Chipatso cha Mzimu
Kodi mzimu wa Mulungu umatithandiza kukhala ndi makhalidwe ati? Nanga n’chifukwa chiyani tifunika kukhala odzichepetsa kuti Mulungu atipatse mzimu wake?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Sl 143:1, 4-11—Pa nthawi imene Mfumu Davide anavutika kwambiri, ankaganizira ntchito za Yehova komanso anapemphera kuti amupatse mzimu woyera
Lu 11:9-13—Yesu anagwiritsa ntchito fanizo potikumbutsa kuti Yehova ndi wofunitsitsa kupereka mzimu wake woyera kwa amene amupempha