Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHIGAWO 4

Mfumu Yoyamba ya Israyeli Mpaka pa Ukapolo Ku Babulo

Mfumu Yoyamba ya Israyeli Mpaka pa Ukapolo Ku Babulo

Sauli anakhala mfumu yoyamba ya Israyeli. Koma Yehova anam’kana, ndipo Davide anasankhidwa kukhala mfumu m’malo mwake. Timapeza zinthu zochuluka zonena za Davide. Monga mnyamata, iye anamenyana ndi chimphona’cho Goliati. Kenako anathawa mfumu yansanje’yo Sauli. Ndiyeno Abigayeli wokongola’yo anam’letsa kuchita chinthu chopusa’chi.

Kenako, tikuphunzira zambiri ponena za mwana wa Davide Solomo, amene analowa m’malo David monga mfumu ya Israyeli. Mafumu atatu oyamba a Israyeli ali yense analamulira zaka 40. Atafa Solomo, Israyeli anagawanika kukhala maufumu awiri, ufumu wakumpoto ndi wakumwela.

Ufumu wakumpoto wa mafuko 10 unakhala zaka 257 usanaonongedwe ndi Asuri. Ndiyeno zaka 133 pambuyo pake, ufumu wakumwela wa mafuko awiri’wo nawo’nso unaonongedwa. Pa nthawi’yi Aisrayeli anatengedwa ukapolo kumka ku Babulo. Chotero CHIGAWO chachinai chikulowetsamo zaka 510 za mbiri, m’kati mwa nthawi imene zochitika zambiri zosangalatsa zikuonekera kwa ife.