Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 2

N’chifukwa Chiyani Timatchedwa Mboni za Yehova?

N’chifukwa Chiyani Timatchedwa Mboni za Yehova?

Nowa

Abulahamu ndi Sara

Mose

Yesu Khristu

Anthu ambiri amaganiza kuti Mboni za Yehova ndi dzina la chipembedzo chatsopano. Komabe zaka zoposa 2,700 zapitazo, Mulungu woona anatchula atumiki ake kuti “mboni zanga.” (Yesaya 43:10-12) M’mbuyomu chaka cha 1931 chisanafike, tinkadziwika ndi dzina lakuti Ophunzira Baibulo. Nanga n’chifukwa chiyani tinasintha n’kutenga dzina lakuti Mboni za Yehova?

Dzina lathu limathandiza anthu kuti adziwe Mulungu wathu. M’mipukutu yakale ya Baibulo, dzina la Mulungu lakuti Yehova linkapezekamo maulendo ambirimbiri. Koma m’Mabaibulo ambiri a masiku ano, dzinali linachotsedwamo ndipo anaikamo mayina aulemu akuti Ambuye kapena Mulungu. Komatu Mulungu woona anaulula kwa Mose dzina lake lenileni lakuti Yehova, ndipo anamuuza kuti: “Limeneli ndilo dzina langa mpaka kalekale.” (Ekisodo 3:15) Mwanjira imeneyi, iye anadzisiyanitsa ndi milungu ina yonse yonyenga. Choncho, ife timanyadira chifukwa chodziwika ndi dzina loyera la Mulungu.

Dzina lathu limasonyeza ntchito yathu yaikulu. Anthu ambirimbiri akale, kuyambira ndi munthu wolungama Abele, anachitira umboni zoti ankakhulupirira Yehova. Kwa zaka zambirimbiri, anthu enanso okhulupirika analowa m’gulu la ‘mtambo waukulu wa mboni’ umenewu. Ena mwa anthuwa anali Nowa, Abulahamu, Sara, Mose ndi Davide. (Aheberi 11:4–12:1) Mofanana ndi munthu amene amapereka umboni m’khoti wosonyeza kuti munthu winawake ndi wosalakwa, ndife otsimikiza ndi mtima wonse kuthandiza anthu kuti adziwe choonadi chokhudza Mulungu wathu.

Tikutsanzira Yesu. Baibulo limamutchula kuti “mboni yokhulupirika ndi yoona.” (Chivumbulutso 3:14) Yesu ananena yekha kuti anathandiza anthu ‘kudziwa dzina la Mulungu’ ndipo anapitiriza ‘kuchitira umboni choonadi’ cha Mulungu. ( Yohane 17:26; 18:37) Choncho, otsatira enieni a Khristu ayenera kudziwika ndi dzina la Yehova ndi kuthandiza anthu ena kuti alidziwe. Zimenezi ndi zomwe anthu a Mboni za Yehova akuyesetsa kuchita.

  • N’chifukwa chiyani Ophunzira Baibulo anatenga dzina lakuti Mboni za Yehova?

  • Kodi Yehova wakhala ali ndi mboni padziko lapansili kwa nthawi yaitali bwanji?

  • Kodi ndani amene ali Mboni yaikulu kwambiri ya Yehova?