Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

DOMINICAN REPUBLIC

Anamangidwa Ndipo Ntchito Yolalikira Inaletsedwa

Anamangidwa Ndipo Ntchito Yolalikira Inaletsedwa

Anamangidwa Chifukwa Chokana Kulowa Usilikali

Enrique Glass komanso ndende imene anakhalamo kwa milungu iwiri

Pa June 19, 1949, gulu la anthu a ku Dominican Republic, amene anathawa m’dzikoli anabwerera kuti achotse Rafael Trujillo pa mpando. Koma boma silinachedwe kuthana ndi anthu oukirawo. Ndiyeno anthu amene anakana kulowa usilikali, ngakhalenso amene boma linkawaona kuti ndi adani, anayamba kumangidwa. Pa gulu la anthu oyambirira kumangidwa, omwe anali a Mboni za Yehova, panali anyamata apachibale. Mayina awo anali León Glass, Enrique Glass, Rafael Glass ndiponso abale ena amene ankagwira ntchito ndi Leon.

León ananena kuti: “Gulu lachinsinsi la asilikali linandimanga ineyo ndi abale amene ndinkagwira nawo ntchito n’kuyamba kutifunsa mafunso komanso kutiopseza. Kenako anatimasula, koma patangopita masiku ochepa, tinaitanidwanso kuti akatilembe usilikali koma sanatsatire dongosolo lake. Titakana, anatitumiza kundende komwe tinapeza anthu ena 4 a Mboni ndipo awiri anali azichimwene anga. Patapita nthawi tinanasulidwa, koma kenako anatimanganso. Zimenezi zinachitika maulendo atatu, ndipo tikatulutsidwa pankangopita tsiku limodzi kapena angapo kenako n’kutimanganso. Ulendo womaliza tinakhala m’ndende zaka 5. Tikaphatikiza nthawi yonse imene tinakhala m’ndende imakwana zaka pafupifupi 7.”

‘Yehova anatipatsa mphamvu ndipo tinatha kupirira ngakhale pamene ankatikwapula ndiponso kutimenya ndi mfuti’

Abale ankakumana ndi mayesero osiyanasiyana kundende. Akaidi ena komanso asilikali olondera ndende ankakhalira kunyoza abalewo usana ndi usiku. Mwachitsanzo, mkulu wa asilikali olondera ndende ya Fort Ozama, ananyoza abale ponena kuti: “Inu a Mboni za Yehova, mukasintha n’kukhala mboni za Mdyerekezi mudzandiuze kuti ndikumasuleni.” Koma abalewo anapitirizabe kukhala okhulupirika. León anafotokoza zimene zinawachititsa kukhalabe okhulupirika. Iye anati: “Nthawi zonse tinkadalira Yehova ndipo anatithandiza. Tinkaoneratu kuti iye akutithandiza ngakhale pa zinthu zing’onozing’ono. Yehova anatipatsa mphamvu ndipo tinatha kupirira ngakhale pamene ankatikwapula ndiponso kutimenya ndi mfuti.”

Ntchito ya Mboni za Yehova Inaletsedwa

M’dziko lonseli a Mboni za Yehova ankazunzidwa kwambiri. Koma pofika mu May 1950, munali ofalitsa 238 osawerengera amishonale aja. Pa ofalitsa amenewa, 21 anali apainiya okhazikika.

Nkhani ya m’nyuzipepala yofotokoza za abale athu amene anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali

Pa nthawiyo, mkulu wina wa asilikali analemba kalata yopita kwa nduna ina mu ofesi ya pulezidenti. M’kalatayo anati: “A Mboni ajatu sakubwerera m’mbuyo. Akulalikira m’madera onse a mzindawu [Ciudad Trujillo].” Iye ananenanso kuti: “Amenewa tisangowasiyasiya chifukwa akamalalikira akusokoneza kwambiri maganizo a anthu, makamaka anthu wamba.”

Ndiyeno nduna yoona za m’dziko ndi apolisi, dzina lake J. Antonio Hungría anauza M’bale Brandt kuti alembe kalata. Anati m’kalatayo afotokoze maganizo a Mboni za Yehova pa nkhani ya usilikali, kulambira mbendera ndiponso kukhoma misonkho. M’baleyu analemba kalatayo ndipo mfundo zake anazitenga m’buku lakuti “Mulungu Akhale Woona.” Koma pa June 21, 1950, ndunayo inatulutsa chikalata choletsa ntchito ya Mboni za Yehova m’dzikoli. M’bale Brandt anaitanidwa ku ofesi ya a Hungría kuti akamve yekha za lamuloli. Ndiyeno M’bale Brandt anafunsa ngati amishonale ayenera kuchoka m’dzikolo. Ndunayo inanena kuti amishonalewo angakhale m’dzikolo ngati atavomereza kutsatira lamulolo komanso kusiya kulalikira. *

^ ndime 2 Kutatsala milungu ingapo kuti lamulo loletsa ntchito ya Mboni za Yehova liperekedwe, ansembe a Katolika ankalemba nkhani zitalizitali n’kumazifalitsa m’manyuzipepala. Nkhanizo zinali zonyoza a Mboni za Yehova komanso ankawanamizira kuti amagwirizana ndi oukira boma