zimene Baibulo limanena, imfa ‘inalowa’ m’dziko kudzera mwa Adamu. Choncho Adamu anapatsira ana ake onse uchimo, womwe chilango chake ndi imfa. N’chifukwa chake tikufunikira dipo lotiwombola kuti tisadzalandire chilango cha imfa chimene tinatengera kwa Adamu.—Werengani Aroma 5:12; 6:23.
Kodi ndani amene akanapereka dipo lotiwombola ku imfa? Panopa munthu aliyense akamwalira, amakhala ngati wapereka malipiro a machimo ake okha. Munthu wopanda ungwiro sangathe kupereka dipo lowombola anthu ena.—Werengani Salimo 49:7-9.
4. N’chifukwa chiyani Yesu anafa?
Mosiyana ndi ife, Yesu anali wangwiro. Choncho sanafunike kufa chifukwa cha machimo ake, popeza sanachite tchimo lililonse. M’malomwake, Yesu anafa chifukwa cha machimo a anthu ena. Mulungu anasonyeza kuti amakonda kwambiri anthu potumiza Mwana wake kuti adzatifere. Nayenso Yesu anasonyeza kuti amatikonda chifukwa anamvera Atate wake pololera kupereka moyo wake kuti atiwombole ku machimo athu.—Werengani Yohane 3:16; Aroma 5:18, 19.
Onerani vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Yesu Anafa?
5. Kodi panopa Yesu akuchita chiyani?
Pamene anali padziko lapansi, Yesu anachiritsa odwala, anaukitsa akufa komanso anathandiza anthu amene anali m’mavuto osiyanasiyana. Iye anachita zimenezi pofuna kusonyeza zimene adzachite m’tsogolo kwa anthu onse omvera. (Mateyu 15:30, 31; Yohane 5:28) Yesu atafa, Mulungu anamuukitsa ndi thupi lauzimu. (1 Petulo 3:18) Kenako Yesu anadikira kudzanja lamanja la Mulungu kufikira pamene Yehova anamupatsa mphamvu zoti alamulire padziko lonse lapansi monga Mfumu. (Aheberi 10:12, 13) Panopa Yesu akulamulira monga Mfumu kumwamba ndipo otsatira ake akulengeza uthenga wabwinowu padziko lonse lapansi.—Werengani Danieli 7:13, 14; Mateyu 24:14.
Posachedwapa, Yesu adzagwiritsa ntchito mphamvu zake monga Mfumu pothetsa mavuto onse komanso powononga anthu onse amene amayambitsa mavutowo. Anthu onse amene amakhulupirira Yesu komanso kumumvera adzasangalala ndi moyo m’paradaiso padziko lapansi.—Werengani Salimo 37:9-11.