NKHANI 64
Solomo Amanga Kachisi
DAVIDE asanafe, anapatsa Solomo malinganizidwe a kamangidwe ochokera kwa Mulungu a kachisi wa Yehova. M’chaka chachinai cha ulamuliro wake, iye akuyamba kumanga kachisi’yo, ndipo kukutenga zaka zisanu ndi ziwiri kum’maliza. Amuna zikwi makumi ochuluka akugwira ntchito pa kachisi, ndipo nyumba’yo ikudya ndalama zochuluka kwambiri. Izi ziri choncho chifukwa chakuti golidi ndi siliva zochuluka zikugwiritsiridwapo ntchito.
Kachisi’yo ali ndi zipinda zazikulu ziwiri, monga momwe chinaliri chihema. Koma zipinda’zi ziri zowirikiza ukulu wa za chihema. Solomo akuchititsa likasa la chipangano kuikidwa m’chipinda cha m’kati-kati, ndipo zinthu zina zimene zinalikusungidwa m’chihema zikuikidwa m’china’cho.
Pamene kachisi’yo atha, pali madyerero akulu. Solomo akugwada patsogolo pa kachisi’yo napemphera, monga momwe mukuonera m’chithunzi’chi. ‘Ngakhale kumwamba kweni-kweni’ko simungakwane’ko,’ akutero Solomo kwa Yehova, ‘koposa kotani nanga, kachisi uyu. Koma, O Mulungu wanga, chonde mverani anthu anu popemphera ataloza ku malo kuno.’
Pamene atsiriza pemphero lake, ukutsika moto kuchokera kumwamba. Ukuocha nyama za nsembe’zo. Ndipo kuunika kowala kochokera kwa Yehova kukudzaza kachisi’yo. Izi zikusonyeza kuti Yehova akumvetsera, n’kuti akukondwera naye kachisi’yo ndi pemphero la Solomo. Kachisi’yo, m’malo mwa chihema, tsopano akukhala malo kumene anthu’wo akudza kudzalambira.
Kwa nthawi yaitali Solomo akulamulira mwanzeru, ndipo anthu nakhala achimwemwe. Koma Solomo akukwatira akazi ambiri a ku maiko ena osalambira Yehova. Kodi mukuona mmodzi wa iwo akulambira fano? Potsiriza akazi ake akupangitsa Solomo naye’nso kulambira milungu ina. Kodi mukudziwa chimene chikuchitika pamene Solomo achita izi? Iye sakuchitira’nso anthu’wo mokomo mtima. Iye akukhala wankhanza, ndipo anthu’wo sali’nso achimwemwe.
Izi zikukwiyitsa Yehova, ndipo akumuuza kuti: ‘Ndidzakuchotsera ufumu ndi kuupatsa kwa munthu wina. Sindidzachita izi m’nthawi ya moyo wako, koma m’kulamulira kwa mwanako. Koma sindidzachotsa anthu onse a ufumu’wo kwa mwanako. Tiyeni tione m’mene zikuchitikira.