Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

GAWO 5

Bwererani kwa ‘M’busa Wanu ndi Woyang’anira Moyo Wanu’

Bwererani kwa ‘M’busa Wanu ndi Woyang’anira Moyo Wanu’

Kodi inuyo mwakumanapo ndi mavuto ena amene atchulidwa m’kabukuka? Ngati ndi choncho, dziwani kuti simuli nokha. Atumiki a Mulungu ambirimbiri akale ndiponso a masiku ano akumanapo ndi mavuto ngati amenewa. Yehova anawathandiza ndipo akhoza kukuthandizaninso inuyo.

Yehova adzakulandirani bwino mukabwerera kwa iye

DZIWANI kuti Yehova adzakulandirani bwino mukabwerera kwa iye. Adzakuthandizani kuti musiye kuda nkhawa, kukhumudwa ndiponso kudziimba mlandu. Zikatero mudzakhala ndi mtendere mumtima n’kumatumikira Yehova limodzi ndi anzanu. Mudzafanana ndi Akhristu amene mtumwi Petulo anawalembera kuti: “Munali ngati nkhosa zosochera, koma tsopano mwabwerera kwa m’busa wanu ndi woyang’anira miyoyo yanu.”—1 Petulo 2:25.

Mudzachita bwino kwambiri mukabwerera kwa Yehova. Tikutero chifukwa chakuti mudzakondweretsa mtima wake. (Miyambo 27:11) Kumbukirani kuti Yehova amatha kukhumudwa kapena kusangalala chifukwa cha zochita zathu. Koma iye satikakamiza kumukonda ndiponso kumutumikira. (Deuteronomo 30:19, 20) Katswiri wina wa Baibulo anati: “Palibe munthu amene angatsegule mtima wa munthu wina. Aliyense amatsegula wake.” Ndiyeno tikamatumikira Yehova chifukwa chomukonda kwambiri zimakhala ngati tasankha kutsegula mtima wathu. Munthu amene wachita zimenezi amakhala atapereka kwa Mulungu mphatso yamtengo wapatali ndipo izi zimamusangalatsa kwambiri. Paja Yehova ndi woyenera kulambiridwa choncho palibe chosangalatsa kuposa kumupatsa zimene ayenera kulandira.—Machitidwe 20:35; Chivumbulutso 4:11.

Mukabwerera kwa Yehova mudzapezanso zosowa zanu zauzimu. (Mateyu 5:3) Anthu ambiri padzikoli sadziwa cholinga cha moyo. Amafunitsitsa kupeza mayankho pa nkhaniyi ndipo izi n’zomveka chifukwa Yehova anatilenga ndi mtima wofuna kudziwa zimenezi. Mtima wathuwo umakhala wosangalala kwambiri ngati tikutumikira Yehova chifukwa chomukonda.—Salimo 63:1-5.

Musakayikire zoti Yehova amafunitsitsa kuti mubwerere. Kabukuka kanakonzedwa pambuyo popemphera ndipo ndi umboni wakuti Yehova akukuitanani. N’kutheka kuti mkulu wina kapena Mkhristu wina ndi amene anakupatsani. Ndiyeno inuyo munaona kuti ndi bwino kukawerenga n’kutsatira malangizo ake. Zonsezi zikungosonyeza kuti Yehova sanakuiwaleni. Zili ngati akukukokani mokoma mtima kuti mubwerere.—Yohane 6:44.

N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova saiwala atumiki ake amene asochera. Mlongo wina dzina lake Donna anatsimikizira mfundo imeneyi. Iye anati: “Ndinayamba kusiya Yehova mwapang’onopang’ono. Koma nthawi zambiri ndinkaganizira lemba la Salimo 139:23, 24 lomwe limati: ‘Ndifufuzeni, inu Mulungu, ndi kudziwa mtima wanga. Ndisanthuleni ndi kudziwa malingaliro anga amene akundisowetsa mtendere, ndipo muone ngati mwa ine muli chilichonse chimene chikundichititsa kuyenda m’njira yoipa, ndipo munditsogolere m’njira yamuyaya.’ Ndinkadziwa kuti ndiyenera kukhala m’gulu la Yehova osati m’dziko loipali. Ndinali ngati mlendo m’dzikoli. Ndiyeno ndinayamba kuona umboni wakuti Yehova sanandisiye. Chofunika chinali kubwerera kwa iye basi ndipo ndikusangalala kuti ndinabwereradi.”

“Ndinayamba kuona umboni wakuti Yehova sanandisiye.

Tikukhulupirira kuti inunso mupeza “chimwemwe chimene Yehova amapereka.” (Nehemiya 8:10) Mukabwerera simudzanong’oneza bondo ngakhale pang’ono.