MUTU 5
Mfumu Inathandiza Anthu Kudziwa Bwino za Ufumu
1, 2. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ndi wotsogolera wanzeru?
TAYEREKEZERANI kuti mwapita kukaona mzinda winawake wokongola komanso wochititsa chidwi ndipo munthu wodziwa bwino ntchito yosonyeza anthu malo akukutsogolerani. Inuyo komanso anthu ena onse amene muli nawo pagulupo n’koyamba kupita kumzindawo moti mukumvetsera mwachidwi zimene wokutsogoleraniyo akufotokoza. Nthawi zina, inuyo komanso anthu ena pagululo mukumakhala ndi chidwi chofuna kumva za zinthu zina zomwe zili mumzindawo koma zoti malo ake simunafike. Koma mukafunsa yemwe akukutsogoleraniyo za zinthu zimenezi, sakufotokoza zambiri mpaka pa nthawi yake yoyenera ndipo nthawi zambiri akumakufotokozerani mukafika pomwe pali chinthu chimene mumafunsacho. M’kupita kwa nthawi, mukuyamba kugoma ndi nzeru zake chifukwa akumakufotokozerani chinthu chilichonse pa nthawi yoyenerera.
2 Zimene zimachitika kwa Akhristu n’zofanana ndi zimene zimachitika kwa anthu amene apita kukaona malo achilendo. Akhristufe tikuphunzira mwachidwi za mzinda wokongola kwambiri kuposa mizinda yonse. Mzinda umenewu ndi Ufumu wa Mulungu ndipo uli ndi “maziko enieni.” (Aheb. 11:10) Yesu ali padziko lapansi anakhala ngati wotsogolera anthu poona malo ndipo anathandiza otsatira ake kuti adziwe zambiri za Ufumuwu. Kodi Yesu anayankha kamodzin’kamodzi mafunso onse amene otsatira ake anali nawo ndiponso kuwauza zonse zokhudza Ufumuwu? Ayi. Iye anati: “Ndili ndi zambiri zakuti ndikuuzeni, koma padakali pano simungathe kuzimvetsa zonsezo.” (Yoh. 16:12) Popeza Yesu ndi wanzeru kwambiri kuposa anthu onse amene amatsogolera anthu, sanafune kusokoneza ophunzira ake ndi mfundo zomwe sakanatha kuzimvetsa pa nthawiyo.
3, 4. (a) Kodi Yesu anapitiriza bwanji kuphunzitsa anthu okhulupirika zinthu zokhudza Ufumu wa Mulungu? (b) Kodi tikambirana chiyani m’mutu uno?
3 Yesu ananena mawu amene ali palemba la Yohane 16:12 usiku womaliza wa moyo wake wa padziko lapansi. Koma kodi akanapitiriza bwanji kuphunzitsa anthu okhulupirika zinthu zokhudza Ufumu wa Mulungu pambuyo pa imfa yake? Iye anatsimikizira atumwi ake kuti: ‘Mzimu wa choonadi, udzakutsogolerani m’choonadi chonse.’ a (Yoh. 16:13) Mzimu woyera uli ngati munthu wotsogolera anthu odzaona malo yemwe safotokoza zinthu zambirimbiri nthawi imodzi. Yesu amagwiritsa ntchito mzimuwu pophunzitsa otsatira ake zinthu zimene akufunikira kudziwa pa nkhani ya Ufumu wa Mulungu ndipo amawafotokozera zinthuzo pa nthawi yomwe akufunikira kuzidziwa.
4 Tiyeni tione mmene mzimu woyera wa Yehova wakhala ukuthandizira Akhristu oona kuti adziwe mfundo zambiri zokhudza Ufumuwu. Choyamba, tiona chimene chinatithandiza kudziwa nthawi yomwe Ufumuwu unayamba kulamulira. Kenako, tikambirana mmene tingadziwire anthu amene adzalamulire nawo mu Ufumuwo komanso anthu omwe adzakhale nzika zake. Pomaliza, tiona zimene zinathandiza otsatira a Khristu kudziwa zoyenera kuchita kuti asonyeze kuti ndi okhulupirika ku Ufumuwu.
Anazindikira Chaka Chapadera
5, 6. (a) Kodi Ophunzira Baibulo anali ndi maganizo olakwika ati pa nkhani ya kukhazikitsidwa kwa Ufumu komanso pa nkhani yokolola? (b) Kodi tinganene kuti Yesu sankatsogolera otsatira ake chifukwa chakuti anali ndi maganizo olakwikawa?
5 Monga mmene tinaonera m’Mutu 2 wa bukuli, kudakali zaka zambiri kuti chaka cha 1914 chifike, Ophunzira Baibulo anakhala akunena kuti chaka chimenechi chidzakhala chapadera kwambiri pa kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’Baibulo. Koma pa nthawi imeneyi sankamvetsa mfundo zina molondola. Mwachitsanzo, ankakhulupirira kuti Khristu anayamba kukhalapo m’chaka cha 1874 ndipo anayamba kulamulira kumwamba m’chaka cha 1878. Ankakhulupiriranso kuti Ufumu wa Mulungu sudzayamba kugwira ntchito zonse bwinobwino mpaka mu October 1914. Ankakhulupiriranso kuti ntchito yokolola idzachitika kuyambira mu 1874 mpaka mu 1914 ndipo idzatha odzozedwa akadzatengedwa kupita kumwamba. Kodi tinganene kuti Yesu sankatsogolera anthu okhulupirika amenewa ndi mzimu wake woyera chifukwa chakuti sanamvetse bwino mfundo zimenezi?
6 Ayi ndithu. Taganizirani za chitsanzo chimene chili kumayambiriro kwa mutuwu. Kodi anthu odzaona malowo angayambe kukayikira munthu amene akuwatsogolerayo chifukwa chakuti sakuwafotokozera zinthu pa nthawi imene iwo akufuna? Ayi. Mofanana ndi zimenezi, nthawi zina anthu a Mulungu amafuna kumvetsa mfundo zina zokhudza chifuniro cha Yehova pamene si nthawi ya Yehova yoti aulule zinthuzo, koma Yesu akuwatsogolerabe. Ndiyeno mzimu woyera ukawathandiza kumvetsa mfundozo molondola, atumiki okhulupirikawa amakhala okonzeka kusintha.—Yak. 4:6.
7. Kodi anthu a Mulungu anamvetsa mfundo ziti za choonadi?
7 Chaka cha 1919 chitadutsa, atumiki a Mulungu anayamba kumvetsa bwino mfundo za choonadi. (Werengani Salimo 97:11.) Mu chaka cha 1925, mu Nsanja ya Olonda munatuluka nkhani yapadera kwambiri yakuti, “Kubadwa kwa Mtundu.” Nkhaniyi inafotokoza momveka bwino kuti Ufumu wa Mesiya unabadwa m’chaka cha 1914. Zimenezi zinakwaniritsa ulosi womwe unalembedwa m’chaputala 12 cha buku la Chivumbulutso, womwe unafotokoza za mkazi wakumwamba wa Mulungu yemwe anabereka mwana. b Nkhaniyi inafotokozanso kuti kuzunzidwa komanso mavuto amene anthu a Yehova anakumana nawo m’nthawi ya nkhondo, unali umboni wakuti Satana anali atagwetsedwa kuchokera kumwamba ndipo anali “ndi mkwiyo waukulu podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.”—Chiv. 12:12.
8, 9. (a) Kodi anthu a Mulungu anadziwa bwanji kuti nkhani ya Ufumu ndi yofunika kwambiri? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?
8 Ufumuwu ndi wofunika kwambiri moti mu 1928, magazini ya Nsanja ya Olonda inanena momveka bwino kuti aliyense ayenera kuona kuti Ufumuwu ndi wofunika kwambiri kuposa kupulumutsidwa. Ndipotu Yehova adzagwiritsa ntchito Ufumu wolamuliridwa ndi Mesiya kuti ayeretse dzina lake, atsimikizire kuti iye ndi amene ali woyenera kulamulira komanso kukwaniritsa zolinga zake zonse zokhudza anthu.
9 Kodi ndani amene adzalamulire ndi Khristu mu Ufumu umenewu? Nanga ndani adzakhale nzika za Ufumu umenewu padziko lapansi? Kodi otsatira a Khristu ayenera kugwira ntchito yotani?
Ntchito Yokolola Kwenikweni Inali Yosonkhanitsa Odzozedwa
10. Kuyambira kale, kodi anthu a Mulungu akhala akukhulupirira zotani zonena za a 144,000?
10 Kudakali zaka zambiri chaka cha 1914 chisanafike, Akhristu oona anali akudziwa kale kuti anthu okhulupirika okwana 144,000 adzalamulira ndi Khristu kumwamba. c Ophunzira Baibulowa anadziwa kuti chiwerengero chimenechi ndi chenicheni komanso kuti chinayamba kusonkhanitsidwa m’nthawi ya atumwi.
11. Kodi omwe ali m’gulu la mkwatibwi wa Khristu anazindikira kuti ayenera kugwira ntchito yotani adakali padziko lapansi?
11 Ndiye kodi anthu amenewa, omwe ali m’gulu la mkwatibwi wa Khristu, anayenera kugwira ntchito yotani adakali padziko lapansi? Ophunzira Baibulo anazindikira kuti Yesu analimbikitsa kwambiri ntchito yolalikira ndipo anaiyerekezera ndi nthawi yokolola. (Mat. 9:37; Yoh. 4:35) Monga tinaonera m’Mutu 2, kwa nthawi yaitali Ophunzira Baibulowa ankakhulupirira kuti ntchito yokololayi idzatenga zaka 40 ndipo idzatha odzozedwa akadzapita kumwamba. Koma chifukwa chakuti zaka 40 zitatha ntchitoyi inapitirirabe, anafunika kusintha zimene ankakhulupirira. Panopa tikudziwa kuti nthawi yokolola inayamba mu 1914. Nthawi imeneyi ndi yosiyanitsa tirigu ndi namsongole. Tirigu akuimira Akhristu odzozedwa okhulupirika ndipo namsongole akuimira Akhristu onyenga. Tsopano nthawi inali itakwana yoti asonkhanitse Akhristu odzozedwa amene anali adakali padziko lapansi.
12, 13. Kodi mafanizo a Yesu onena za anamwali 10 ndi matalente akwaniritsidwa bwanji m’masiku otsiriza ano?
12 Kuyambira m’chaka cha 1919 kupita m’tsogolo, Khristu anatsogolera kapolo wokhulupirika ndi wanzeru kulimbikitsa anthu kuti azigwira ntchito yolalikira. Iye anachita zimenezi pa nthawi imene anali padziko lapansi. (Mat. 28:19, 20) Ananenanso za makhalidwe amene otsatira ake odzozedwa ayenera kukhala nawo kuti akwanitse kugwira ntchito yolalikirayi. M’fanizo la anamwali 10, Yesu anasonyeza kuti odzozedwa adzafunika kukhala maso mwauzimu kuti adzakwanitse kukakhala nawo paphwando la ukwati kumwamba, pamene Khristu adzakumane ndi “mkwatibwi” wake, yemwe akuimira odzozedwa okwana 144, 000. (Chiv. 21:2) Kenako m’fanizo lake la matalente, Yesu anasonyezanso kuti odzozedwa adzachita khama pogwira ntchito yolalikira imene anawapatsa.—Mat. 25:1-30.
13 Pa zaka 100 zapitazi, Akhristu odzozedwa asonyezadi kuti akhala ali maso komanso akhala akugwira ntchito yolalikira mwakhama. Sitikukayikira kuti adzadalitsidwa chifukwa chokhala maso. Koma kodi ntchito yokolola inali yongosonkhanitsa Akhristu okwana 144,000 omwe akalamulire ndi Khristu kumwamba?
Ufumuwo Unayamba Kusonkhanitsa Nzika Zake Zapadziko Lapansi
14, 15. Kodi buku la mutu wakuti The Finished Mystery linafotokoza magulu 4 ati a anthu?
14 Anthu okhulupirika akhala akufuna kumvetsa kuti “khamu lalikulu” lotchulidwa pa Chivumbulutso 7:9-14 likuimira ndani. Panopo timadziwa komanso kumvetsa bwino za khamu lalikulu. Koma poyamba, Ophunzira Baibulo anali ndi maganizo osiyana ndi zimene tikudziwa panopo. Iwo anali ndi maganizo amenewo chifukwa siinali nthawi yoti Khristu aulule kuti khamu lalikulu likuimira ndani.
15 Mu 1917, buku la mutu wakuti, “The Finished Mystery” linanena kuti pali “magulu awiri a anthu odzapita kumwamba komanso pali magulu awiri a anthu omwe adzakhale padziko lapansi.” Kodi magulu 4 amenewa anapangidwa ndi anthu ati? Ponena za magulu awiri opita kumwamba, gulu loyamba linali la anthu okwana 144,000 amene akalamulire ndi Khristu. Gulu lachiwiri linali khamu lalikulu. Nthawi imeneyo ankakhulupirira kuti khamu lalikulu ndi Akhristu amene anali adakali m’matchalitchi amene amati ndi achikhristu. Ankakhulupirira kuti anthu amenewa anali ndi chikhulupiriro ndithu koma chinali chosakwanira kuti azichita zinthu zonse mokhulupirika. Chifukwa cha zimenezi, ankakhulupirira kuti Akhristu amenewa akakhala ndi malo otsikirapo kumwamba. Ponena za magulu awiri apadziko lapansi, ankakhulupirira kuti gulu lina linapangidwa ndi anthu okhulupirika akale omwe adzakhale ndi maudindo akuluakulu. Anthu amenewa ndi monga Abulahamu, Mose ndi ena. Kenako ankakhulupirira kuti palinso gulu lina lopangidwa ndi anthu wamba omwe azidzalamuliridwa ndi anthu okhulupirika akalewa.
16. Kodi Ophunzira Baibulo anayamba kumvetsa mfundo za choonadi ziti m’chaka cha 1923 ndi 1932?
16 Koma kodi mzimu woyera unathandiza bwanji otsatira a Khristu kuyamba kumvetsa molondola mfundo za choonadi pa nkhani imeneyi? Kuwala kwauzimu kunayamba pang’onopang’ono. Kuyambira m’chaka cha 1923, Nsanja ya Olonda inafotokoza za gulu la anthu amene anali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi n’kumalamuliridwa ndi Khristu. M’chaka cha 1932, Nsanja ya Olonda inafotokoza za Yonadabu (Yehonadabu), amene anagwirizana ndi Mfumu Yehu yachiisiraeli pomenya nkhondo yothetsa kulambira konyenga. (2 Maf. 10:15-17) Magaziniyi inafotokoza kuti pali gulu lina la anthu amene ali ngati Yonadabu. Inawonjezeranso kuti Yehova adzapulumutsa gulu limeneli “pa nthawi ya Aramagedo” ndipo lidzakhala ndi moyo padziko lapansi.
17. (a) Kodi Ophunzira Baibulo anamvetsa mfundo yosangalatsa iti mu 1935? (b) Kodi Akhristu okhulupirika anamva bwanji atamvetsa bwino za khamu lalikulu? (Onani bokosi lakuti, “ Mitima Yathu Inakhala M’malo.”)
17 Kenako m’chaka cha 1935, abale anamvetsa bwino mfundo ya choonadi imeneyi. Pa msonkhano wachigawo womwe unachitikira ku Washington, D.C., zinadziwika kuti khamu lalikulu ndi gulu la anthu amene adzakhale padziko lapansi. Amenewa ndi anthu angati nkhosa omwe Yesu anawafotokoza m’fanizo lake la nkhosa ndi mbuzi. (Mat. 25:33-40) Khamu lalikululi ndi gulu la “nkhosa zina” zomwe Yesu ananena kuti: “Zimenezonso ndiyenera kuzibweretsa.” (Yoh. 10:16) Pa msonkhanowo, M’bale J. F. Rutherford ananena kuti: “Onse amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo kosatha padziko lapansi aimirire.” Zitatero, pafupifupi hafu ya anthu amene anasonkhana anaimirira. Kenako ananenanso kuti: “Taonani khamu lalikulu.” Anthu ambiri anasangalala kuti anamvetsa bwino zoti ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi.
18. Kodi n’chiyani chathandiza otsatira a Khristu kugwira ntchito yolalikira mwakhama ndipo pakhala zotsatirapo zotani?
18 Kuyambira nthawi imeneyo, Khristu wakhala akuthandiza anthu ake pa ntchito yosonkhanitsa anthu amene akupanga khamu lalikulu. Anthu amenewa ndi amene adzapulumuke pa chisautso chachikulu. Poyamba ntchito yosonkhanitsayi inkaoneka ngati siiyenda bwino. Moti nthawi ina M’bale Rutherford ananena kuti: “Zikuoneka kuti ‘khamu lalikulu’ silikhala lalikulu ngati mmene timaganizira.” Koma panopo tikudziwa mmene Yehova wadalitsira ntchito yokololayi. Pogwiritsa ntchito mzimu woyera, Yesu wakhala akutsogolera odzozedwa komanso a “nkhosa zina” ndipo amachita zinthu ngati “gulu limodzi” lomwe likutsogoleredwa ndi “m’busa mmodzi.”
19. Kodi tingatani kuti tithandize nawo kuwonjezera khamu lalikulu?
19 Gulu lalikulu la anthu okhulupirika lidzakhala ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi ndipo azidzalamuliridwa ndi Khristu pamodzi ndi a 144,000. Kunena zoona, n’zolimbikitsa kwambiri kuganizira mmene Khristu wakhala akuthandizira anthu a Mulungu kumvetsa bwino chiyembekezo chimenechi. Ndipotu ndi mwayi waukulu kugwira nawo ntchito youza anthu ena za chiyembekezo chimenechi. Choncho, tiyeni tiziyesetsa kulalikira mmene tingathere kuti khamu lalikulu lipitirize kukula. Zimenezi zingachititse kuti dzina la Yehova lilemekezedwe kwambiri.—Werengani Luka 10:2.
Zimene Anthu Okhulupirika ku Ufumuwu Ayenera Kuchita
20. (a) Kodi gulu la Satana lapangidwa ndi anthu ati? (b) Kodi Akhristu ayenera kuchita chiyani kuti apitirize kukhala okhulupirika ku Ufumu wa Mulungu?
20 Pamene atumiki a Mulungu ankapitiriza kuphunzira za Ufumu, ankafunikanso kumvetsa kuti kukhala wokhulupirika ku Ufumuwo kumatanthauza chiyani. Pofotokoza mfundo imeneyi, Nsanja ya Olonda imene inatuluka m’chaka cha 1922, inafotokoza kuti pali magulu awiri amene munthu angasankhe. Pali gulu la Yehova komanso gulu la Satana ndipo gulu la Satana lapangidwa ndi anthu amalonda, achipembedzo komanso andale. Anthu amene ali okhulupirika ku Ufumu wa Mulungu wolamuliridwa ndi Khristu, sayenera kuchita chilichonse chogwirizana ndi anthu omwe ali kumbali ya Satana chifukwa zingasokoneze kukhulupirika kwawo ku gulu la Yehova. (2 Akor. 6:17) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?
21. (a) Kodi kapolo wokhulupirika wakhala akuchita chiyani pofuna kuchenjeza anthu pa nkhani ya malonda? (b) Kodi Nsanja ya Olonda yomwe inatuluka mu 1963 inafotokoza chiyani za “Babulo Wamkulu”?
21 Mabuku amene kapolo wokhulupirika amatipatsa akhala akuulula za chinyengo chimene anthu amalonda amachita ndipo akhala akuchenjeza anthu a Mulungu kuti asakopeke ndi moyo wokonda chuma. (Mat. 6:24) Mabukuwa akhala akuululanso za zipembedzo zomwe zili kumbali ya Satana. Mwachitsanzo m’chaka cha 1963, Nsanja ya Olonda inafotokoza momveka bwino kuti “Babulo Wamkulu” samangotanthauza matchalitchi amene amati ndi achikhristu okha, komanso amatanthauza zipembedzo zonse zonyenga. Choncho, monga mmene tidzaonere m’Mutu 10, anthu a Mulungu a mitundu yosiyanasiyana komanso ochokera m’mayiko onse athandizidwa ‘kutuluka’ m’Babulo Wamkulu komanso kusiya miyambo yake yonse.—Chiv. 18:2, 4.
22. Pa nthawi ya nkhondo yoyamba yapadziko lonse, kodi anthu a Mulungu ankamva bwanji lemba la Aroma 13:1?
22 Bwanji nanga pa nkhani ya zandale? Kodi Akhristu oona ankayenera kumenya nawo nkhondo kapena kulowerera nawo m’mikangano ya mayiko? Pa nthawi ya nkhondo yoyamba yapadziko lonse, Ophunzira Baibulo ankaona kuti Akhristu sayenera kupha munthu. (Mat. 26:52) Komabe, Ophunzira Baibulo ambiri ankakhulupirira kuti potsatira malangizo omwe amapezeka pa Aroma 13:1, omwe amati tizimvera “olamulira akuluakulu,” akhoza kulowa usilikali, kuvala yunifomu ya asilikali ndiponso kugwira mfuti. Koma olamulirawo akawauza kuti awombere munthu ankayenera kuwombera m’mwamba.
23, 24. Pa nthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse, kodi otsatira a Khristu ankamva bwanji lemba la Aroma 13:1, ndipo anathandizidwa bwanji kuti ayambe kumvetsa lembali molondola?
23 Pamene nkhondo yachiwiri yapadziko lonse inkayamba m’chaka cha 1939, Nsanja ya Olonda inafotokoza momveka bwino kwambiri nkhani ya kusalowerera nawo ndale. Nkhaniyi inanena kuti Akhristu sayenera kulowerera nkhondo ndiponso mikangano imene imachitika m’dziko la Satanali. Malangizowa anafika pa nthawi yake chifukwa anateteza Akhristu kuti asakhale ndi mlandu wamagazi umene mayiko amene ankachita nkhondoyi anali nawo. Koma kuyambira m’chaka cha 1929, mabuku athu ankafotokoza kuti olamulira akuluakulu amene anatchulidwa pa Aroma 13:1 sakuimira olamulira dzikoli koma akuimira Yehova ndi Yesu. Apa n’kuti asanamvetsebe molondola zimene lembali limatanthauza ndipo anafunika kulimvetsa bwino.
24 Patapita nthawi mzimu woyera unathandiza otsatira a Khristu kumvetsa lemba la Aroma 13:1-7 kuchokera m’nkhani zomwe zinatuluka mu Nsanja ya Olonda ya November 15 ndi December 1, 1962. Nkhanizi zinathandiza anthu a Mulungu kumvetsa mfundo, yoti tizigonjera maulamuliro, imene Yesu ananena kuti: “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu kwa Mulungu.” (Luka 20:25) Panopa Akhristu oona amadziwa kuti olamulira akuluakulu amaimira anthu amene akulamulira dzikoli ndipo Akhristuwo ayenera kuwamvera. Koma pa nkhani yomvera olamulirawa Akhristu ali ndi malire. Ngati olamulirawa akutiuza kuti tichite zinthu zimene Yehova Mulungu amadana nazo, timayankha ngati mmene atumwi anayankhira kuti: “Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.” (Mac. 5:29) M’mutu 13 ndi 14, tidzaphunzira zimene Akhristu achita kuti asamalowerere nkhani zandale.
25. Kodi ndi zinthu ziti zimene mzimu woyera watithandiza kumvetsa molondola zokhudza Ufumu wa Mulungu?
25 Ndiyeno taganizirani zinthu zambiri zonena za Ufumu zimene otsatira a Khristu akhala akuphunzira pa zaka 100 zapitazi. Taphunzira kuti Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa liti kumwamba komanso kufunika kwa Ufumuwu. Tikumvetsa bwino kuti pali magulu awiri a anthu okhulupirika. Gulu loyamba lili ndi chiyembekezo chodzapita kumwamba ndipo gulu linalo lili ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi. Panopo tikudziwa zimene tiyenera kuchita kuti tisonyeze kuti ndife okhulupirika ku Ufumu wa Mulungu. Tikudziwanso zimene tiyenera kuchita pa nkhani yomvera olamulira a m’dzikoli. Ndiyeno dzifunseni kuti, ‘Kodi ndikanadziwa mfundo zamtengo wapatali zimenezi akanakhala kuti Yesu Khristu sanatsogolere kapolo wake wokhulupirika kuti amvetse ndi kuphunzitsa mfundo zimenezi?’ Kunena zoona, ndife odala chifukwa chakuti Khristu akutitsogolera pogwiritsa ntchito mzimu woyera.
a Buku lina linanena kuti mawu achigiriki amene anawamasulira kuti ‘kutsogolera’ pa vesili amatanthauza “kusonyeza njira.”
b Kale, Ophunzira Baibulo ankakhulupirira kuti masomphenyawa ankanena za nkhondo yapakati pa tchalitchi cha Katolika ndi anthu a ku Roma omwe sanali Akatolika.
c M’mwezi wa June, chaka cha 1880, magazini ya Zion’s Watch Tower inafotokoza kuti a 144,000 adzakhala anthu ochokera mu mtundu wachiyuda okha amene adzaphunzire choonadi pofika mu 1914. Koma chakumapeto kwa chaka cha 1880, panatulukanso nkhani ina imene inasintha zomwe ankakhulupirirazo ndipo inafotokoza zofananako ndi zimene timakhulupirira masiku ano.