Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
Bukuli likuthandizani kuti mupitirize kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo pa moyo wanu zimene zingachitse kuti Mulungu apitirize kukukondani.
Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova likulimbikitsa onse omwe amakonda Yehova kuti azitsanzira chitsanzo cha Yesu yemwe ankachita zinthu zomwe zinachititsa kuti Atate ake azimukondabe.
MUTU 1
Zimene “Kukonda Mulungu Kumatanthauza”
Baibulo limafotokoza m’mawu aafupi mmene tingachitire zimenezi.
MUTU 2
Kodi Mungatani Kuti Mukhalebe ndi Chikumbumtima Chabwino?
Kodi zingatheke munthu kukhala ndi chikumbumtima chimene sichikumutsutsa koma chili chodetsedwa pamaso pa Mulungu?
MUTU 3
Muzikonda Anthu Amene Mulungu Amawakonda
Yehova amasankha bwino anthu amene angakhale anzake, ifenso tichita chimodzimodzi.
MUTU 4
Kodi N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kulemekeza Ulamuliro?
TMalemba amasonyeza njira zitatu zimene Yehova amafuna kuti tizitsatira posonyeza kuti timamvera amene akutilamulira.
MUTU 5
Kodi Tingatani Kuti Tikhale Osiyana ndi Dzikoli?
Mawu a Mulungu amafotokoza njira 5 zimene tingasonyezere kuti ndife osiyana ndi dzikoli.
MUTU 6
Kodi Mungasankhe Bwanji Zosangalatsa Zabwino?
Mafunso atatu omwe angakuthandizeni kuti muzisankha mwanzeru.
MUTU 7
Kodi Mumalemekeza Moyo Ngati Mmene Mulungu Amachitira?
Kulemekeza moyo kumatanthauza zambiri osati kungopewa kupha munthu
MUTU 8
Mulungu Amakonda Anthu Oyera
Baibulo lingakuthandizeni kupewa makhalidwe omwe angapangitse kuti musakhale oyera pamaso pa Mulungu.
MUTU 9
“Thawani Dama”
Chaka chilichonse Akhristu ambiri masauzande ambiri amachita chiwerewere. Kodi inuyo mungatani kuti musagwere mumsampha umenewu?
MUTU 10
Ukwati Ndi Mphatso Yochokera Kwa Mulungu Wachikondi
Kodi mungatani kuti banja lanu lizidzayenda bwino? Ngati muli kale pabanja, kodi, kodi mungatani kuti likhalebe mpaka kalekale?
MUTU 11
“Ukwati Ukhale Wolemekezeka”
Pali mafunso 6 omwe angakuthandize kudzifufuza komanso kuti banja lanu liziyenda bwino.
MUTU 12
Muzilankhula Mawu “Olimbikitsa”
Zimene mumalankhula zikhoza kulimbikitsa ena kapena kuwafooketsa. Phunzirani kugwiritsa ntchito bwino mphatso ya kulankhula ngati mmene Yehova amafunira.
MUTU 13
Zikondwerero Zimene Mulungu Amadana Nazo
Zikondwerero komanso miyambo ina yomwe imaoneka ngati ndi yolemekeza Mulungu amanyansidwa nayo.
MUTU 14
Chitani Zinthu Zonse Moona Mtima
Kuti mukwanitse kuchita zinthu moona mtima ndi ena pali pali choyamba chimene muyenera kuchita.
MUTU 15
Sangalalani Chifukwa Chogwira Ntchito Mwakhama
Mayankho a mafunso 5 angakuthandizeni kudziwa ngati ndi zoyenera kulowa ntchito inayake.
MUTU 16
Tsutsani Mdyerekezi ndi Njira Zake
Timadziwa kuti Satana ali ndi mphamvu koma timapewa kuchita naye mantha kwambiri. Chifukwa chiyani?
MUTU 17
‘Dzilimbitseni Pamaziko a Chikhulupiriro Chanu Choyera Kopambana’
TPali zinthu zitatu zimene zingakuthandizeni kuti chikhulupirire chanu chilimbe zomwe zingathandize kuti Mulungu apitirize kukukondani.
ZAKUMAPETO
Mmene Tiyenera Kuchitira ndi Munthu Wochotsedwa
Kodi tifunikadi kumapeweratu anthu ochotsedwa?
ZAKUMAPETO
Kodi Mlongo Ayenera Kuvala Chinachake Kumutu pa Zochitika Ziti, Ndipo N’chifukwa Chiyani?
Baibulo limanena zinthu zitatu zimene mungaziganizire kuti mudziwe ngati mukufunika kumanga chinachake kumutu.
ZAKUMAPETO
Kuchitira Sailuti Mbendera, Kuvota Ndiponso Kugwira Ntchito Zosakhudzana ndi Usilikali
kodi ndi mfundo ziti za m’Malemba zimene zingatithandize kuti tikhale ndi chikumbumtima chabwino pankhani zimenezi?
ZAKUMAPETO
Tizigawo ta Magazi ndi Njira Zopangira Opaleshoni
Kungochita zinthu zochepa chabe mukhoza kuthana ndi mavuto okhudza chithandizo cha chipatala.
ZAKUMAPETO
Mungathe Kuthetsa Vuto Loseweretsa Maliseche
Kodi mungathane bwanji ndi khalidwe loipa limeneli?
ZAKUMAPETO
Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani Yothetsa Banja ndi Kupatukana
Kodi Baibulo limati munthu amene banja lake linatha angakhale ndi ufulu wokwatiwa kapena wokwatiranso panthawi iti?
ZAKUMAPETO
Kuthetsa Kusamvana pa Nkhani za Bizinezi
Kodi ndi zoyenera kuti Mkhristu asumire Mkhristu mnzake kukhoti?