PHUNZIRO 24
Kodi Ndalama Zothandizira pa Ntchito Yathu Yapadziko Lonse Zimachokera Kuti?
Chaka chilichonse gulu lathu limafalitsa ndi kugawira Mabaibulo ndi mabuku ena popanda mtengo uliwonse. Komanso timamanga ndi kukonza Nyumba za Ufumu ndi maofesi athu. Timathandizanso anthu ambiri omwe akutumikira pa Beteli, ndiponso amishonale, ndipo kukachitika tsoka timathandiza anthu omwe akhudzidwa. Ndiye mwina mungadabwe kuti, ‘Kodi ndalama zoyendetsera ntchito zonsezi zimachokera kuti?’
Sitiuza anthu kuti azipereka chakhumi, komanso sitiyendetsa mbale ya zopereka. Ngakhale kuti ndalama zomwe zimafunika pothandizira pa ntchito yolalikira n’zambiri, ife sitimapemphetsa ndalama kwa anthu. Zaka zoposa 100 zapitazi, magazini ya Nsanja ya Olonda inanena zoti timakhulupirira kuti Yehova ndi amene akutithandiza. Choncho “sitidzapemphetsa kwa anthu kapena kuwachonderera kuti athandize pa ntchito imeneyi,” ndipo sitinachitepo zimenezi pa zaka zonsezi.—Mateyu 10:8.
Ndalama zonse zimene timagwiritsa ntchito n’zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo. Anthu ambiri amayamikira ntchito yathu yophunzitsa Baibulo ndipo amapereka ndalama zothandizira pa ntchitoyi. Nawonso a Mboni amapereka ndalama zawo, zinthu zina zosiyanasiyana, komanso amagwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zawo pothandizira kuti chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lonse lapansi. (1 Mbiri 29:9) Ku Nyumba ya Ufumu komanso kumisonkhano yathu ikuluikulu kumakhala mabokosi a zopereka kuti aliyense aziponyamo zopereka zake ngati angakonde kutero. M’mayiko ena, abale amapereka zopereka zawo kudzera pawebusaiti ya jw.org. Nthawi zambiri, si anthu olemera amene amaponya ndalama m’mabokosiwa. Ambiri amakhala ngati mkazi wamasiye wosauka yemwe Yesu anamuyamikira ataponya timakobidi tating’ono, moponyamo zopereka m’kachisi. (Luka 21:1-4) Choncho nthawi zonse aliyense ‘amaika kenakake pambali’ n’cholinga choti adzapereke “mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake.”—1 Akorinto 16:2; 2 Akorinto 9:7.
Tili ndi chikhulupiriro choti Yehova apitiriza kulimbikitsa anthu kuti ‘azimulemekeza ndi zinthu zawo zamtengo wapatali’ ndi kupititsa patsogolo ntchito ya Ufumu n’cholinga choti chifuniro chake chikwaniritsidwe.—Miyambo 3:9.
-
N’chiyani chomwe chimasiyanitsa gulu lathu ndi zipembedzo zina?
-
Kodi ndalama zomwe anthu amapereka mwa kufuna kwawo zimagwiritsidwa ntchito bwanji?