Zokhudza Kusunga Chinsinsi

Pofuna kukuthandizani kuti musamavutike kuchita zinthu pawebusaiti yathu, timagwiritsa ntchito ma cookies ndiponso njira zina zamakono zofanana ndi zimenezi. Ma cookies ena amathandiza kuti webusaiti yathu izigwira bwino ntchito ndipo sizingatheke kuwakana. Mukhoza kuvomereza kapena kukana ma cookies ena owonjezera, omwe cholinga chake ndi kungokuthandizani kuti musamavutike kuchita zinthu zina pawebusaiti. Sitidzagulitsa kapena kugwiritsa ntchito mauthenga amenewa pofuna kutsatsa malonda. Kuti mudziwe zambiri, werengani Ndondomeko ya Padziko Lonse ya Mmene Timagwiritsira Ntchito ma Cookies ndi Njira Zina Zamakono. Mukhoza kusintha ma settings nthawi ina iliyonse popita pa Zokhudza Kusunga Chinsinsi.

Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 14

Kuthandiza Anthu Kuti Aone Mfundo Zazikulu

Kuthandiza Anthu Kuti Aone Mfundo Zazikulu
Lemba

Aheberi 8:1

MFUNDO YAIKULU: Thandizani anthu kuti azitsatira nkhani yanu komanso aziona kugwirizana pakati pa mfundo zazikulu ndi mutu wa nkhani yonseyo.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Muzikhala ndi cholinga. Muzidzifunsa kuti, Kodi cholinga cha nkhaniyi n’chiyani? Kodi ndi kuphunzitsa, kuthandiza anthu kuti asinthe maganizo kapena kuwalimbikitsa kuchita zinazake? Ndiyeno mfundo zikuluzikulu zizikuthandizani kukwaniritsa cholingacho.

  • Muzitsindika mutu wa nkhani yanu. Munkhani yanu yonse muzitsindika mutu potchula mawu ofunika kwambiri a m’mutuwo kapena kugwiritsa ntchito mawu ofanana nawo.

  • Muzithandiza anthu kuona mfundo zazikulu m’njira yosavuta. Muzisankha mfundo zikuluzikulu zimene zikugwirizana ndi mutu wa nkhani komanso zimene mungazifotokoze bwino popanda kudya nthawi. Mfundo zikuluzikulu zizikhala zochepa, muzitchula mfundo iliyonse momveka, muzipuma mukamachoka pa mfundo ina kupita pa ina kuti musawasiye anthu m’malere.