GAWO 6
Thandizo Limene Ufumu Umapereka—Kumanga Malo Olambirira Komanso Kuthandiza pa Nthawi ya Mavuto
TAYEREKEZERANI kuti mwalowa mu Nyumba ya Ufumu yanu koma n’kupeza kuti chilichonse chasinthiratu. Mwakhala mukunyadira chifukwa chokhala ndi nyumba imeneyi ndipo mwina mumakumbukira zinthu zina zosangalatsa zimene zinkachitika pa nthawi imene munkagwira nawo ntchito yomanga nyumbayo. Koma panopa ndinu osangalala kwambiri chifukwa chakuti Nyumba ya Ufumuyo yasintha n’kukhala malo othandizirako anthu pa nthawi ya mavuto. Chifukwa cha mvula ya mphepo yomwe yachititsa kuti madzi asefukire m’dera lanulo, Komiti ya Nthambi yakonza zoti anthu amene akhudzidwa ndi vutoli alandire chakudya, zovala, madzi ndiponso zinthu zina. Katunduyo akusanjidwa mwadongosolo ndipo abale ndi alongo akubwera mu Nyumba ya Ufumuyo kudzalandira zinthu zofunikira kwinaku akutuluka misozi yachisangalalo.
Yesu ananena kuti anthu ake azidzadziwika chifukwa chokondana. (Yoh. 13:34, 35) M’chigawochi tikambirana mmene Mboni za Yehova zimasonyezerana chikondi chimenechi pa ntchito zomangamanga komanso kuthandizana pa nthawi ya mavuto. Kusonyezana chikondi kumeneku ndi umboni wakuti Ufumu wa Khristu ukulamulira.
M'CHIGAWO ICHI
MUTU 18
Mmene Timapezera Ndalama Zoyendetsera Ntchito za Ufumu
Kodi ndalama zimene amagwiritsa ntchito zimachokera kuti? Kodi ndalamazo zimagwira ntchito yanji?
MUTU 19
Ntchito Yomanga Yomwe Imalemekeza Yehova
Malo olambirira amalemekeza Mulungu, koma pali chinthu china chomwe Mulungu amachiona kuti n’chamtengo wapatali kwambiri.
MUTU 20
Utumiki Wothandiza Anthu pa Nthawi ya Mavuto
Kodi timadziwa bwanji ntchito yothandiza anthu ndi mbali ya utumiki wopatulika kwa Yehova?