Dzikoli Lidzakhala Paradaiso
Yehova adzathetsa mavuto onse amene Satana anayambitsa ndipo anasankha Yesu kuti akhale Mfumu ya dziko lonse. Yesu akadzayamba kulamulira dzikoli, lidzakhala paradaiso.—Danieli 7:13, 14; Luka 23:43.
Yehova anatilonjeza zinthu zotsatirazi:
-
PADZAKHALA CHAKUDYA CHAMBIRI: “Dziko lapansi lidzapereka zipatso zake. Mulungu, ndithu Mulungu wathu, adzatidalitsa.” “Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.”—Salimo 67:6; 72:16.
-
SIPADZAKHALANSO NKHONDO: “Bwerani anthu inu, onani ntchito za Yehova, onani mmene wakhazikitsira zinthu zodabwitsa padziko lapansi. Akuletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”—Salimo 46:8, 9.
-
SIPADZAKHALANSO ANTHU OIPA: “Pakuti ochita zoipa adzaphedwa. Koma oyembekezera Yehova ndi amene adzalandire dziko lapansi. Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso. Udzayang’ana pamene anali Salimo 37:9, 10.
kukhala, ndipo sadzapezekapo.”— -
SIPADZAKHALANSO MATENDA, KUVUTIKA KOMANSO IMFA: “Pa nthawi imeneyo, maso a anthu akhungu adzatsegulidwa, ndipo makutu a anthu ogontha adzayamba kumva. Pa nthawiyo, munthu wolumala adzakwera phiri ngati mmene imachitira mbawala yamphongo. Lilime la munthu wosalankhula lidzafuula mokondwa.”—Yesaya 35:5, 6.
“Mulunguyo adzakhala nawo. Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
Yehova amanena zoona zokhazokha koma Satana ndi ziwanda ndi abodza. Yehova amachita chilichonse chimene walonjeza. (Luka 1:36, 37) Iye amakukondani ndipo akufuna kuti mudzakhale m’Paradaiso. A Mboni za Yehova angakuthandizeni kudziwa zinthu zabwino zimene zili m’Mawu a Mulungu. Mukamatsatira mfundo za m’Baibulo simudzanamizidwa, simudzaopa mizimu ndipo mudzakhala ozindikira. M’tsogolomu, tonse sitidzakhalanso akapolo a uchimo ndi imfa. Paja Yesu ananena kuti: “Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.”—Yohane 8:32.