PHUNZIRO 47
Kodi Mwakonzeka Kubatizidwa?
Pofika pano mwaphunzira zambiri zokhudza Yehova kuchokera m’Baibulo. Sitikukayikira kuti zomwe mwakhala mukuphunzira zakuthandizani kusintha zinthu zina pa moyo wanu. Komabe n’kutheka kuti pali zinthu zina zimene zikukulepheretsani kuti mudzipereke kwa Yehova komanso kubatizidwa. M’phunziroli tikambirana zinthu zina zimene zimalepheretsa anthu kubatizidwa komanso zomwe inuyo mungachite kuti zimenezi zisakulepheretseni kubatizidwa.
1. Kodi muyenera kudziwa zinthu zochuluka bwanji kuti mubatizidwe?
Kuti mubatizidwe, muyenera ‘kudziwa choonadi molondola.’ (1 Timoteyo 2:4) Zimenezi sizikutanthauza kuti muyenera kudziwa yankho la funso lililonse limene anthu angafunse lokhudza Baibulo. Tikutero chifukwa chakuti ngakhale Akhristu amene anabatizidwa kalekale, amapitirizabe kuphunzira zinthu zina. (Akolose 1:9, 10) Komabe, kuti mubatizidwe mufunika kuyamba kumvetsa bwino zimene Baibulo limaphunzitsa. Akulu amumpingo adzakuthandizani kudziwa ngati mwadziwa zinthu zokwanira zokhudza Baibulo.
2. Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene muyenera kuchita kuti mubatizidwe?
Kuti mubatizidwe muyenera ‘kulapa ndi kutembenuka.’ (Werengani Machitidwe 3:19.) Zimenezi zikutanthauza kuti muyenera kudzimvera chisoni chifukwa cha machimo amene munachita komanso kupempha Yehova kuti akukhululukireni. Muyeneranso kuyesetsa kupewa kuchita zimene Mulungu amaziona kuti ndi zoipa n’kumachita zimene iye amafuna. Kuwonjezera pamenepa, muyeneranso kumachita nawo misonkhano yampingo ndiponso kulalikira monga wofalitsa wosabatizidwa.
3. N’chifukwa chiyani simuyenera kulola kuti mantha akulepheretseni kubatizidwa?
Anthu ena amaopa kubatizidwa chifukwa amaona kuti akhoza kulephera kukwaniritsa zimene anamulonjeza Yehova. N’zoona kuti nthawi zina mukhoza kulakwitsadi zinthu. Koma dziwani kuti ngakhale amuna ndi akazi okhulupirika amene amatchulidwa m’Baibulo nawonso ankalakwitsa zinazake. Yehova sayembekezera kuti atumiki ake azichita zinthu mosalakwitsa kanthu. (Werengani Salimo 103:13, 14.) Yehova amasangalala mukamayesetsa kuchita zabwino. Iye ndi wokonzeka kukuthandizani. Ndipotu Yehova amatitsimikizira kuti ‘palibe chimene chingatilekanitse ndi chikondi chake.’—Werengani Aroma 8:38, 39.
FUFUZANI MOZAMA
Onani mmene kumudziwa bwino Yehova komanso kulola kuti akuthandizeni kungakuthandizireni kuti muthane ndi zinthu zimene zingakulepheretseni kubatizidwa.
4. Yesetsani kumudziwa bwino Yehova
Kodi mukuyenera kudziwa zinthu zochuluka bwanji zokhudza Yehova kuti mubatizidwe? Kuti muzikonda Yehova ndiponso kuchita zinthu zomusangalatsa muyenera kumudziwa bwino. Onerani VIDIYO kuti muone mmene anzanu ena padziko lonse achitira zimenezi. Kenako mukambirane funso lotsatirali.
-
N’chiyani chimene chinathandiza anthu omwe ali muvidiyoyi kuti abatizidwe?
Werengani Aroma 12:2, kenako mukambirane mafunso awa:
-
Kodi mukukayikira kuti zimene Baibulo limaphunzitsa ndi zoona kapena ngati zimene a Mboni za Yehova amaphunzitsa zilidi zolondola?
-
Ngati ndi choncho, muchitapo chiyani?
5. N’zotheka kuthana ndi zinthu zimene zingakulepheretseni kubatizidwa
Aliyense amakumana ndi mavuto akasankha kudzipereka kwa Yehova komanso kubatizidwa. Kuti muone chitsanzo cha zimenezi, onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.
-
Kodi Narangerel anathana ndi zinthu ziti zomwe zikanamulepheretsa kutumikira Yehova?
-
Kodi kukonda Yehova kunamuthandiza bwanji kuti athane ndi zinthu zomwe zikanamulepheretsa kubatizidwa?
Werengani Miyambo 29:25 ndi 2 Timoteyo 1:7, kenako mukambirane funso ili:
-
N’chifukwa chiyani timalimba mtima n’kuthana ndi zinthu zomwe zikanatilepheretsa kutumikira Yehova?
6. Musamakayikire kuti Yehova akuthandizani
Yehova ndi wokonzeka kukuthandizani kuti muzichita zomusangalatsa. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso awa.
-
Muvidiyoyi, n’chiyani chimene chinkalepheretsa wophunzira uja kuti abatizidwe?
-
Kodi anaphunzira mfundo iti yomwe inamuthandiza kuti asamakayikire kuti Yehova amuthandiza?
Werengani Yesaya 41:10, 13, kenako mukambirane funso ili:
-
N’chifukwa chiyani simuyenera kukayikira kuti mungakwanitse zonse zimene munalonjeza pamene munkadzipereka kwa Yehova?
7. Pitirizani kuyamikira Yehova chifukwa cha chikondi chimene anakusonyezani
Mukamaganizira kwambiri chikondi chimene Yehova anakusonyezani m’pamene mumamuyamikira kwambiri ndipo zimenezi zingakuchititseni kuti muzimutumikira kwa moyo wanu wonse. Werengani Salimo 40:5, kenako mukambirane funso ili:
-
Kodi ndi zinthu ziti zimene Yehova wakuchitirani zimene mumaziyamikira kwambiri?
Mneneri Yeremiya ankakonda Yehova ndi Mawu ake komanso ankayamikira kwambiri mwayi wodziwika ndi dzina la Yehova. Iye ananena kuti: “Mawu anu amandikondweretsa ndi kusangalatsa mtima wanga, pakuti ine ndimatchedwa ndi dzina lanu, inu Yehova Mulungu.” (Yeremiya 15:16) Yankhani mafunso awa:
-
N’chifukwa chiyani kukhala wa Mboni za Yehova ndi mwayi wapadera?
-
Kodi inuyo mukufuna kubatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova?
-
Kodi pali chilichonse chimene chikukulepheretsani kubatizidwa?
-
Kodi mungatani kuti mukwaniritse cholinga chanu choti mubatizidwe?
ZIMENE ENA AMANENA: “Ndikuopa kuti ndikabatizidwa ndikhoza kulephera kukwaniritsa zonse zomwe ndingalonjeze.”
-
Kodi inunso mukuona choncho?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Yehova angakuthandizeni kuthana ndi vuto lililonse lomwe lingakulepheretseni kuti mubatizidwe.
Kubwereza
-
Kodi mufunika kudziwa zinthu zochuluka bwanji kuti mubatizidwe?
-
Kodi mukufunikira kusintha zinthu ziti pa moyo wanu kuti mubatizidwe?
-
N’chifukwa chiyani simuyenera kuopa kubatizidwa?
ONANI ZINANSO
Onani chifukwa chake kukonda Yehova n’kofunika kwambiri kuti munthu abatizidwe.
“Kodi Ndinu Okonzeka Kubatizidwa?” (Nsanja ya Olonda, March 2020)
Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene mungachite ngati pali zinazake zimene zikukulepheretsani kubatizidwa.
“Chikundiletsa Kubatizidwa N’chiyani?” (Nsanja ya Olonda, March 2019)
Onani zimene munthu wina anachita kuti athane ndi zinthu zimene zinkamulepheretsa kubatizidwa.
Poyamba munthu wina, dzina lake Ataa, ankazengereza kubatizidwa. Onani chimene chinamuthandiza kutsimikizira kuti akufunikira kubatizidwa.