MUTU 7
Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso ndi Moyo
-
Kodi n’chiyani chimatitsimikizira kuti akufa adzaukadi?
-
Kodi n’chiyani chimasonyeza kuti Yehova amafunitsitsa kuukitsa akufa?
-
Kodi ndi anthu otani amene adzaukitsidwe?
1-3. Kodi tonsefe tikuthamangitsidwa ndi mdani uti, ndipo n’chifukwa chiyani kukambirana zimene Baibulo limaphunzitsa kuli kothandiza?
TAYEREKEZANI kuti mukuthamangitsidwa ndi mdani woopsa kwambiri. Mdaniyo ndi wamphamvu komanso amadziwa kuthamanga kukuposani. Mumadziwa kuti ndi wankhanza chifukwa munamuonapo akupha anzanu ena. Mukuyesetsa kuthawa koma akuoneka kuti akukupezani. Mukuona kuti nthawi iliyonse akhoza kukugwirani. Kodi mungamve bwanji ngati mwadzidzidzi pafika munthu wodzakupulumutsani? Iye ndi wamphamvu kwambiri kuposa mdani wanuyo ndipo akulonjeza kuti akuthandizani.
2 Tinganene kuti aliyense panopa akuthamangitsidwa ndi mdani wangati ameneyu. Monga tinaphunzirira m’Mutu 6, Baibulo limanena kuti imfa ndi mdani wathu. Palibe munthu amene angathawe imfa kapena kulimbana nayo. Ambiri taonapo imfa ikupha achibale athu komanso anzathu. Koma Yehova ndi wamphamvu kwambiri kuposa imfa. Iye ndi Mpulumutsi wachikondi amene wasonyeza kale kuti akhoza kugonjetsa imfa. Ndipo analonjeza kuti adzawononga mdani ameneyu ndipo sadzapezekanso. Baibulo limaphunzitsa kuti: “Imfa . . . monga mdani womalizira, idzawonongedwa.” (1 Akorinto 15:26) Imeneyi ndi nkhani yosangalatsa kwambiri.
Yesaya 26:19) Izi zikusonyeza kuti anthu amene anamwalira adzaukitsidwa.
3 Choyamba tiyeni tikambirane mmene timamvera mnzathu kapena m’bale wathu akamwalira. Kukumbukira mmene timamvera kungatithandize kuyamikira zinthu zosangalatsa zimene Yehova adzachite. Yehova amalonjeza kuti akufa adzakhalanso ndi moyo. (MMENE TIMAMVERA WACHIBALE KAPENA MNZATHU AKAMWALIRA
4. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti mmene Yesu anamvera Lazaro atamwalira zikutiphunzitsa mmene Yehova amaonera imfa? (b) Kodi Yesu ankakonda kucheza ndi anthu ati?
4 Wachibale kapena mnzathu akamwalira timakhala ndi chisoni chachikulu komanso timathedwa nzeru. Zikatere tiyenera kudalira Mawu a Mulungu kuti atilimbikitse. (Werengani 2 Akorinto 1:3, 4.) Baibulo limatithandiza kudziwa mmene Yehova ndi Yesu amaonera imfa. Yesu, yemwe ankatsanzira makhalidwe a Atate ake, anamva chisoni mnzake atamwalira. (Yohane 14:9) Nthawi zambiri Yesu akakhala ku Yerusalemu ankakonda kupita kunyumba kwa Lazaro ndi alongo ake, Marita ndi Mariya, omwe ankakhala m’tawuni yotchedwa Betaniya. Yesu ankagwirizana kwambiri ndi anthu amenewa. Baibulo limati: “Yesu anali kukonda onsewa, Marita ndi m’bale wake, ndiponso Lazaro.” (Yohane 11:5) Koma monga mmene tinaphunzirira m’mutu wapitawu, patapita nthawi Lazaro anamwalira.
5, 6. (a) Kodi Yesu anachita chiyani atangoona achibale ndi anzake a Lazaro? (b) Timalimbikitsidwa bwanji tikamva kuti Yesu anagwidwa ndi chisoni?
5 Kodi Yesu anamva bwanji mnzake wapamtima atamwalira? Baibulo limatiuza kuti Yesu anapita kukakhala ndi achibale ndiponso anzake a Lazaro pa nthawi ya chisoniyi. Iye atangoona anthuwo, anakhudzidwa kwambiri moti “anadzuma povutika mumtima ndi kumva chisoni.” Ndipo Baibulo limapitiriza kufotokoza kuti: “Yesu anagwetsa misozi.” (Yohane 11:33, 35) Kodi Yesu anamva chisoni choncho chifukwa choti sadzaonananso ndi Lazaro? Ayi, iye ankadziwa kuti achita zinazake zosangalatsa. (Yohane 11:3, 4) Komabe anali ndi chisoni chifukwa ankadziwa mmene zimapwetekera munthu amene umam’konda akamwalira.
6 Timalimbikitsidwa tikamamva kuti Yesu anagwidwa ndi chisoni chifukwa zimatiphunzitsa kuti iyeyo limodzi ndi Atate ake, Yehova, amadana ndi imfa. Koma Yehova Mulungu ali ndi mphamvu zothetsa imfa imeneyi. Tiyeni tione zimene Mulungu anamuthandiza Yesu kuchita.
“LAZARO, TULUKA!”
7, 8. Malinga n’kuona kwa anthu, n’chifukwa chiyani zinkaoneka ngati panalibe chimene chikanachitika kwa Lazaro, koma kodi Yesu anachita chiyani?
7 Lazaro anaikidwa m’phanga n’kutsekapo ndi mwala waukulu. Yesu atafika paphangapo anauza anthu kuti achotse mwala umene anatsekerawo. Marita analetsa kuti asachite zimenezo chifukwa panali patadutsa masiku 4 chimuikireni m’manda, choncho ankaona kuti thupi la Lazaro linali litayamba kuwonongeka. (Yohane 11:39) Malinga n’kuona kwa anthu, palibenso chimene chikanachitika.
8 Mwalawo utachotsedwa, Yesu anafuula mwamphamvu kuti: “Lazaro, tuluka!” Ndiyeno kodi chinachitika n’chiyani? “Amene anali wakufa uja anatuluka.” (Yohane 11:43, 44) Tangoganizani mmene alongo ake, achibale komanso anzake anasangalalira kumuonanso Lazaro ali wamoyo. Ayenera kuti ankangoona ngati akulota chifukwa anali atatsimikiza kuti wamwaliradi. N’zodziwikiratu kuti ambiri anamukumbatira mosangalala. Pamenepatu imfa inali itagonjetsedwa.
9, 10. (a) Kodi Yesu anasonyeza kuti mphamvu zoukitsira Lazaro anazitenga kuti? (b) Kodi nkhani za m’Baibulo za anthu amene anaukitsidwa zimatithandiza bwanji?
9 Yesu sananene kuti anaukitsa Lazaro ndi mphamvu zake. M’pemphero limene anapereka asanaitane Lazaro, anasonyeza kuti Yehova ndi amene ali ndi mphamvu zoukitsa munthu. (Werengani Yohane 11:41, 42.) Komatu kameneka sikanali koyamba kuti Yehova aukitse munthu. Lazaro ndi mmodzi mwa anthu 9 otchulidwa m’Baibulo amene anaukitsidwa. * Nkhani zimenezi zimasangalatsa kwambiri ukamaziwerenga. Zimatiphunzitsa kuti Mulungu alibe tsankho chifukwa ena mwa anthu amene anaukitsidwawo anali ana, akuluakulu, amuna, akazi, Aisiraeli komanso anthu a mitundu ina. Nkhani zimenezi zimasonyeza kuti anthu ankasangalala kwambiri munthu akaukitsidwa. Mwachitsanzo, Yesu ataukitsa kamtsikana kena, makolo ake “anasangalala kwambiri.” (Maliko 5:42) Yehova anali atawachitira zinthu zosaiwalika.
10 N’zoona kuti anthu amene anaukitsidwa ndi Yesu anamwaliranso patapita nthawi. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti kuwaukitsa kunali kopanda phindu? Ayi, chifukwa nkhanizi zimatithandiza kutsimikizira zimene Baibulo limalonjeza zoti akufa adzauka.
ZIMENE TINGAPHUNZIRE PA NKHANI ZOKHUDZA ANTHU AMENE ANAUKITSIDWA
11. Kodi kuukitsidwa kwa Lazaro kumatsimikizira bwanji mfundo yopezeka pa Mlaliki 9:5?
11 Baibulo limanena kuti “akufa sadziwa chilichonse.” (Mlaliki 9:5) Iwo salinso ndi moyo kwinakwake komanso palibe chimene amadziwa. Nkhani ya Lazaro imatsimikizira zimenezi. Kodi Lazaro ataukitsidwa ankauza anthu zoti anali kumwamba ndipo waona zinthu zinazake zochititsa chidwi? Kapena ankawauza zinthu zoopsa zimene zimachitika kumoto? Ayi, Baibulo silifotokoza kuti Lazaro analankhulapo zinthu ngati zimenezi. Pa masiku onse 4 amene anali atamwalira, iye ‘sankadziwa chilichonse.’ Lazaro anali mu tulo ta imfa.—Yohane 11:11.
12. N’chifukwa chiyani sitingakayikire zoti Lazaro anaukitsidwadi?
12 Nkhani ya kuukitsidwa kwa Lazaro imatiphunzitsanso kuti nkhani yoti akufa adzauka ndi yoona, osati yongopeka. Yesu anaukitsa Lazaro pamaso pa anthu ambirimbiri. Ngakhale atsogoleri achipembedzo omwe ankadana ndi Yesu, sanatsutse zoti iye anaukitsadi Lazaro. M’malo mwake iwo anati: “Kodi tichite chiyani pamenepa, chifukwa munthu uyu [Yesu] akuchita zizindikiro zochuluka?” (Yohane 11:47) Ndipo anthu ambiri ankapita kukaona munthu amene anaukitsidwayo. Chifukwa cha zimenezi, anthu ambiri anayamba kukhulupirira Yesu. Akaona Lazaro ankaona umboni wosatsutsika woti Yesu anatumidwadi ndi Mulungu. Umboni umenewu unali wamphamvu kwambiri moti mpaka atsogoleri ena achiyuda anayamba kupangana zoti angopha Yesu ndi Lazaro yemwe.—Yohane 11:53; 12:9-11.
13. Kodi n’chiyani chimatitsimikizira kuti Yehova angathe kuukitsa akufa?
13 Kodi ndi nzeru kukhulupirira kuti akufa adzaukitsidwa? Inde, chifukwa Yesu ananena kuti tsiku lina “onse ali m’manda achikumbutso” adzaukitsidwa. (Yohane 5:28) Yehova ndi amene analenga zinthu zonse zamoyo. Ndiye kodi zingamuvute kuti alengenso moyo wa zinthu zimene zinafa? Komano kuti achite zimenezi akufunika kukhala ndi luso lokumbukira anthu amene anamwalirawo. Kodi iye angathe kukumbukira anzathu komanso abale athu amene anamwalira? Kumwamba kuli nyenyezi zosawerengeka, koma Mulungu amadziwa nyenyezi iliyonse ndi dzina lake lomwe. (Yesaya 40:26) Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova Mulungu angathe kukumbukira zonse zokhudza anthu amene anamwalira ndipo ndi wokonzeka kuwaukitsa.
14, 15. Malinga ndi zimene Yobu ananena, kodi n’chiyani chimasonyeza kuti Yehova amafunitsitsa kuukitsa akufa?
14 Koma kodi Yehova amafunadi kuukitsa akufa? Inde ndipo ndi zimene Baibulo limanena. Yobu anafunsa kuti: “Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo?” Yobu anatchula zoyembekezera m’manda mpaka itakwana nthawi imene Mulungu adzamukumbukire. Iye anauza Yehova kuti: “Inu mudzaitana ndipo ine ndidzayankha. Mudzalakalaka ntchito ya manja anu.”—Yobu 14:13-15.
15 Tangoganizani, Yehova amachita kulakalaka nthawi imene adzaukitse anthu akufa. Kodi si zosangalatsa kudziwa kuti Yehova amafunitsitsa kuukitsa akufa? Koma kodi ndi anthu otani omwe adzaukitsidwe, ndipo akadzaukitsidwa azidzakhala kuti?
“ONSE ALI M’MANDA ACHIKUMBUTSO”
16. Kodi akufa adzaukitsidwira padziko lapansi lotani?
16 Nkhani za m’Baibulo zonena za anthu amene anaukitsidwa zimatiphunzitsa zambiri zokhudza kuukitsidwa kwa anthu kumene kudzachitike m’tsogolo. Anthu amene anaukitsidwa m’mutu 3, Mulungu adzabwezeretsa paradaiso padziko lonse lapansili. Ndiye kuti akufa sadzaukitsidwira m’dziko la nkhondo, chiwawa komanso matenda. Choncho iwo adzakhala ndi mwayi wokhala ndi moyo wosatha padziko lapansi lamtendere.
m’mbuyomu anapitiriza kukhala ndi anzawo komanso achibale awo. Ndi mmenenso zidzakhalire pa kuukitsidwa kumene kukubwera kutsogoloku. Kungoti pa nthawiyi zinthu zidzakhala bwino kwambiri kuposa mmene zinalili nthawi imeneyo. Chifukwa monga mmene tinaphunzirira17. Kodi ndi ndani amene adzaukitsidwe?
17 Kodi ndi ndani amene adzaukitsidwe? Yesu ananena kuti “onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu ake [Yesu] ndipo adzatuluka.” (Yohane 5:28, 29) Komanso lemba la Chivumbulutso 20:13 limati: “Nyanja inapereka akufa amene anali mmenemo. Nayonso imfa ndi Manda zinapereka akufa amene anali mmenemo.” (Onani Zakumapeto, tsamba 212-213.) M’manda a anthu onse simudzakhalanso mtembo ngakhale umodzi. Anthu osawerengeka amene ali mmenemo adzakhalanso ndi moyo. Mtumwi Paulo ananena kuti: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” (Machitidwe 24:15) Kodi mawu amenewa akutanthauza chiyani?
18. Kodi “olungama” amene adzaukitsidwe akuphatikizapo ndani, nanga kudziwa kuti akufa adzauka kungakuthandizeni bwanji?
18 “Olungama” omwe adzaukitsidwe akuphatikizapo anthu ambiri amene timawawerenga m’Baibulo, omwe anakhala ndi moyo Yesu asanabwere padziko lapansi. Mwina mungakumbukire kuti kunali anthu ngati Nowa, Abulahamu, Sara, Mose, Rute, Esitere, ndi ena ambiri. Chaputala 11 cha Aheberi chimafotokoza zokhudza ena mwa amuna ndi akazi okhulupirika amenewa. Koma “olungama” amenewa akuphatikizaponso atumiki a Yehova amene amamwalira m’nthawi yathu ino. Chifukwa timadziwa kuti akufa adzauka, sitimaopa kufa.—Aheberi 2:15.
19. Kodi anthu “osalungama” ndi ati, nanga Yehova adzawapatsa mwayi wotani?
19 Koma nanga bwanji za anthu amene sanatumikire kapena kumvera Yehova chifukwa choti sanamudziwe? Anthu ambirimbiri Tsiku la Chiweruzo. *
“osalungama” amenewa sadzaiwalidwa. Adzaukitsidwa n’kupatsidwa mwayi woti aphunzire za Mulungu woona ndi kum’tumikira. Mkati mwa zaka 1,000, akufa adzaukitsidwa ndi kupatsidwa mwayi wotumikira Yehova limodzi ndi anthu okhulupirika padziko lapansi. Imeneyi idzakhala nthawi yosangalatsa kwambiri. Nthawi imeneyi ndi yomwe imatchulidwa m’Baibulo kuti20. Kodi Gehena n’chiyani, ndipo kumapita anthu otani?
20 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti anthu onse amene anamwalira adzaukitsidwa? Ayi. Baibulo limanena kuti akufa ena ali “m’Gehena.” (Luka 12:5) Dzina lakuti Gehena linachokera ku dzala linalake limene linali kunja kwa mzinda wakale wa Yerusalemu. Kumalo amenewa ndi komwe ankawotcherako zinyalala komanso mitembo ya anthu. Anthu amene mitembo yawo inkatayidwa kumeneko ndi omwe ankaonedwa ndi Ayuda ngati zigawenga zoopsa zosayenera kuikidwa m’manda mwadongosolo. Anthu amenewa ankawaonanso kuti sangaukitsidwe. Choncho dzina lakuti Gehena ndi loyenera kugwiritsidwa ntchito pofotokoza za anthu oipa amene sadzaukitsidwa. Ngakhale kuti Yesu ndi amene wapatsidwa udindo woweruza amoyo ndi akufa, Yehova ndi amene ali woweruza wamkulu. (Machitidwe 10:42) Iye sadzaukitsa anthu oipa omwe sakufuna kusintha.
ENA AMAUKITSIDWA KUTI AKAKHALE KUMWAMBA
21, 22. (a) Kodi anthu ena amene adzaukitsidwe adzakhala kuti? (b) Kodi ndi ndani anali woyamba kuukitsidwa monga mzimu?
21 Baibulo limanena kuti anthu ena amene adzaukitsidwe adzakhala ndi thupi lauzimu ndipo azidzakhala kumwamba. M’Baibulo muli chitsanzo chimodzi chokha cha munthu amene anaukitsidwa n’kupita kumwamba, yemwe ndi Yesu Khristu.
22 Yesu ataphedwa, Yehova sanalole kuti Mwana wake wokhulupirikayu akhalebe m’manda. (Salimo 16:10; Machitidwe 13:34, 35) Mulungu anaukitsa Yesu ndi thupi lauzimu. Mtumwi Petulo anafotokoza kuti Khristu “anaphedwa m’thupi, koma anaukitsidwa monga mzimu.” (1 Petulo 3:18) Chimenechi chinali chozizwitsa chachikulu kwambiri. Yesu anaukitsidwadi ndipo anakhalanso ndi moyo ngati munthu wauzimu wamphamvu. (Werengani 1 Akorinto 15:3-6.) Yesu anali munthu woyamba kuukitsidwa n’kupita kumwamba, koma si kuti ndi womaliza.—Yohane 3:13.
23, 24. Kodi anthu amene amatchulidwa kuti “kagulu kankhosa” ndi ndani, ndipo alipo angati?
23 Atatsala pang’ono kubwerera kumwamba, Yesu anauza otsatira ake okhulupirika kuti ‘akukawakonzera malo’ kumwambako. (Yohane 14:2) Iye amatchula anthu amene adzapite kumwamba kuti ndi “kagulu ka nkhosa.” (Luka 12:32) Kodi Akhristu okhulupirika amenewa adzakhalapo angati? Malinga ndi Chivumbulutso 14:1, mtumwi Yohane ananena kuti: “Nditayang’ana, ndinaona Mwanawankhosa [Yesu Khristu] ataimirira paphiri la Ziyoni. Limodzi naye panali enanso 144,000 olembedwa dzina lake ndi dzina la Atate wake pamphumi pawo.”
24 Akhristu 144,000 amenewa, omwe akuphatikizapo atumwi okhulupirika a Yesu, kuukitsidwa kwawo n’koti akakhale kumwamba. Koma kodi kuukitsidwa kwawo kudzachitika liti? Mtumwi Paulo analemba kuti kudzachitika m’nthawi ya kukhalapo kwa Khristu. (1 Akorinto 15:23) Panopa tili kale m’nthawi imeneyi ndipo tidzaphunzira zambiri m’Mutu 9. Choncho anthu ochepa otsala am’gulu la 144,000 amene amamwalira masiku ano, amaukitsidwa nthawi yomweyo n’kupita kumwamba. (1 Akorinto 15:51-55) Koma anthu ambiri amayembekezera kudzaukitsidwa m’tsogolo ndipo adzakhala m’Paradaiso padziko lapansi pompano.
25. Kodi tidzakambirana chiyani m’mutu wotsatira?
25 Zimenezi zikutitsimikizira kuti Yehova adzagonjetsadi imfa yomwe ndi mdani wathu ndipo sidzakhalaponso. (Werengani Yesaya 25:8.) Koma mwina mungakhale ndi funso lakuti, ‘Kodi anthu amene adzapite kumwambawo azikachita chiyani?’ Adzalamulira nawo mu Ufumu wakumwamba wa Mulungu. Tidzakambirana zambiri za Ufumu umenewu m’mutu wotsatira.
^ ndime 9 Nkhani za anthu ena amene anaukitsidwa zimapezeka pa 1 Mafumu 17:17-24; 2 Mafumu 4:32-37; 13:20, 21; Mateyu 28:5-7; Luka 7:11-17; 8:40-56; Machitidwe 9:36-42; ndi Machitidwe 20:7-12.
^ ndime 19 Kuti mudziwe zambiri zokhudza Tsiku la Chiweruzo ndiponso zimene Mulungu adzaone poweruza anthu ,onani Zakumapeto, tsamba 213-215.