Kodi Ndimagwiritsa Ntchito Zipangizo Zamakono Mopitirira Muyezo?
Mutu 36
Kodi Ndimagwiritsa Ntchito Zipangizo Zamakono Mopitirira Muyezo?
“Ndimakonda kwambiri kutumizirana mameseji ndi anzanga. Palibe chinthu chimene chimandikomera kuposa kutumizirana mameseji. Ndimangokhalira kutumizira anthu mameseji moti ndimalephera kuchita zinthu zina.”—Anatero Alan.
PA NTHAWI imene makolo anu anali achinyamata, zipangizo zamakono zimene zinalipo zinali TV ndi wailesi basi. Pa nthawi imeneyo kunalibe foni zam’manja. Foni zomwe zinalipo zinali zam’nyumba kapena muofesi basi (zagilaundi) zoti sungayende nazo ndipo zinali zongogwiritsa ntchito polankhulana ndi anthu osati potumizirana mameseji. Kodi mukuona kuti nthawi imeneyo moyo unali wotsalira? Mtsikana wina dzina lake Anna amaona choncho. Pofotokoza za makolo ake iye anati: “Zipangizo zamakono akuzionera kuukulu. Panopa m’pamene ayambano kudziwa mmene angagwiritsire ntchito zinthu zina zimene zili mufoni mwawo.”
Mafoni a masiku ano ndi aang’ono okwanira m’thumba ndipo ukangokhala ndi foni ukhoza kuimbira munthu wina, kumvetsera nyimbo, kuonera mafilimu, kusewera magemu, kutumizira anzako imelo, kujambula zithunzi komanso kufufuza zinthu pa intaneti. Mwina inuyo simuona vuto kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono kwa nthawi yaitali chifukwa mwakula pa nthawi imene kuli makompyuta, mafoni a m’manja, ma TV komanso intaneti. Koma makolo anu akhoza kumaona kuti mukugwiritsa ntchito zinthu zimenezi mopitirira malire. Ngati atakuuzani kuti zimene mukuchitazo zingakuikeni m’mavuto, musanyalanyaze poganiza kuti iwowo sakudziwa mmene moyo ukuyendera masiku ano. Mfumu yanzeru Solomo inanena kuti: “Munthu aliyense woyankhira nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa.”—Kodi mumadabwa kuti n’chifukwa chiyani makolo anu amada nkhawa ndi zimenezi? Yankhani mafunso ali m’munsiwa kuti muone ngati mwayamba kugwiritsira ntchito chipangizo chinachake mopitirira malire.
Dziyeseni Kuti Muone Ngati Mukugwiritsa Ntchito Zipangizozi Mopitirira Muyezo
Buku lina linafotokoza kuti tingati munthu akugwiritsa ntchito chinthu mopitirira malire ngati “ali ndi chizolowezi chochita zinthu kwa nthawi yaitali komanso mobwerezabwereza ndipo akulephera kapena sakufuna kusiya, ngakhale kuti akudziwa mavuto amene angakumane nawo ngati atapitiriza kuchita zinthuzo.” Tiyeni tikambirane zigawo za tanthauzo limeneli. Werengani zimene anthuwo anafotokoza ndiye muganizire ngati nanunso munanenapo kapena kuchita zofanana ndi zimenezozo. Kenako lembani mayankho anu m’mipatamo.
Kuchita zinthu kwa nthawi yaitali. “Ndinkasewera magemu pa kompyuta kwa nthawi yaitali moti pena zinkandilepheretsa kugona. Komanso ndikakhala ndi anzanga, nkhani zimene tinkakamba zinkangokhala zamasewerowa. Sindinkakonda kucheza ndi anthu kunyumba. Ndinkakomedwa kwambiri ndi
masewerawo moti ndinkangokhala kwandekha n’kumasewera ndekhandekha.”—Anatero Andrew.Kodi inuyo mukuganiza kuti ndi nthawi yaitali bwanji imene ili yoyenera kwa munthu kukhala akugwiritsa ntchito zipangizozi pa tsiku? ․․․․․
Kodi makolo anu amati muzigwiritsa ntchito zipangizozi kwa nthawi yaitali bwanji? ․․․․․
Phatikizani n’kulemba m’munsimu nthawi imene mumawononga pa tsiku potumizirana mameseji, kuonera TV, kuika zithunzi komanso ndemanga zanu pa intaneti, kusewera magemu a pa kompyuta ndiponso zinthu zina. ․․․․․
Mukaona zimene mwalemba pamwambapa, kodi munganene kuti mukugwiritsa ntchito zipangizozi mopitirira malire?
□ Inde □ Ayi
Kulephera kapena kusafuna kusiya. “Makolo anga amaona kuti ndimangokhalira kutumizirana mameseji ndi anzanga ndipo amandiuza kuti ndichepetse. Koma ndikaganizira mmene ana ena amsinkhu wanga amatumizira mameseji, ndimaona kuti mameseji amene ndimatumiza ine m’pang’ono. Ndi zoona kuti tikayerekezera ndi makolo anga, ineyo ndi amene ndimatumiza mameseji ambiri. Koma si bwino kundiyerekezera ndi makolo anga chifukwa iwowo ali ndi zaka 40 ine ndili ndi zaka 15. Sitingafanane, zili ngati kuyerekezera maapozi ndi malalanje.”—Anatero Alan.
Kodi makolo anu kapena anzanu anakuuzanipo kuti mumakhalitsa kwambiri pa foni, pa TV, pa kompyuta kapena pa intaneti?
□ Inde □ Ayi
Kodi mumalephera kapena simufuna kuchepetsa nthawi imene mumagwiritsa ntchito zipangizo zimenezi?
□ Inde □ Ayi
Mavuto amene mungakumane nawo. “Anzanga amakhalira kutumizirana mameseji ngakhale akamayendetsa galimoto. Ndimaona kuti zimenezi n’zoopsa kwambiri.”—Anatero Julie.
“Nditangokhala ndi foni yanga yoyamba ndinkangokhalira kuimbira anthu kapena kuwatumizira mameseji. Zimenezi zinachititsa kuti ndisamacheze ndi makolo anga, abale anga komanso anzanga ena. Panopa ndimaona kuti nthawi zambiri ndikakhala ndi anzanga n’kumacheza amandidula mawu amvekere: ‘Taima kaye. Ndikufuna ndiyankhe meseji.’ Zimenezi sizindisangalatsa moti n’chifukwa chake sindigwirizana kwambiri ndi anthu amene amachita zimenezi.”—Anatero Shirley.
Kodi mumawerenga kapena kutumiza mameseji mukamayendetsa galimoto, mukakhala m’kalasi kapena mukakhala pamisonkhano yachikhristu?
□ Inde □ Ayi
Mukamalankhula ndi makolo anu, abale anu kapena anzanu, kodi mumakondanso kuyankha maimelo, mafoni kapena mameseji?
□ Inde □ Ayi
Kodi mumagwiritsa ntchito zipangizo zamakono kwa nthawi yaitali moti mumalephera kugona mokwanira kapena kuwerenga?
□ Inde □ Ayi
Kodi mukuona kuti mukufunika kusintha penapake? Ngati ndi choncho, ganizirani mfundo zotsatirazi.
Njira Yabwino Yogwiritsa Ntchito Zipangizozi
Ngati mumagwiritsa ntchito zipangizo zamakono, ngati kompyuta kapena foni ya m’manja, dzifunseni mafunso 4 otsatirawa. Kutsatira malangizo ochokera m’Baibulo omwe ali m’munsi mwakewo komanso mfundo zina kukuthandizani kuti muzigwiritsa ntchito zipangizozi moyenera.
● Kodi mumakambirana zotani? “Zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambiri, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zachikondi, zilizonse zoyamikirika, khalidwe labwino lililonse, ndi chilichonse chotamandika, pitirizani kuganizira zimenezi.”—✔ Muzicheza ndi anzanu komanso achibale anu ndipo muzikambirana nawo zinthu zolimbikitsa.—Miyambo 25:25; Aefeso 4:29.
X Musamafalitse nkhani zabodza zonena anthu ena, kutumizirana mameseji kapena zithunzi zolaula, komanso kuonera mavidiyo kapena mapulogalamu olaula a pa TV.—Akolose 3:5; 1 Petulo 4:15.
● Kodi ndikugwiritsa ntchito zipangizozi nthawi yanji? “Chilichonse chili ndi nthawi yake.”—Mlaliki 3:1.
✔ Muziika malire a nthawi imene mungawononge poimba mafoni, potumizirana mameseji, poonera TV kapena posewera magemu.
X Musalole kuti kugwiritsa ntchito zipangizozi kusokoneze nthawi imene munaika yoti muziwerenga, kuchita zinthu zauzimu kapena kucheza ndi anzanu komanso abale anu.—Aefeso 5:15-17; Afilipi 2:4.
● Kodi ndikumacheza ndi ndani? “Musasocheretsedwe. Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.”—✔ Muzigwiritsa ntchito zipangizo zamakono munjira yoti zikuthandizeni kugwirizana kwambiri ndi anthu omwe angakulimbikitseni kukhala ndi makhalidwe abwino.—Miyambo 22:17.
X Musapusitsike. M’kupita kwa nthawi mudzatengera khalidwe, kalankhulidwe komanso kaganizidwe ka anthu amene mumacheza nawo kudzera pa intaneti, mameseji, imelo kapena amene mumaonera pa TV ndi m’mavidiyo.—Miyambo 13:20.
● Kodi ndimagwiritsa ntchito zipangizozi kwa nthawi yaitali bwanji? “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”—Afilipi 1:10.
✔ Muzilemba nthawi imene mumawononga pogwiritsa ntchito zipangizo zamakono.
X Musamanyalanyaze zimene anzanu angakuuzeni kapena malangizo amene makolo anu angakupatseni chifukwa choti akuona kuti mukumagwiritsa ntchito zipangizozi kwa nthawi yaitali.—Miyambo 26:12.
Pofotokoza za kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono, Andrew, yemwe tamutchula kumayambiriro kwa nkhaniyi, ananena kuti: “Kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono n’kosangalatsa koma zimakhala bwino ngati ukuzigwiritsa ntchito nthawi yochepa. Ndinaphunzira kugwiritsa ntchito zipangizozi mosamala kuti zisamandilepheretse kucheza ndi abale anga komanso anzanga.”
KUTI MUMVE ZAMBIRI PA NKHANIYI WERENGANI MUTU 30, M’BUKU LACHIWIRI
Kodi mungatani kuti makolo anu azikulolani kumapita kocheza nthawi zina?
LEMBA
“Usamadzione kuti ndiwe wanzeru. Uziopa Yehova ndi kupatuka pa choipa.”—Miyambo 3:7.
MFUNDO YOTHANDIZA
Kuti musamangokhalira pa foni, muziwauza anzanu kuti nthawi zina simungayankhe foni, mameseji kapena maimelo nthawi yomweyo.
KODI MUKUDZIWA . . . ?
Chilichonse chomwe mungalembe kapena zithunzi zomwe mungaike pa intaneti lero zidzakhalabe pomwepo moti anthu ena komanso anthu ofuna kukulembani ntchito akhoza kudzaziona ngakhale patapita zaka zambiri.
ZOTI NDICHITE
Ngati nditayamba kugwiritsa ntchito ․․․․․ mopitirira malire ndidzayesetsa kuika malire kuti ndizingoigwiritsa kwa maola ․․․․․ okha pa mlungu.
Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?
● N’chifukwa chiyani zingakhale zovuta kuti muzindikire zoti mukugwiritsa ntchito zipangizo zamakono mopitirira malire?
● Kodi chingachitike n’chiyani ngati mutalephera kudziikira malire pa mmene mumagwiritsira ntchito zipangizozi?
[Mawu Otsindika patsamba 262]
“Pali zinthu zingapo zimene zinandithandiza kuti ndisiye kumangokhalira kuonera TV. Ndinadzikakamiza kukhala ndi malire a nthawi imene ndingaonere TV. Ndinkakambirana ndi mayi anga pafupipafupi za vuto limeneli komanso ndinkapemphera kawirikawiri.”—Anatero Kathleen
[Chithunzi patsamba 263]
Kodi zipangizo zamakono zimakulamulirani kapena inuyo ndi amene mumazilamulira?