Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 20

Utumiki Wothandiza Anthu pa Nthawi ya Mavuto

Utumiki Wothandiza Anthu pa Nthawi ya Mavuto

CHOLINGA CHA MUTUWU

Akhristu amasonyezana chikondi pa nthawi ya mavuto

1, 2. (a) Kodi Akhristu omwe ankakhala ku Yudeya anakumana ndi mavuto otani? (b) Kodi Akhristuwa anathandizidwa bwanji?

 M’CHAKA cha 46 C.E., ku Yudeya kunali njala yoopsa. Chifukwa chakuti chakudya chinali chochepa, chinkadula kwambiri moti Ayuda omwe anali ophunzira a Khristu sakanakwanitsa kugula. Anali ndi njala ndipo zinkachita kuonekeratu kuti zinthu sizili bwino. Komabe, Yehova anali atatsala pang’ono kuwateteza m’njira imene anali asanachitirepo wophunzira wa Khristu aliyense. Kodi Mulungu anawateteza bwanji?

2 Akhristu achiyuda komanso amitundu ina a ku Antiokeya, wa ku Siriya, atamva za mavuto amene Akhristu anzawo achiyuda a ku Yerusalemu ndi ku Yudeya akukumana nawo, anamva chisoni ndipo anasonkhanitsa zinthu zoti athandizire okhulupirira anzawowo. Kenako anasankha abale awiri oyenerera, omwe ndi Baranaba ndi Saulo, kuti akapereke thandizolo kwa akulu a mpingo wa ku Yerusalemu. (Werengani Machitidwe 11:27-30; 12:25.) Taganizani mmene abale a ku Yudeya anamvera ataona chikondi cha abale awo a ku Antiokeya.

3. (a) Kodi anthu a Mulungu masiku ano amatsatira bwanji chitsanzo cha Akhristu a ku Antiokeya? Perekani chitsanzo. (Onaninso bokosi lakuti, “ Ntchito Yaikulu Yoyamba Yothandiza Anthu M’nthawi Yathu Ino.”) (b) Kodi mu nkhaniyi tikambirana mafunso ati?

3 Zimene zinachitika pa nthawiyi ndi nkhani yoyamba kulembedwa yosonyeza Akhristu a dziko lina akutumiza thandizo kwa Akhristu anzawo a m’dziko lina. Masiku ano, timatsanzira chitsanzo cha abale athu a ku Antiokeya. Tikamva kuti okhulupirira anzathu a m’dera lina akuzunzika chifukwa cha nkhondo, masoka achilengedwe kapena chifukwa cha mavuto a zandale, timawathandiza. a Kuti timvetse kugwirizana kwa ntchito yothandiza anthuyi ndi mautumiki ena amene timachita, tiyeni tikambirane mafunso atatu okhudza ntchito yothandiza anthu amene ali pa mavuto. Mafunso ake ndi akuti: N’chifukwa chiyani timaona kuti ntchito yothandiza anthu pa mavuto ndi utumiki? Kodi zolinga zathu pogwira ntchitoyi ndi zotani? Kodi timapindula bwanji ndi ntchito imeneyi?

N’chifukwa Chiyani Timaona Kuti Kuthandiza Anthu pa Mavuto Ndi “Utumiki Wopatulika”?

4. Kodi Paulo anafotokozera chiyani Akorinto pa nkhani ya utumiki wachikhristu?

4 M’kalata yake yachiwiri yopita kwa Akorinto, Paulo anafotokoza kuti utumiki umene Akhristu ali nawo uli ndi mbali ziwiri. Ngakhale kuti kalata ya Paulo inkapita kwa Akhristu odzozedwa, masiku ano mawu akewa amagwiranso ntchito kwa “nkhosa zina” za Khristu. (Yoh. 10:16) Mbali yoyamba ndi “utumiki wokhazikitsanso mtendere,” womwe ndi ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa anthu. (2 Akor. 5:18-20; 1 Tim. 2:3-6) Mbali yachiwiri ndi utumiki umene timachitira okhulupirira anzathu. Ndipotu Paulo anatchula mwachindunji “utumiki wothandiza” anthu. (2 Akor. 8:4) Mawu akuti “utumiki,” omwe ali m’chiganizo chakuti “utumiki wokhazikitsanso mtendere,” komanso chakuti “utumiki wothandiza” anthu, anatanthauziridwa kuchokera ku mawu achigiriki akuti di·a·ko·niʹa. Kodi kudziwa kumene mawuwa anachokera n’kothandiza bwanji?

5. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Paulo ananena zoti ntchito yothandiza anthu pa nthawi ya mavuto ndi utumiki?

5 Kugwiritsa ntchito mawu ofanana m’ziganizo ziwirizi, kukusonyeza kuti Paulo ankaona kuti ntchito yothandiza anthu ndi yofanana ndi mautumiki ena onse amene ankachitika mumpingo wachikhristu. Iye anali atanenanso kale kuti: “Pali mautumiki osiyanasiyana, koma Ambuye ndi mmodzi. Palinso ntchito zosiyanasiyana, . . . Koma ntchito zonsezi, mzimu umodzimodziwo ndiwo umazichita.” (1 Akor. 12:4-6, 11) Ndipotu Paulo ananena kuti mautumiki osiyanasiyana ochitika pampingo ndi “utumiki wopatulika.” b (Aroma 12:1, 6-8) N’chifukwa chake ankaona kuti ndi bwino kuti nthawi yake ina aziigwiritsa ntchito ‘kutumikira oyera.’​—Aroma 15:25, 26.

6. (a) Malinga ndi zimene Paulo ananena, n’chifukwa chiyani tinganene kuti ntchito yothandiza anthu ndi mbali ya kulambira kwathu? (b) Fotokozani mmene ntchito yothandiza anthu pa mavuto ikuchitikira padziko lonse lapansi. (Onani bokosi lakuti “ Kukonzekera Masoka a Chilengedwe” patsamba 214.)

6 Paulo anathandiza Akorinto kuti adziwe chifukwa chake ntchito yothandiza anthu inali mbali ya utumiki komanso kulambira kwawo Yehova. Iye ananena kuti: Akhristu amene amathandiza Akhristu anzawo amachita zimenezo chifukwa ‘chogonjera uthenga wabwino wonena za Khristu.’ (2 Akor. 9:13) Choncho, pofuna kutsatira zimene Khristu anaphunzitsa, Akhristu amathandiza okhulupirira anzawo. Paulo ananenanso kuti zinthu zabwino zimene amachitira abale awo ndi ‘kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu wawasonyeza.’ (2 Akor. 9:14; 1 Pet. 4:10) Posonyeza kufunika kotumikira abale athu amene ali pa mavuto, Nsanja ya Olonda ya December 1, 1975, inanena kuti: “Tisamakayikire kuti Yehova Mulungu ndi Mwana wake Yesu Khristu amaona kuti utumiki umenewu ndi wofunika kwambiri.” Izi zikusonyeza kuti kuthandiza anthu amene ali pa mavuto ndi mbali yofunika kwambiri ya utumiki wopatulika.​—Aroma 12:1, 7; 2 Akor. 8:7; Aheb. 13:16.

Zolinga Zathu Pogwira Ntchito Yothandiza Anthu

7, 8. Kodi cholinga chathu choyamba pothandiza anthu amene ali pa mavuto ndi chiyani? Fotokozani.

7 Kodi zolinga zathu pogwira ntchitoyi ndi zotani? Paulo anayankha funso limeneli m’kalata yake yachiwiri yopita kwa Akorinto. (Werengani 2 Akorinto 9:11-15.) M’mavesi amenewa, Paulo anafotokoza zifukwa zitatu, kapena kuti zolinga, zimene timakwaniritsa tikamachita nawo “utumiki wothandiza anthu umenewu.” Tiyeni tikambirane zolinga zimenezi chimodzi ndi chimodzi.

8 Choyamba, utumiki wothandiza anthu amene ali pa mavuto umalemekeza Yehova. Onani kuti m’mavesi 5 amene tawerenga pamwambawa, Paulo analimbikitsa abale kuganizira kwambiri za Yehova Mulungu. Mtumwiyu anawakumbutsa “kuyamika Mulunguyo” ndiponso “kupereka mapemphero ochuluka oyamika Mulungu.” (Vesi 11, 12) Anafotokoza mmene ntchito yothandiza anthu amene ali pa mavuto imachititsira Akhristu ‘kulemekeza Mulungu’ ndiponso kuyamikira “kukoma mtima kwakukulu [kwa] Mulungu.” (Vesi 13, 14) Paulo anamaliza nkhaniyi ndi mawu akuti: “Tikuyamika Mulungu.”​—Vesi 15; 1 Pet. 4:11.

9. Kodi ntchito yothandiza anthu imene timagwira imathandiza bwanji anthu ena kusintha mmene amaonera Mboni za Yehova? Perekani chitsanzo.

9 Mofanana ndi Paulo, atumiki a Mulungu a masiku ano amaona kuti kuthandiza anzawo amene ali pa mavuto ndi mwayi wawo wolemekeza Yehova komanso wokometsera zimene Mulungu amaphunzitsa. (1 Akor. 10:31; Tito 2:10) Ndipotu nthawi zambiri ntchito imeneyi imathandiza anthu amene anali ndi maganizo olakwika onena za Yehova ndi Mboni zake kuti asinthe. Mwachitsanzo: Mzimayi wina, yemwe ankakhala m’dera limene kunachitika mphepo yamkuntho, analemba pakhomo pake mawu akuti “Kuno a Mboni Ayi.” Kenako tsiku lina, mzimayiyu anaona anthu akukonza nyumba yomwe inawonongeka ndi mphepoyo mbali ina ya msewu wapafupi ndi nyumba yake. Kwa masiku angapo, ankaona anthuwo akugwira ntchito mogwirizana kenako anapita kukafunsa kuti adziwe kuti anthuwo anali ndani. Anadabwa kwambiri atadziwa kuti anthuwo ndi a Mboni za Yehova, ndipo anati: “Ndinkakuonani ngati anthu oipa.” Kodi kenako anachita chiyani? Anachotsa zimene analemba pakhomo pake zija.

10, 11. (a) Fotokozani zitsanzo zosonyeza kuti tikamagwira ntchito yothandiza anthu pa mavuto timawapatsa zimene akufunikira komanso kuchepetsa mavuto awo. (b) Kodi ndi kabuku kati komwe anthu othandiza anzawo pa nthawi ya mavuto amagwiritsa ntchito? (Onani bokosi lakuti, “ Kabuku Kothandiza Anthu Othandiza Anthu pa Nthawi ya Mavuto.”)

10 Chachiwiri, timapereka “zinthu zochuluka zimene [okhulupirira anzathu] akufunikira.” (2 Akor. 9:12a) Timafunitsitsa kuthandiza abale ndi alongo athu powapatsa zimene akufunikira komanso kuchepetsa mavuto awo. Timachita zimenezi chifukwa anthu a m’banja lachikhristu amapanga “thupi . . . limodzi” ndipo “chiwalo chimodzi chikavutika, ziwalo zina zonse zimavutikira nacho limodzi.” (1 Akor. 12:20, 26) Chikondi komanso chifundo chimene amakhala nacho pa abale awo, chimachititsa kuti abale ndi alongo ambiri masiku ano akamva kuti kwinakwake kwachitika masoka achilengedwe, nthawi yomweyo asiye zimene akuchita n’kupita kukathandiza okhulupirira anzawo a m’deralo. (Yak. 2:15, 16) Mwachitsanzo, m’chaka cha 2011, madzi atasefukira n’kuwononga kwambiri zinthu ku Japan, ofesi ya nthambi ya ku United States inatumiza kalata ku Makomiti Omanga Achigawo yopempha ngati pangapezeke “abale ochepa a luso” oti akathandize nawo ntchito yomanga Nyumba za Ufumu ku Japan. Patangopita nthawi yochepa, anthu pafupifupi 600 anadzipereka kuti akufuna kukathandiza ndipo anavomera kuti alipira okha ulendo wa pa ndege wopita kukagwira ntchitoyo. Ofesi ya nthambi ya ku United States inanena kuti: “Tinachita chidwi kwambiri kuona mmene abale anadziperekera.” M’bale wina wa ku Japan atafunsa munthu wina zimene zinam’chititsa kuti adzipereke kukagwira ntchitoyo, munthuyo anamuyankha kuti: “Abale athu a ku Japan timawaona ngati mbali ya thupi lathu. Akamavutika kapena kuzunzika, nafenso timamva kupweteka.” Chifukwa cha chikondi chololera kuvutikira ena, abale othandiza anzawo pa mavuto nthawi zina amaika moyo wawo pangozi kuti athandize okhulupirira anzawo. c​—1 Yoh. 3:16.

11 Nawonso anthu omwe si Mboni amayamikira ntchito yothandiza anthu amene ali pa mavuto imene timachita. Mwachitsanzo, ku Arkansas, ku America, kutachitika masoka achilengedwe mu 2013, nyuzipepala ina inalemba nkhani yoyamikira changu chimene a Mboni amene anakathandiza m’deralo anachita. Inanena kuti: “A Mboni za Yehova amene amathandiza anthu pa nthawi ya mavuto ali ndi dongosolo labwino moti amatha kuthandiza bwino kwambiri anthu amene ali pa mavutowo komanso mwachangu.” Izi zikusonyeza kuti, mogwirizana ndi mawu a Paulo, timapereka “zinthu zochuluka zimene [okhulupirira anzathu] akufunikira.”

12-14. (a) N’chifukwa chiyani kuthandiza anthu amene ali pa mavuto kuti ayambirenso kuchita zinthu zauzimu kuli kofunika kwambiri? (b) Kodi zimene anthu ena anena zikusonyeza bwanji kufunika kopitiriza kuchita zinthu zauzimu?

12 Chachitatu, timathandiza anthu amene ali pa mavutowo kuti ayambirenso kuchita zinthu zauzimu ngati kale. Kodi zimenezi n’zofunika bwanji? Paulo ananena kuti anthu amene adzathandizidwe pa nthawi yamavuto ‘adzayamika Mulungu.’ (2 Akor. 9:12b) Njira yabwino imene munthu wovutika angayamikire Yehova ndi kuyambiranso kuchita zinthu zauzimu mwamsanga. (Afil. 1:10) Nsanja ya Olonda ina imene inatuluka mu 1945 inanena kuti: “Paulo anavomereza . . . zoti Akhristu azitolera zopereka chifukwa chakuti zoperekazo zinkathandiza . . . Akhristu ovutika kuti apeze zinthu zofunika pa moyo wawo, zomwe zinkawathandiza kuti azigwira ntchito yochitira umboni za Yehova momasuka komanso mwamphamvu.” Masiku anonso cholinga chathu ndi chomwechi. Abale athu akayambiranso kugwira ntchito yolalikira, amalimbikitsa anthu ena omwe ali pa mavuto komanso amadzilimbitsa okha.​—Werengani 2 Akorinto 1:3, 4.

13 Tamvani zimene anthu ena ananena, omwe anathandizidwa atakumana ndi mavuto kenako n’kuyambiranso ntchito yolalikira yomwe inawalimbikitsa. M’bale wina anati: “Banja lathu linkaona kuti kulowa mu utumiki ndi dalitso chifukwa tikamalimbikitsa ena tinkaiwalako za mavuto athu.” Mlongo wina anati: “Kuchita zinthu zauzimu kunkandithandiza kuti ndisiye kuganizira za zinthu zomvetsa chisoni zimene zinali ponseponse. Zimenezi zinkandithandiza kuti mtima wanga ukhaleko m’malo.” Mlongo winanso anati: “Panali mavuto ambiri omwe tinkaona kuti palibe chimene tingachite kuti tiwapewe, koma utumiki unkalimbikitsa banja lathu. Tikamauza anthu ena za chiyembekezo chimene tili nacho choti Mulungu adzabweretsa dziko latsopano, tinkalimbitsa chikhulupiriro chathu choti zinthu zonse zidzakhala zatsopano.”

14 Kusonkhana ndi chinthu china chimene abale athu omwe akumana ndi mavuto amafunika kuyambiranso mwamsanga. Taganizirani zimene zinachitikira mlongo wina dzina lake Kiyoko ali ndi zaka pafupifupi 60. Katundu wake yense anawonongeka ndi madzi osefukira, moti anangopulumuka ndi zovala za m’thupi komanso masilipasi amene anavala ndipo anasoweratu mtengo wogwira. Kenako mkulu wina anamuuza kuti abale akhala ndi misonkhano yawo yachikhristu ya mlungu umenewo m’galimoto ya mkuluyo. Kiyoko anati: “M’galimotomo munangokhala ineyo, mkulu uja ndi mkazi wake komanso mlongo wina. Pamsonkhanowu panalibe zinthu zambiri koma zinali ngati kutulo kuona kuti msonkhanowu unandithandiza kuti ndisiye kuganiza za mavuto anga, moti mtima wanga unakhala m’malo. Msonkhano umenewu unandithandiza kudziwa kuti misonkhano yachikhristu ndi yamphamvu.” Pofotokoza za misonkhano imene anapita m’dera lawo mutachitika masoka achilengedwe, mlongo wina anati: “Inandithandiza kuti ndipirire.”​—Aroma 1:11, 12; 12:12.

Madalitso Amene Timapeza Chifukwa Cha Utumikiwu Ndi Osatha

15, 16. (a) Kodi Akhristu a ku Korinto ndi m’madera ena akanapeza madalitso otani chifukwa chothandiza anthu ena amene ali pa mavuto? (b) Kodi nafenso timadalitsidwa bwanji masiku ano chifukwa cha ntchitoyi?

15 Pofotokoza za utumiki wothandiza anthu pa nthawi ya mavuto, Paulo anauzanso Akorinto madalitso amene iwowo komanso Akhristu ena angapeze chifukwa chochita utumikiwu. Iye ananena kuti: “Iwo [Akhristu achiyuda a ku Yerusalemu amene munawatumizira thandizo] amakuperekerani mapembedzero kwa Mulungu ndiponso amakukondani kwambiri chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu wakusonyezani.” (2 Akor. 9:14) Kuwolowa manja kumene Akorinto anasonyeza kunachititsa kuti Akhristu achiyuda awapempherere komanso kuti apempherere Akhristu amitundu ina, ndipo zimenezi zinachititsa kuti Akorinto aziwakonda kwambiri Akhristu anzawowa.

16 Pofotokoza za madalitso amene timapeza masiku ano chifukwa chotsatira mawu a Paulo amenewa, Nsanja ya Olonda ya December 1, 1945, inanena kuti: “Tangoganizani mgwirizano umene umakhalapo gulu la anthu a Mulungu likapereka zinthu kuti lithandize abale awo amene ali pa mavuto.” Anthu amene akugwira ntchito yothandiza anzawo pa nthawi ya mavuto amaona kuti mawu amenewa ndi oona. M’bale wina, yemwe ndi mkulu ndipo anakathandizako kudera limene madzi anasefukira, ananena kuti: “Kuthandiza nawo pa nthawi ya mavutoyi kunathandiza kuti ndizikonda kwambiri abale kuposa kale.” Mlongo wina amene analandira thandizo pa nthawi ya mavuto ananena moyamikira kuti: “Ubale umene tili nawo ndi umboni wakuti tatsala pang’ono kulowa m’Paradaiso.”​—Werengani Miyambo 17:17.

17. (a) Kodi mawu omwe amapezeka pa Yesaya 41:13 amakwaniritsidwa bwanji anthu akakhala pa mavuto? (b) Fotokozani zitsanzo zosonyeza mmene ntchito yothandiza anthu imalemekezera Yehova komanso kulimbitsa ubale wathu. (Onaninso bokosi lakuti, “ Anthu Ongodzipereka Ochokera M’mayiko Osiyanasiyana Anagwira Ntchito Yothandiza Anthu.”)

17 Abale othandiza pa nthawi ya mavuto akafika kumene kwachitika masoka a chilengedwe, abale amene akhudzidwa ndi vutolo amaona okha umboni wa zimene Mulungu analonjeza kuti: “Ine, Yehova Mulungu wako, ndagwira dzanja lako lamanja. Ine amene ndikukuuza kuti, ‘Usachite mantha. Ineyo ndikuthandiza.’” (Yes. 41:13) Mlongo wina atapulumuka pa masoka achilengedwe amene anachitika, ananena kuti: “Nditaona mmene zinthu zinawonongekera ndinasowa mtengo wogwira koma Yehova anandigwira dzanja. Abale anandithandiza kwambiri moti ndilibe chonena.” Dera linalake kutachitika chivomezi, abale awiri a m’deralo omwe ndi akulu analemba kalata m’malo mwa mipingo yawo. Kalatayi inali yoyamikira mmene abale anawathandizira. Iwo anati: “Ngakhale kuti chivomezichi chinatichititsa kukhala pa mavuto aakulu, tinaona Yehova akutithandiza kudzera mwa abale. Tinkawerenga nkhani zofotokoza mmene abale amathandizirana pa nthawi ya mavuto koma panopa tadzionera tokha ndi maso athu.”

Inunso Mukhoza Kuthandiza Nawo

18. Kodi muyenera kuchita chiyani ngati mukufuna kugwira nawo ntchito yothandiza anthu pa nthawi ya mavuto? (Onaninso bokosi lakuti, “ Ntchito Yothandiza Anthu Inasintha Moyo Wake.”)

18 Kodi nanunso mukufuna kuti muzisangalala chifukwa chogwira ntchito yothandiza anthu amene ali pa mavuto? Ngati ndi choncho dziwani kuti anthu okagwira ntchito zimenezi nthawi zambiri amasankhidwa kuchokera m’gulu la abale ndi alongo amene amagwira ntchito yomanga Nyumba za Ufumu. Mungawauze akulu a mumpingo mwanu kuti mukufuna akupatseni fomu yofunsira utumiki umenewu. M’bale wina yemwe ndi mkulu ndipo wakhala akugwira ntchito yothandiza anthu kwa nthawi yaitali, ananena kuti: “Muzipita kukathandiza kudera limene kuli mavutoko pokhapokha ngati mwalandira kalata yokuitanani yochokera ku Komiti Yopereka Chithandizo.” Zimenezi zingachititse kuti ntchito yathu yothandiza anthu pa nthawi ya mavuto ipitirizebe kuyenda mwadongosolo.

19. Kodi anthu amene amagwira ntchito yothandiza anthu pa nthawi ya mavuto amasonyeza bwanji kuti ndi ophunzira a Khristu enieni?

19 Ntchito yothandiza anthu ndi njira yabwino yosonyezera kuti timatsatira lamulo la Khristu lakuti ‘tizikondana.’ Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti ndifedi ophunzira a Khristu. (Yoh. 13:34, 35) Panopa ndife odala chifukwa pali anthu ambiri amene amalemekeza Yehova podzipereka kukathandiza abale awo omwe amatumikira Ufumu wa Mulungu mokhulupirika.

a Mu nkhaniyi tikambirana za ntchito yothandiza okhulupirira anzathu amene ali pa mavuto. Komabe, nthawi zambiri timathandizanso anthu ena omwe si Mboni.​—Agal. 6:10.

b Paulo anagwiritsira ntchito mawu akuti di·aʹko·nos (mtumiki) pamene ankafotokoza za “atumiki othandiza.”​—1 Tim. 3:12.

c Onani nkhani yakuti “Kuthandiza Banja Lathu la Chikhulupiriro mu Bosnia,” mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 1994, tsamba 23-27.