Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 1

“Yehova Mulungu Wako Ndi Amene Uyenera Kumulambira”

“Yehova Mulungu Wako Ndi Amene Uyenera Kumulambira”

MATEYU 4:10

MFUNDO YAIKULU: Chifukwa chake kulambira koyera kukufunika kubwezeretsedwa

1, 2. Kodi chinachitika n’chiyani kuti Yesu apezeke m’chipululu cha Yudeya mu 29 C.E, nanga n’chiyani chinamuchitikira kumeneko? (Onani chithunzi choyambirira.)

 CHAKUMAPETO kwa October kapena kumayambiriro kwa November mu 29 C.E, Yesu anapita kuchipululu cha Yudeya chomwe chinali kumpoto kwa Nyanja Yakufa. Chipululuchi chinali cha miyala komanso maphedi. Mzimu woyera ndi umene unamupititsa kumeneko pambuyo poti wabatizidwa komanso kudzozedwa. Yesu anakhala m’chipululu chimenechi kwa masiku 40 ndipo ankasala kudya, ankapemphera komanso kusinkhasinkha. Mwina pa nthawi imeneyi, Yehova analankhula ndi Mwana wakeyu n’kumukonzekeretsa zimene zichitike m’tsogolo.

2 Ndiyeno Yesu atafooka ndi njala Satana anabwera. Zimene zinachitika pambuyo pake zikusonyeza nkhani yofunika kwambiri imene ikukhudza onse amene amakonda kulambira koyera, kuphatikizapo inuyo.

“Ngati Ndinu Mwana wa Mulungu . . . ”

3, 4. (a) Kodi Satana anayamba mayesero awiri oyambirira ndi mawu oti chiyani, nanga ankafuna kuti Yesu azikayikira za chiyani? (b) Kodi Satana amagwiritsa ntchito bwanji njira zimenezi potiyesa masiku ano?

3 Werengani Mateyu 4:1-7. Satana anayamba mayesero awiri oyamba ndi mawu akuti, “Ngati ndinu mwana wa Mulungu.” Kodi Satana ankakaikira zoti Yesu ndi Mwana wa Mulungu? Ayi. Mngelo wopandukayu ankadziwa bwino kuti Yesu ndi Mwana woyamba kubadwa wa Mulungu. (Akol. 1:15) Satana ayenera kuti ankadziwanso mawu amene Yehova analankhula kuchokera kumwamba pa nthawi imene Yesu ankabatizidwa. Mulungu ananena kuti: “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa ndipo amandisangalatsa kwambiri.” (Mat. 3:17). Mwina Satana ankafuna kuti Yesu ayambe kukaikira zoti Atate ake anali odalirika komanso ankamuganizira. Pamene ankamuyesa koyamba, Satana anauza Yesu kuti asandutse mwala kukhala mkate. Ponena zimenezi iye ankatanthauza kuti: ‘Popeza ndiwe Mwana wa Mulungu n’chifukwa chiyani Atate ako sanakupatse chakudya m’chipululu muno?’ Pamene ankamuyesa kachiwiri Satana anauza Yesu kuti adumphe pamwamba pa mpanda wa kachisi. Ponena zimenezi Satana ankatanthauza kuti: ‘Popeza ndiwe Mwana wa Mulungu, kodi ukukhulupiriradi kuti Atate ako angakuteteze?’

4 Masiku ano Satana amagwiritsanso ntchito njira zofanana ndi zimenezi. (2 Akor. 2:11) Woyesayu amayembekezera kuti amene amalambira Mulungu m’njira yoyenera afooke kaye kapena kukhumudwa kuti kenako awayese m’njira zovuta kuzindikira. (2 Akor. 11:14) Iye amafuna kutipusitsa kuti tizikhulupirira kuti Yehova sangatikonde kapena kusangalala nafe. Woyesayu amafunanso kuti tizikhulupirira kuti Yehova ndi wosadalirika ndipo sadzachita zimene analonjeza m’Mawu ake. Koma amenewa ndi mabodza amkunkhuniza. (Yoh. 8:44) Kodi tingapewe bwanji mabodza amenewa?

5. Kodi Yesu anayankha bwanji mayesero awiri oyambirira?

5 Ganizirani mmene Yesu anakanira mayesero oyamba ndi achiwiri aja. Iye sankakayikira kuti Atate ake amamukonda ndipo ankawakhulupirira kwambiri. Mosazengereza Yesu anakana kuchita zimene Satana ankafuna ndipo anagwira Mawu ouziridwa a Atate ake. Apa Yesu anagwira Malemba amene anali ndi dzina la Mulungu, lakuti Yehova. (Deut. 6:16; 8:3) Dzinali ndi lapadera chifukwa limatsimikizira kuti Yehova adzakwaniritsa malonjezo ake onse. Choncho pogwiritsa ntchito dzina la Mulungu, Yesu anasonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri Atate ake. a

6, 7. Kodi tingatani kuti tipewe mayesero osaonekera a Satana?

6 Tingapewe mayesero osaonekera a Satana tikamadalira Mawu a Yehova komanso kuganizira tanthauzo la dzina la Mulungu. Tikamaona kuti Yehova amatikonda ngati mmene Malemba amanenera komanso kuti amaganizira anthu amene amamulambira, kuphatikizapo amene akuvutika ndi nkhawa, tingapewe bodza la Satana lakuti Yehova sangatikonde ndipo sizingatheke kumusangalatsa. (Sal. 34:18; 1 Pet. 5:8) Tikamakumbukira kuti Yehova nthawi zonse amachita zinthu mogwirizana ndi dzina lake, sitidzakayikira kuti Mulungu, amene amakwaniritsa zimene walonjeza ndi woyenera kumukhulupirira ndi mtima wonse.​—Miy. 3:5, 6.

7 Koma kodi cholinga chachikulu cha Satana n’chiyani? Kodi kwenikweni amafuna kuti tizichita chiyani? Yankho tikulipeza tikaganizira zimene Satana ananena pamene ankayesa Yesu kachitatu.

‘Mugwade Pansi Kamodzi Kokha Nʼkundilambira’

8. Pamene ankayesa Yesu kachitatu, kodi Satana anasonyeza bwanji zimene ankafuna?

8 Werengani Mateyu 4:8-11. M’mayesero achitatuwa Satana ananena mosapita m’mbali zimene ankafuna. Iye anaonetsa Yesu (mwina kudzera m’masomphenya) “maufumu onse apadziko ndi ulemerero wawo,” koma sanamuonetse zinthu zoipa zimene amachita. Kenako anauza Yesu kuti: “Ndikupatsani zinthu zonsezi ngati mutagwada pansi kamodzi kokha nʼkundilambira.” b Chimene ankafuna ndi kulambiridwa basi. Satana ankafuna kuti Yesu asiye kulambira Atate ake koma azilambira iyeyo. Zimene Satana anauza Yesu zinkaoneka ngati njira yachidule yopezera zimene ankafuna. Iye ankatanthauza kuti Yesu angakhale ndi mphamvu zonse komanso chuma cha padziko lapansi koma popanda kukumana ndi mavuto. Mwachitsanzo, sakanafunikira kuvala chisoti chaminga, kukwapulidwa komanso kumukhomerera pamtengo wozunzikirapo. Amenewatu anali mayesero amphamvu. Yesu sanatsutse kuti maboma onse am’dzikoli ali m’manja mwa Satana. (Yoh. 12:31; 1 Yoh. 5:19) N’zoonekeratu kuti Satana anali wokonzeka kupereka chilichonse kuti achititse Yesu kusiya kulambira koyera.

9. (a) Kodi Satana kwenikweni amafuna kuti olambira oona azichita chiyani, nanga amatiyesa m’njira ziti? (b) Kodi kulambira kwathu kumaphatikizapo zinthu ziti? (Onani bokosi lakuti “Kodi Kulambira N’kutani?”)

9 Masiku anonso Satana akufuna kuti tisiye kulambira Mulungu n’kumalambira iyeyo kapena kuti tisiye kuchita zimene Mulungu amafuna. Popeza kuti iye ndi “mulungu wa nthawi ino,” zipembedzo zonse zabodza kapena kuti Babulo Wamkulu, zimalambira iyeyo. (2 Akor. 4:4) Koma iye sakhutira ndi anthu mabiliyoni ambiri amene ali m’zipembedzo zabodza omwe amamulambira ndipo akufuna kuti anthu amene amalambira Mulungu m’njira yoyenera azichita zosemphana ndi zimene Mulunguyo amafuna. Amatinyengerera kuti tizifunafuna chuma komanso kutchuka m’dzikoli m’malo motsatira mfundo za m’Malemba zimene nthawi zina zimachititsa kuti tizivutika “chifukwa chochita zinthu mwachilungamo.” (1 Pet. 3:14) Ngati titagonja pa mayesero oti tisiye kulambira koyera n’kukhala mbali ya dziko la Satanali, ndiye kuti Satana wakhala mulungu wathu ndipo tikumugwadira komanso kumulambira. Kodi tingapewe bwanji mayesero amenewa?

10. Kodi Yesu anayankha bwanji mayesero achitatu ndipo n’chifukwa chiyani anayankha choncho?

10 Onani mmene Yesu anayankhira pa mayesero achitatu aja. Posonyeza kuti anali wokhulupirika kwa Yehova, nthawi yomweyo anauza Satana kuti: “Choka Satana!” Monga mmene anachitira ndi mayesero awiri oyamba aja, Yesu anagwira mawu ochokera m’buku la Deuteronomo omwe ali ndi dzina la Mulungu. Iye anati: “Malemba amati, ‘Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.’” (Mat. 4:10; Deut. 6:13) Choncho Yesu anakana kupeza udindo waukulu mosavutikira komanso moyo wawofuwofu wa m’dzikoli womwe ndi wosakhalitsa. Iye ankadziwa kuti Atate ake okha ndi amene akuyenera kulambiridwa komanso kuti ‘kulambira’ Satana kamodzi kokha kukanasonyeza kuti amagonjera Satanayo. Molimba mtima Yesu anakana kuti Woyesayo akhale mulungu wake. Yesu atakana zimene Woyesayo ankafuna, “Mdyerekezi uja anamusiya.” c

“CHOKA SATANA!” (Onani ndime 10)

11. Kodi tingatani kuti tipewe Satana ndi mayesero ake?

11 Mofanana ndi Yesu, ifenso tili ndi ufulu wosankha kukana mayesero a Satana ndi dziko lake loipali. Yehova anatipatsa mphatso yamtengo wapatali yomwe ndi ufulu wosankha zochita. Choncho palibe aliyense amene angatikakamize kuti tisiye kulambira koyera, ngakhale Satana yemwe ndi wamphamvu komanso woipa. ‘Tikakhala ndi chikhulupiriro cholimba n’kumalimbana ndi Satana’ mokhulupirika, timakhala tikunena kuti: “Choka Satana!” (1 Pet. 5:9) Tisaiwale kuti Satana anachoka Yesu atamukana mwamphamvu. Mofanana ndi zimenezi, Baibulo limatiuza kuti: “Tsutsani Mdyerekezi ndipo adzakuthawani.”​—Yak. 4:7.

Tikhoza kusankha kukana mayesero a dziko la Satanali (Onani ndime 11, 19)

Mdani wa Kulambira Koyera

12. M’munda wa Edeni, kodi Satana anasonyeza bwanji kuti amadana ndi kulambira koyera?

12 Mayesero omalizira a Satana anasonyeza kuti iye anali woyambirira kudana ndi kulambira koyera. Zaka masauzande ambiri m’mbuyomo m’munda wa Edeni, Satana anasonyeza kuti amadana ndi kulambira Yehova. Popusitsa Hava amene pambuyo pake ananyengerera Adamu kuti asamvere lamulo la Yehova, Satana anachititsa kuti akhale mtsogoleri wawo n’kuyamba kuwalamulira. (Werengani Genesis 3:1-5; 2 Akor. 11:3; Chiv. 12:9) Apa tinganene kuti Satana anakhala mulungu wawo ndipo iwo anayamba kumulambira ngakhale kuti sankadziwa bwinobwino kuti amene wawasocheretsayu ndi ndani. Komanso poyambitsa kupanduka m’munda wa Edeni, sikuti Satana anangotsutsa ulamuliro wa Yehova kapena kukaikira ngati ali woyenera kulamulira koma anayambanso kutsutsa kulambira koyera. Kodi anachita bwanji zimenezi?

13. Kodi kulambira koyera kukugwirizana bwanji ndi nkhani yakuti ndi ndani amene ali woyenera kulamulira?

13 Nkhani ya ulamuliro ikukhudzanso kulambira koyera. Wolamulira Wamkulu, amene ‘analenga zinthu zonse’ ndi yekhayo amene ali woyenera kumulambira. (Chiv. 4:11) Yehova atalenga Adamu ndi Hava omwe anali angwiro n’kuwaika m’munda wa Edeni, ankafuna kuti pamapeto pake dziko lonse lapansi lidzadzaze ndi anthu angwiro amene azidzamulambira m’njira yovomerezeka komanso ndi mtima woyera. (Gen. 1:28) Satana anatsutsa ulamuliro wa Yehova chifukwa ankafuna kuti azilambiridwa. Komatu Yehova yekha, amene ndi Ambuye Wamkulu Koposa, ndi amene akuyenera kulambiridwa.​—Yak. 1:14, 15.

14. Kodi Satana anakwanitsa kusokoneza kulambira koyera? Fotokozani.

14 Kodi zolinga za Satana potsutsa kulambira koyera zinakwaniritsidwa? Iye anakwanitsa kuchotsa Adamu ndi Hava kumbali ya Mulungu. Kuchokera nthawi imeneyo Satana akumenyabe nkhondo yolimbana ndi kulambira koyera ndipo akufuna kuchotsa anthu ambiri kumbali ya Yehova Mulungu. Chikhristu chisanayambe, Satana anapitirizabe kuyesa atumiki a Yehova. M’nthawi ya atumwi iye anayambitsa mpatuko umene unachititsa kuti zinthu zisokonekere mumpingo wa Chikhristu ndipo patapita nthawi zinkaoneka ngati kulambira koyera kwatha. (Mat. 13:24-30, 36-43; Mac. 20:29, 30) M’zaka za m’ma 100 C.E., atumiki a Mulungu anakhala kwa nthawi yaitali mu ukapolo wauzimu mu Babulo Wamkulu, amene ndi zipembedzo zonse zabodza. Koma Satana sanakwanitse kulepheretsa cholinga cha Mulungu chokhudza kulambira koyera. Palibe chimene chingalepheretse Mulungu kukwaniritsa cholinga chake. (Yes. 46:10; 55:8-11) Cholinga chake chikukhudza dzina lake ndipo nthawi zonse amachita zinthu zogwirizana ndi tanthauzo la dzina lake. Yehova sangalephere kukwaniritsa zolinga zake.

Wolimbikitsa Kulambira Koyera

15. Kodi Yehova anachita chiyani mu Edeni kwa opandukawo pofuna kuonetsetsa kuti cholinga chake chidzakwaniritsidwe?

15 M’munda wa Edeni Yehova anapereka chilango kwa opandukawo nthawi yomweyo komanso anaonetsetsa kuti cholinga chake chidzakwaniritsidwe. (Werengani Genesis 3:14-19.) Adamu ndi Hava adakali m’mundamo Yehova anapereka chiweruzo kwa onse atatu, kuyambira ndi Satana amene anayambirira kuchimwa, kenako Hava n’kumaliza ndi Adamu. Polankhula ndi Satana amene Adamu ndi Hava sankatha kumuona, Yehova ananeneratu kuti kudzabwera “mbadwa” imene idzathetse mavuto amene anabwera chifukwa cha kupandukako. “Mbadwa” yolonjezedwayo inali yoti idzathandize kukwaniritsa cholinga cha Yehova chokhudza kulambira koyera.

16. Satana, Adamu ndi Hava atapanduka m’munda wa Edeni, kodi Yehova wakhala akuchita chiyani kuti cholinga chake chidzakwaniritsidwe?

16 Satana, Adamu ndi Hava atapanduka mu Edeni, Yehova wakhala akugwirabe ntchito pokwaniritsa cholinga chake. Iye anakonza zoti anthu omwe si angwiro azimulambira movomerezeka, ngati mmene tionere m’mutu wachiwiri. (Aheb. 11:4–12:1) Komanso anauzira anthu osiyanasiyana amene analemba Baibulo kuphatikizapo Yesaya, Yeremiya ndi Ezekieli, kuti alembe maulosi ochititsa chidwi okhudza kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera. Mfundo yaikulu ya Baibulo lonse ikukhudza kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera kumeneku. Maulosi onsewo anali oti adzakwaniritsidwa ndi “mbadwa” yolonjezedwa, yomwe ndi Yesu Khristu. (Agal. 3:16) Yesu amalimbikitsa kwambiri kulambira koyera. Zimenezi zikuonekera bwino pa zimene anayankha pamene Satana ankamuyesa kachitatu. N’chifukwa chake Yehova anasankha Yesu kuti akwaniritse maulosi okhudza kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera. (Chiv. 19:10) Yesu ndi amene anali woyenera kudzapulumutsa anthu a Mulungu ku ukapolo wauzimu n’kubwezeretsa kulambira koyera pamalo ake oyenera.

Kodi Muchita Chiyani?

17. N’chifukwa chiyani maulosi a m’Baibulo okhudza kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera amatisangalatsa kwambiri?

17 Kuphunzira maulosi a m’Baibulo okhudza kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera n’kosangalatsa komanso ndi kolimbitsa chikhulupiriro. Maulosi amenewa amatisangalatsa kwambiri chifukwa tikuyembekezera nthawi imene zolengedwa zonse zakumwamba ndi zapadziko lapansi, zidzalambire Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa mogwirizana. Maulosiwa amatipatsanso chiyembekezo chifukwa mfundo zina zolimbikitsa za m’Mawu a Mulungu zikupezeka m’maulosi amenewa. Tonsefe tikufunitsitsa titaona maulosi a Yehova akukwaniritsidwa kuphatikizapo kuukitsidwa kwa okondedwa athu, dziko lapansi laparadaiso komanso kudzakhala ndi moyo wathanzi kwamuyaya.​—Yes. 33:24; 35:5, 6; Chiv. 20:12, 13; 21:3, 4.

18. Kodi tiphunzira chiyani m’bukuli?

18 M’bukuli tikambirana maulosi ochititsa chidwi opezeka m’buku la Ezekieli. Ambiri mwa maulosi amenewa akunena za kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera. Tikambirananso mmene maulosi opezeka m’buku la Ezekieli akugwirizanirana ndi maulosi ena, mmene adzakwaniritsidwire kudzera mwa Khristu komanso mmene akutikhudzira ifeyo.​—Onani bokosi lakuti “Mfundo Zachidule za M’buku la Ezekieli.”

19. Kodi inuyo mwatsimikiza kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

19 Pamene Yesu anali m’chipululu cha Yudeya mu 29 C.E, Satana analephera pamene ankamuyesa kuti asiye kulambira koyera. Koma kodi tikanakhala ifeyo tikanatani? Kuposa ndi kale lonse, panopa Satana akufunitsitsa kuti atisiyitse kulambira koyera. (Chiv. 12:12, 17) Bukuli litithandiza kuti tizifunitsitsa kukana mayesero ochokera kwa Woipayo. Ndipo zolankhula komanso zochita zathu zizisonyeza kuti tikugwirizana ndi mawu akuti, “Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira.” Tikamachita zimenezi tidzakhala ndi mwayi woona cholinga cha ulemerero cha Yehova chikukwaniritsidwa. Cholinga chimenechi n’chakuti mogwirizana, aliyense kumwamba komanso padziko lapansi azilambira Yehova m’njira yoyenera komanso kuchokera pansi pamtima. Kulambira kumeneku ndi kumene Yehova amafunikira.

a Anthu ena amaona kuti dzina lakuti Yehova limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhala.” Tanthauzo limeneli likugwirizana ndi udindo wa Yehova monga Mlengi komanso Wokwaniritsa zolinga zake.

b Pofotokoza za mawu a Satanawa buku lina lofotokozera Baibulo linanena kuti: “Mofanana ndi mmene zinalili pa mayesero oyambirira amene Adamu ndi Hava analephera . . . , nkhani yagona pa kusankha pakati pa kuchita zimene Satana amafuna kapena kuchita zimene Mulungu amafuna, zomwe zikutanthauza kuti munthu akuyenera kusankha mmodzi woti azimulambira. Satana amafuna kuti anthu azimulambira m’malo molambira Mulungu yekha.”

c Zikuoneka kuti Mateyu anafotokoza mayeserowa potsatira ndondomeko ya mmene anachitikira, koma Luka analemba Uthenga Wabwino potsatira ndondomeko yosiyana ndi imeneyi. Tikutero chifukwa cha zifukwa zitatu zotsatirazi: (1) Pofotokoza mayesero achiwiri, Mateyu anayamba ndi mawu akuti “kenako,” kusonyeza kuti anali atafotokoza kale mayesero ena. (2) N’zomveka kunena kuti mayesero awiri osaonekerawo, amene akuyamba ndi mawu akuti, “Ngati ndinu mwana wa Mulungu,” akutsatana ndi mayesero oonekeratu ofuna kumuchititsa kuti aphwanye lamulo loyamba. (Eks. 20:2, 3) (3) Komanso n’zomveka kunena kuti mawu a Yesu akuti “Choka Satana!” anawanena pambuyo pa mayesero achitatu komanso omaliza.​—Mat. 4:5, 10, 11.