Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ULENDO WOBWEREZA

PHUNZIRO 7

Kuchita Khama

Kuchita Khama

Mfundo yaikulu: “Anapitiriza kuphunzitsa mwakhama . . . komanso ankalengeza uthenga wabwino.”​—Mac. 5:42.

Zomwe Paulo Anachita

1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Machitidwe 19:8-10. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  1.    Kodi Paulo anasonyeza bwanji khama pothandiza anthu omwe anasonyeza chidwi m’malo mogwa ulesi ndi anthu omwe ankamutsutsa?

  2.   Kodi Paulo anapita maulendo angati kukathandiza anthu achidwiwa, nanga anachita zimenezi kwa nthawi yaitali bwanji?

Zomwe Tikuphunzira kwa Paulo

2. Pamafunika nthawi yokwanira komanso khama kuti tichite maulendo obwereza komanso kuyambitsa maphunziro a Baibulo.

Zomwe Mungachite Potsanzira Paulo

3. Muzibwererakonso pa nthawi yomwe ali ndi mpata. Dzifunseni kuti: Kodi malo komanso nthawi yabwino kwambiri yomwe ndingamupeze ingakhale iti? Kodi iye adzapeza mpata liti? Khalani okonzeka kubwererakonso ngakhale kuti nthawiyo si yabwino kwa inu.

4. Muzipangana nthawi yoti mudzachezenso. Pambuyo pa ulendo uliwonse, kambiranani nthawi yeniyeni yomwe mungadzachezenso naye. Yesetsani kudzakumana naye pa nthawi yomwe mwagwirizanayo.

5. Musamataye mtima msanga. Musamathamangire kuganiza kuti ngati sapezekapezeka pakhomo komanso chifukwa choti amakhala wotanganidwa ndiye kuti basi alibe chidwi. (1 Akor. 13:4, 7) M’malomwake, yesetsanibe kumuyendera. Koma onetsetsani kuti mukugwiritsa ntchito nthawi yanu mwanzeru.​—1 Akor. 9:26.