MUTU 16
Tsutsani Mdyerekezi
“Tsutsani Mdyerekezi ndipo adzakuthawani.”—YAKOBO 4:7.
1, 2. Kodi tikufunika kudziwa chiyani chokhudza Satana ndi ziwanda zake?
M’DZIKO latsopano tidzasangalala kwambiri. Tidzakhala ndi moyo wosangalala ngati mmene Yehova ankafunira poyamba. Koma panopa tikukhala m’dziko lomwe anthu ambiri akutsogoleredwa ndi Satana ndi ziwanda zake. (2 Akorinto 4:4) Ngakhale kuti Satana ndi ziwanda zake sitingathe kuwaona, alipo ndithu ndipo ndi amphamvu kwambiri.
2 M’mutuwu tikambirana zimene tingachite kuti tikhalebe pa ubwenzi ndi Yehova komanso tidziteteze kwa Satana. Yehova walonjeza kuti atithandiza. Koma tiyenera kudziwa njira zimene Satana ndi ziwanda zake amagwiritsa ntchito akafuna kutipusitsa komanso kutisocheretsa.
“MKANGO WOBANGULA”
3. Kodi Satana amafuna kuchita chiyani?
3 Satana amanena kuti anthufe timalambira Yehova pa zifukwa zadyera, ndipo zinthu zitavuta kwambiri tikhoza kusiya kumulambira. (Werengani Yobu 2:4, 5.) Munthu akasonyeza kuti akufuna kuphunzira za Yehova, Satana ndi ziwanda zake amazindikira zimenezi ndipo amayesetsa kuti amulepheretse. Iwo amakwiya munthu akadzipereka kwa Yehova kenako n’kubatizidwa. Baibulo limanena kuti Mdyerekezi ali ngati “mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.” (1 Petulo 5:8) Satana amafuna kuti awononge ubwenzi wathu ndi Yehova.—Salimo 7:1, 2; 2 Timoteyo 3:12.
4, 5. (a) Kodi Satana sangathe kuchita chiyani? (b) Kodi ‘tingatsutse bwanji Mdyerekezi’?
4 Koma sitiyenera kuopa Satana ndi ziwanda zake. Yehova samawalola kuti azitichitira chilichonse chimene akufuna. Yehova analonjeza kuti “khamu lalikulu” la Akhristu oona lidzapulumuka “chisautso chachikulu.” (Chivumbulutso 7:9, 14) Palibe chimene Mdyerekezi angachite kuti zimenezi zilephereke, chifukwa Yehova amateteza anthu ake.
2 Mbiri 15:2; werengani 1 Akorinto 10:13.) Anthu akale okhulupirika monga Abele, Inoki, Nowa, Sara komanso Mose anatsutsa Mdyerekezi poyesetsa kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. (Aheberi 11:4-40) Ifenso tingachite chimodzimodzi. Mawu a Mulungu amatiuza kuti: “Tsutsani Mdyerekezi ndipo adzakuthawani.”—Yakobo 4:7.
5 Ngati titayesetsa kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, Satana sangawononge ubwenzi wathuwo. Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti: “Yehova akhala nanu inuyo mukapitiriza kukhala naye.” (PALI KULIMBANA
6. Kodi Satana amatiukira bwanji?
6 Ngakhale kuti Satana akudziwa kuti Yehova sangamulole kutichitira chilichonse chimene akufuna, amayesetsabe kuchita chilichonse chimene angathe kuti awononge ubwenzi wathu ndi Mulungu. Masiku ano Mdyerekezi amaukira anthu m’njira zosiyanasiyana ndipo njirazi wakhala akuzigwiritsa ntchito kwa zaka zambiri. Kodi zina mwa njira zimenezi ndi ziti?
7. Kodi Satana amaukira anthu a Yehova chifukwa chiyani?
7 Mtumwi Yohane analemba kuti: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Dziko lonse loipali lili m’manja mwa Satana ndipo amafuna kuti azilamulira anthu onse, ndi anthu a Yehova omwe. (Mika 4:1; Yohane 15:19; Chivumbulutso 12:12, 17) Mdyerekezi akudziwa kuti watsala ndi nthawi yochepa, choncho akuyesetsa kuti atilepheretse kukhala okhulupirika kwa Mulungu. Nthawi zina amagwiritsa ntchito njira zoonekera, koma nthawi zambiri amagwiritsa ntchito njira zovuta kuzitulukira.
8. Kodi Mkhristu aliyense ayenera kudziwa chiyani?
8 Lemba la Aefeso 6:12 limanena kuti: ‘Tikulimbana ndi makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba.’ Izi zikusonyeza kuti Mkhristu aliyense amene anadzipereka kwa Yehova ali pa nkhondo yolimbana ndi Mdyerekezi komanso ziwanda. M’kalata imene Paulo analembera Akhristu a ku Efeso, anawalimbikitsa kuti ‘akhale olimba.’—Aefeso 6:11, 13, 14.
9. Kodi Satana ndi ziwanda zake amafuna kutichitira chiyani?
9 Satana ndi ziwanda zake amayesetsa kutisocheretsa m’njira zosiyanasiyana. Tikapambana pa mayesero enaake a Satana, sizitanthauza kuti sitingagonje pa mayesero ena onse. Mdyerekezi amayesetsa kuyang’ana zofooka zathu kuti apeze msampha wabwino woti atikole nawo. Koma sitikuyenera kukodwa chifukwa Baibulo limatithandiza kudziwa misampha imene Satana amagwiritsa ntchito. (2 Akorinto 2:11; onani Mawu Akumapeto 31.) Msampha umodzi umene amagwiritsa ntchito ndi kukhulupirira mizimu.
MUSAMAKHUDZE CHILICHONSE CHOGWIRIZANA NDI KUKHULUPIRIRA MIZIMU
10. (a) Kodi kukhulupirira mizimu n’kutani? (b) Kodi Yehova amaona bwanji kukhulupirira mizimu?
10 Kuchita zamizimu kumaphatikizapo kuchita chilichonse chimene chingapangitse kuti munthu azigwirizana ndi ziwanda. Izi ndi zinthu monga kulosera, kuchita zaufiti, kuombeza kapena kuyesa kulankhula ndi akufa. Baibulo limanena kuti zamizimu ndi “zonyansa” ndipo sitingamachite zamizimu kwinaku n’kumalambiranso Yehova. (Deuteronomo 18:10-12; Chivumbulutso 21:8) Choncho Akhristu ayenera kupewa mtundu uliwonse wa kukhulupirira mizimu.—Aroma 12:9.
11. Kodi chingachitike n’chiyani ngati titayamba kuchita chidwi ndi zinthu zamatsenga?
11 Satana amadziwa kuti tikayamba kuchita chidwi ndi zamatsenga, sizingakhale zovuta kutikopa kuti tiyambe kuchita zamizimu. Mtundu uliwonse wa kukhulupirira mizimu ungasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova.
SATANA AMAFUNA KUTIPUSITSA
12. Kodi Satana amachita chiyani pofuna kusokoneza maganizo athu?
12 Satana amafuna kusokoneza maganizo a anthu. Amatichititsa kuti tiyambe kukayikira zinthu zina mpaka kufika pomaona kuti “chabwino n’choipa ndipo choipa n’chabwino.” (Yesaya 5:20) Iye amalimbikitsa maganizo akuti malangizo a m’Baibulo ndi osathandiza ndipo tingamasangalale kwambiri ngati titasiya kutsatira mfundo za m’Baibulo.
13. Kodi Satana wachitapo zotani kuti anthu ayambe kukayikira zinazake?
13 Umodzi mwa misampha imene Satana amaidalira kwambiri ndi kukayikira. Iye wakhala akugwiritsa ntchito msampha umenewu kuyambira kale kwambiri. Mwachitsanzo, m’munda wa Edeni anamufunsa Hava funso lom’chititsa kuti ayambe kukayikira zimene Mulungu anamuuza. Anamufunsa kuti: “Eti n’zoona kuti Mulungu anati musadye zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu?” (Genesis 3:1) Patapita nthawi, Satana anafunsa Yehova pamaso pa angelo ena kuti: “Kodi mukuganiza kuti Yobu amangoopa Mulungu pachabe?” (Yobu 1:9) Komanso Yesu atabatizidwa, Satana anamuuza kuti: “Ngati ndinudi mwana wa Mulungu, uzani miyala iyi kuti isanduke mitanda ya mkate.”—Mateyu 4:3.
14. Kodi Satana amatani pofuna kuchititsa kuti anthu azikayikira ngati kuchita zamizimu kulidi koopsa?
14 Masiku anonso Satana amachititsa kuti anthu ayambe kukayikira zinazake. Mwachitsanzo, amawachititsa kuti azikayikira ngati zamizimu zilidi zoipa kwambiri. Iye amachita zimenezi popangitsa zinthu zina zokhudza kukhulupirira mizimu kuoneka ngati zabwinobwino. Moti ngakhale Akhristu ena ayamba kuona kuti palibe vuto kuchita zinthu zina zokhudzana ndi kukhulupirira mizimu. (2 Akorinto 11:3) Ndiye kodi tingadziteteze bwanji? Nanga tingatani kuti Satana asatipusitse? Tiyeni tikambirane njira ziwiri zimene Satana angazigwiritse ntchito pofuna kutipusitsa. Njira zake ndi: Zosangalatsa komanso thandizo lamankhwala.
SATANA AMATIKOPA NDI ZINTHU ZOMWE MWACHIBADWA TIMAZIFUNA NDI KALE
15. Kodi zosangalatsa zimene timakonda zingachititse bwanji kuti tiyambe kuchita zinthu zogwirizana ndi zamizimu?
15 Masiku ano, mavidiyo, mapulogalamu a pa TV, masewera a pakompyuta komanso mawebusaiti ambiri amakhala ndi zinthu zolimbikitsa kukhulupirira mizimu komanso kuchita zamatsenga. Anthu ambiri amaona kuti zimenezi zilibe vuto ndipo sadziwa kuti kuchita zinthu zokhudzana ndi ziwanda n’koopsa. Munthu angathenso kuyamba kuchita zamizimu kudzera mu zinthu monga kukhulupirira nyenyezi, kutanthauzira mizere ya m’manja, kugwiritsa ntchito makadi oombezera komanso kuona pagalasi la matsenga. Mdyerekezi amachititsa kuti anthu asamaone kuopsa kwa zinthu zimenezi ndipo amayesetsa kuti zizioneka zokopa komanso zosangalatsa. Munthu akhoza kumaganiza kuti palibe vuto kumaonera zinthu zamizimu kapena zamatsenga bola ngati iyeyo sachita zamizimu. Kodi maganizo amenewa ndi oopsa bwanji?—1 Akorinto 10:12.
16. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kupewa zosangalatsa zokhudzana ndi zamizimu?
16 Satana ndi ziwanda zake sangadziwe zimene tikuganiza. Koma akaona zimene timasankha pa nkhani ya zosangalatsa komanso nkhani zokhudza ifeyo kapena banja lathu, amatha kudziwa zimene timaganiza komanso zimene timalakalaka. Mwachitsanzo, akaona kuti tasankha mafilimu, nyimbo kapena mabuku onena za asing’anga, matsenga, anthu okhala ndi ziwanda, afiti, mizukwa kapena zinthu zina za ngati zimenezi, amadziwa kuti tili ndi chidwi ndi zamizimu. Agalatiya 6:7.
Akaona zimenezi amayesetsa kuti tiyambe kukonda kwambiri zinthu zamizimu.—Werengani17. Kodi Satana amapezerapo bwanji mwayi pa mtima wathu wofuna kukhala ndi moyo wathanzi?
17 Satana angapezereponso mwayi pa mtima wathu wofuna kukhala ndi moyo wathanzi. Masiku ano anthu ambiri akuvutika ndi matenda. Munthu angayese njira zosiyanasiyana koma n’kupezeka kuti sakuchira. (Maliko 5:25, 26) Angafike posowa mtengo wogwira ndipo angakhale wokonzeka kuchita chilichonse kuti achire. Komabe Akhristufe tiyenera kupewa thandizo lililonse lamankhwala limene limaphatikizapo kugwiritsa ntchito “mphamvu zamatsenga.”—Yesaya 1:13.
18. Kodi ndi chithandizo chamankhwala chiti chimene Mkhristu ayenera kupewa?
Yesaya 1:15) Taganizirani mfundo imeneyi: Yehova sankamvetsera n’komwe mapemphero awo. Timafuna kuti Yehova azitithandiza nthawi zonse, makamaka tikamadwala. Choncho sitingakonde kuchita chilichonse chimene chingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova kapena chimene chingachititse kuti asiye kutithandiza. (Salimo 41:3) Choncho tisanalandire chithandizo chilichonse chamankhwala tiyenera kufufuza kuti tidziwe ngati sichikugwirizana ndi zamizimu kapena zamatsenga. (Mateyu 6:13) Ngati zikuoneka kuti chithandizocho chikugwirizana ndi zamizimu, tiyenera kukana.—Onani Mawu Akumapeto 32.
18 Kale ku Isiraeli, anthu ena ankagwiritsa ntchito “mphamvu zamatsenga.” Yehova anauza anthu amenewa kuti: “Mukatambasula manja anu, ndimakubisirani maso anga. Ngakhale mupereke mapemphero ambiri, ine sindimvetsera.” (NKHANI ZA ZIWANDA
19. N’chiyani chachititsa kuti anthu ambiri aziopa Mdyerekezi?
19 Anthu ena amaganiza kuti Mdyerekezi ndi ziwanda ndi ongoyerekezera. Koma ena amadziwa kuti Satana ndi ziwanda zake alipodi chifukwa cha zimene anakumana nazo pa moyo wawo. Anthu ambiri amakhala mwamantha chifukwa choopa kwambiri mizimu yoipa ndipo amakakamizika kuchita nawo miyambo yokhudzana ndi kukhulupirira mizimu. Ena amachititsa kuti anthu aziopa ziwanda pofalitsa nkhani za zinthu zoopsa zimene ziwanda zimachitira anthu. Anthu ambiri amachita chidwi ndi nkhani zoterezi ndipo amasangalala kufotokozeranso ena. Nkhani zimenezi zimachititsa kuti anthu aziopa kwambiri Mdyerekezi.
20. Kodi tingafalitse bwanji bodza la Satana?
20 Taganizirani mfundo iyi: Satana amafuna kuti anthu 2 Atesalonika 2:9, 10) Iye ndi wabodza ndipo amadziwa mmene angasokonezere maganizo a anthu amene amakhulupirira zamizimu ndipo amawapangitsa kuti azikhulupirira zinthu zomwe si zoona. Anthu oterewa amafotokozera anzawo nkhani za zinthu zimene akuganiza kuti aona kapena kumva. Nkhani zimenezi zikamafalikira zimanka zikometseredwa, moti kenako zimayamba kuoneka ngati zoona. Koma Akhristufe timapewa kuuza ena nkhani zoterezi chifukwa sitifuna kuthandiza Satana kufalitsa bodza.—Yohane 8:44; 2 Timoteyo 2:16.
azimuopa. (21. M’malo mouza anthu nkhani zokhudza ziwanda, kodi tiyenera kuwauza za chiyani?
21 Ngati mtumiki wa Yehova ankavutitsidwa ndi ziwanda, sayenera kumaona zomwe zinkamuchitikirazo ngati nkhani zosangalatsa zoti n’kumafotokozera ena. Si bwino kumawopseza anthu a Mulungu ndi nkhani za zimene Satana ndi ziwanda zake amachita. M’malomwake, tiyenera kumakambirana kwambiri za Yesu komanso mphamvu zimene Yehova anamupatsa. (Aheberi 12:2) Yesu sankangokhalira kucheza ndi ophunzira ake nkhani zokhudza ziwanda. Iye ankakonda kuwafotokozera za uthenga wa Ufumu komanso “zinthu zazikulu za Mulungu.”—Machitidwe 2:11; Luka 8:1; Aroma 1:11, 12.
22. Kodi inuyo mukufunitsitsa kuchita chiyani?
22 Tisaiwale kuti cholinga cha Satana ndi kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova. Iye adzayesetsa kuchita chilichonse kuti zimenezi zitheke. Koma ubwino wake ndi wakuti tikudziwa njira zonse zimene amagwiritsa ntchito ndipo tikufunitsitsa kupewa mtundu uliwonse wa kukhulupirira mizimu. Sitikufuna ‘kumupatsa malo Mdyerekezi’ kuti atilepheretse kupewa kukhulupirira mizimu. (Werengani Aefeso 4:27.) Tikatsutsa Mdyerekezi, sadzakwanitsa kutikola ndi misampha yake ndipo tidzakhala otetezeka m’manja mwa Yehova.—Aefeso 6:11.