DOMINICAN REPUBLIC
Ntchito Inayambika
Ntchito Yolalikira Inayambika
Lamlungu pa April 1, 1945, Lennart Johnson ndi mkazi wake Virginia anafika m’dziko la Dominican Republic. Iwo anali atangomaliza kumene maphunziro a ku Giliyadi ndipo anafika kulikulu la dzikoli lotchedwa Ciudad Trujillo (panopa ndi Santo Domingo). Iwo anali amishonale a Mboni za Yehova oyamba kufika m’dzikoli, lomwe m’mbuyomu munali nkhondo ndi chipwirikiti. * Mu Buku lapachaka la 1946 munali mawu akuti: “Apainiya ankafunika kwambiri m’dzikoli chifukwa kunalibe ngakhale wa Mboni mmodzi.” Amishonalewa anafika m’dziko limene munalibe ofesi ya nthambi, Nyumba za Ufumu kapena mipingo. Iwo sankadziwa aliyense m’dzikoli, sankadziwanso Chisipanishi ndipo analibe nyumba kapena katundu wa m’nyumba. Kodi iwo anachita chiyani?
M’bale Johnson anati: “Titafika tinapeza malo ogona kuhotelo ina. Ankatilipiritsa madola 5 pa tsiku kuti tigone komanso kudya komweko. Pa tsiku lomwelo, tinayambitsa phunziro la Baibulo. Zimene zinachitika n’zakuti azimayi awiri a ku Dominican Republic amene tinkaphunzira nawo ku Brooklyn anatipatsa mayina a achibale ndiponso anzawo. Wina anali Dr. Green ndipo tinakamupeza limodzi ndi mnzake wina dzina lake Moses Rollins. Titatchula anthu amene anatipatsa mayina awo, anamvetsera uthenga wathu ndipo anavomera kuphunzira. Pasanapite nthawi, Moses anakhala wofalitsa woyamba wa m’dzikoli.”
Amishonale ena 4 anafikanso m’dzikoli mu June 1945. Pasanathe nthawi yaitali, anagawira mabuku ambirimbiri
ndipo anayambitsa maphunziro a Baibulo ochuluka. Pofika mu October anaona kuti ankafunika malo ochitira misonkhano. Choncho analumikiza balaza ndi malo odyera a nyumba ya amishonale kuti apange Nyumba ya Ufumu. Nthawi zina anthu okwana 40 ankafika ku misonkhano.Munthu winanso amene anayamba kuphunzira anali Pablo Bruzaud koma ankadziwika ndi dzina lakuti Palé. Iye anali dalaivala wa basi imene inkayenda pakati pa mzinda wa Santiago ndi wa Ciudad Trujillo. Tsiku lina ali ku Ciudad Trujillo, iye analankhula ndi amishonale a Mboni ndipo anamugawira buku lakuti “The Truth Shall Make You Free.” Amishonalewo anayamba kumuphunzitsa Baibulo tsiku lililonse. Pasanapite nthawi yaitali, anayamba kulalikira limodzi ndi amishonalewo komanso ankawatenga pa basiyo. Pa nthawi ina, iye anakumana ndi M’bale Johnson ndipo anayenda limodzi ulendo wochokera ku Ciudad Trujillo kudutsa ku Santiago. Anadutsa m’mapiri n’kufika kutauni ya Puerto Plata, yomwe ili m’mphepete mwa nyanja. Ulendowu unali wokaona gulu la anthu limene linalemba kalata kulikulu lathu ku Brooklyn yopempha kuti athandizidwe kudziwa zambiri.
M’bale Knorr ndi M’bale Franz Anafika M’dzikoli
Mu March 1946, M’bale Nathan Knorr ndi M’bale Frederick Franz ochokera kulikulu lathu ku Brooklyn anafika m’dziko la Dominican Republic. Anthu ambiri ankayembekezera kufika kwawo moti pa nkhani imene M’bale Knorr anakamba, panafika abale ndi alongo komanso anthu ena 75. Pa ulendowu, M’bale Knorr anakonza zoti m’dzikoli mukhale ofesi ya nthambi.
Amishonale enanso anafika ndipo pofika kumapeto kwa chaka chautumiki cha 1946, m’dzikoli munali ofalitsa 28. Popeza ntchito yolalikira inali itangoyamba kumene, nthawi zambiri madzulo amishonale ankakonza
mapu a magawo a dzikoli n’cholinga choti azilalikira mwadongosolo.Ofalitsa Anawonjezeka
Pofika mu 1947, ku Dominican Republic kunali ofalitsa oposa 50. M’chaka chomwechi, amishonale ena amene anali ku Cuba anatumizidwa m’dzikoli. Pa gulu la amishonalewa panali Roy Brandt ndi mkazi wake dzina lake Juanita. Kenako M’bale Brandt anadzakhala mtumiki wa nthambi kwa zaka 10.
Pofika kumapeto kwa chaka chautumiki mu 1948, m’dzikoli munali ofalitsa pafupifupi 110 omwe ankalalikira limodzi ndi amishonalewa. Koma abalewa sankadziwa kuti mavuto aakulu adzayamba pasanapite nthawi yaitali.
^ ndime 1 Mabuku athu anayamba kufalitsidwa m’dziko la Dominican Republic cha m’ma 1932. Koma anthu anayamba kuphunzitsidwa Baibulo pamene banja la a Johnson linafika mu 1945.