GAWO 8
Aisiraeli Analowa M’dziko la Kanani
Yoswa anatsogolera Aisiraeli pogonjetsa dziko la Kanani. Yehova anathandiza oweruza kuti apulumutse anthu ake m’manja mwa anthu amene ankawazunza
PAFUPIFUPI zaka 470 Aisiraeli asanalowe m’dziko la Kanani, Yehova analonjeza kuti adzapereka dzikolo kwa mbadwa za Abulahamu. Tsopano motsogoleredwa ndi Yoswa, Aisiraeli anali okonzeka kutenga Dziko Lolonjezedwa kuti likhale lawo.
Mulungu anali ataweruza kuti Akanani ayenera kuwonongedwa. Iwo anaipitsa dzikolo ndi makhalidwe oipa kwambiri a chiwerewere ndiponso ankaphana mwachisawawa. Choncho Aisiraeli anayenera kuwonongeratu mizinda ya Akanani imene anaigonjetsa.
Koma iwo asanalowe m’dzikolo, Yoswa anatumiza azondi awiri mumzinda wa Yeriko ndipo anakakhala m’nyumba ya mayi wina dzina lake Rahabi. Mayiyu analandira azondiwo ndipo anawateteza ngakhale ankadziwa kuti anali Aisiraeli. Rahabi ankakhulupirira Mulungu wa Aisiraeli chifukwa anamva zimene Yehova anachita populumutsa anthu ake. Choncho iye anauza azondiwo kuti alumbire kuti iye ndi anthu a m’banja lake sadzaphedwa Aisiraeliwo akamawononga mzindawo.
Kenako Aisiraeli atalowa m’dziko la Kanani n’kuzungulira mzinda wa Yeriko, mozizwitsa Yehova anagwetsa makoma a mpanda wa Yeriko. Ndiyeno asilikali a Yoswa analowa mumzindawo mofulumira ndi kuuwononga, koma sanaphe Rahabi ndi anthu a m’banja lake. Kenako, Yoswa anamenya nkhondo zosiyanasiyana kwa zaka 6, ndipo anagonjetsa adani awo ndi kutenga dera lalikulu la Dziko Lolonjezedwa. Atatero anagawa dzikolo kwa mafuko a Isiraeli.
Cha kumapeto kwa utumiki wake, Yoswa anasonkhanitsa anthu. Iye anakambirana nawo zimene Yehova anachitira makolo awo ndipo anawalimbikitsa kuti apitirize kutumikira Yehova. Koma Yoswa ndi akuluakulu ena amene ankatumikira naye limodzi atamwalira, Aisiraeli anasiya Yehova ndipo anayamba kutumikira milungu yonyenga. Chotero kwa zaka pafupifupi 300, nthawi zina mtundu wa Isiraeli sunkatsatira malamulo a Yehova. Pa nthawi imeneyo, Yehova ankalola kuti Aisiraeliwo azizunzidwa ndi adani awo, monga Afilisiti. Koma Aisiraeli atapempha Yehova kuti awathandize, iye anasankha oweruza kuti awapulumutse ndipo oweruza onse analipo 12.
Malinga ndi zimene buku la Oweruza limafotokoza, woweruza woyamba kutsogolera mtundu wa Isiraeli anali Otiniyeli ndipo womaliza anali Samisoni, amene anali munthu wamphamvu kwambiri kuposa aliyense. Mfundo yaikulu imene ikuonekera mobwerezabwereza m’nkhani yosangalatsa ya m’buku la Oweruza ndi yakuti: Munthu amapeza madalitso akamamvera Yehova, koma akapanda kumumvera amakumana ndi mavuto.
—Nkhaniyi yachokera m’mabuku a Yoswa; ndi Oweruza; komanso pa Levitiko 18:24, 25.