NKHANI 66
Yezebeli—Mkazi Woipa wa Mfumu
ATAFA Mfumu Yerobiamu, mfumu iri yonse imene ikulamulira ufumu wakumpoto wa mafuko 10 a Israyeli njoipa. Mfumu Ahabu ndiye anali woipitsitsa. Kodi mukudziwa chifukwa chake? Chifukwa chimodzi chachikulu ndicho mkazi wake, Mkazi woipa wa Mfumu Yezebeli.
Yezebeli si mkazi Wachiisrayeli. Iye ndi mwana wamkazi wa mfumu ya Sidoni. Iye amalambira mulungu wonyenga Baala, ndipo akuchititsa Ahabu ndi Aisrayeli ambiri kulambira’nso Baala. Yezebeli amada Yehova ndipo akupha aneneri ake ambiri. Ena anafunikira kubisala m’mapanga kuti asaphedwe. Yezebeli akafuna kanthu kena, iye angangopha munthu kuti achipeze.
Tsiku lina Mfumu Ahabu wakwiya kwambiri. Chotero Yezebeli akum’funsa kuti: ‘Kodi wakwiyiranji lero?’
‘Chifukwa cha zimene Naboti wandiuza,’ akutero Ahabu. ‘Ndinafuna kugula munda wake wamphesa. Koma iye anati sindingaugule.’
Yezebeli akuti, ‘Usabvutike, ndidzakupezera ndine.’
Chotero Yezebeli akulembera makalata kwa akalonga ena a mu mzinda umene Naboti’yu amakhala. ‘Pezani anthu ena oipa oti anamizire Naboti kuti anatukwana Mulungu ndi mfumu,’ iye akuwauza motero. ‘Ndiyeno m’tulutsireni kunja kwa mzinda ndi kum’ponya miyala mpaka atafa.’
Pamene angomva kuti Naboti wafa, iye akuti kwa Ahabu: ‘Tsopano pita katenge munda wake wamphesa.’ Kodi simubvomereza kuti Yezebeli ayenera kulangidwa chifukwa cha kuchita chinthu choopsya’chi?
Chotero, m’nthawi yake, Yehova akutumiza Yehu kukam’langa. Pakumva Yezebeli kuti Yehu akudza, akulocha maso ake ndi kuyesa kudzikonza kuti aoneke kukhala wokongola. Koma pakudza Yehu ndi kuona Yezebeli pa zenera, iye akuitana amuna okhala m’mphala’yo nati: ‘Mponyereni pansi!’ Amuna’wo akumvera, monga momwe mukuonera m’chithunzi’cho. Akum’ponyera pansi, nafa. Ndiwo mapeto a Yezebeli woipa’yo.