Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

BOKOSI 4A

“Ndinkayangʼana Angelowo”

“Ndinkayangʼana Angelowo”

N’zodziwikiratu kuti Ezekieli anaonapo zifaniziro zikuluzikulu za ng’ombe zamphongo zamapiko komanso mikango zomwe zinali ndi mitu ya anthu ataziimika kutsogolo kwa nyumba zachifumu komanso akachisi. Zifaniziro ngati zimenezi zinkapezeka paliponse kalero ku Asuri komanso ku Babeloniya. Mofanana ndi zimene aliyense angachite, Ezekieli ayenera kuti ankayang’anitsitsa modabwa zifaniziro zazikuluzi, zomwe zinali zazitali mamita pafupifupi 6. Komabe, ngakhale kuti zifanizirozi zinkaoneka zamphamvu, zinali zopanda moyo chifukwa zinali zogobedwa kuchokera kumwala.

Mosiyana ndi zimenezi, angelo 4 amene Ezekieli anaona m’masomphenya anali amoyo. Kumenekutu kunali kusiyana kwakukulu. Zimene Ezekieli anaonazi zinamukhudza kwambiri moti anatchula mawu oti angelo maulendo oposa 10 m’mawu oyamba a ulosi wake. (Ezek. 1:5-22) Masomphenya a angelo 4 amene ankayenda mogwirizana pansi pa mpando wachifumu wa Mulungu ayenera kuti anathandiza Ezekieli kumvetsa mfundo yoti Yehova ndi amene akulamulira zinthu zonse zimene analenga. Masiku anonso masomphenya amenewa amatithandiza kumvetsa kuti Yehova ndi wamkulu ndiponso wamphamvu komanso kuti ulamuliro wake ndi waulemerero.​—1 Mbiri 29:11.