Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Ngati Makolo Anga Akwatiranso?

Kodi Ndingatani Ngati Makolo Anga Akwatiranso?

Mutu 5

Kodi Ndingatani Ngati Makolo Anga Akwatiranso?

N’KUTHEKA kuti makolo anu angakhale osangalala kwambiri pa tsiku limene akukwatiranso. Koma mwina inuyo simungakhale wosangalala. Izi zimachitika chifukwa kholo lanu likakwatiranso mumakhala mulibe chiyembekezo choti kholo lanu lomwe linachokalo lidzabwererananso ndi mayi kapena bambo anu. Kukwatiranso kwa makolo kumakhala kopweteka kwambiri ngati kholo linalo langomwalira kumene ndipo munkalikonda.

Kodi inuyo munamva bwanji bambo kapena mayi anu atakwatiranso? Ikani chizindikiro ichi ✔ m’kabokosi kamene kakufotokoza mmene munamvera.

Kholo langa litakwatiranso . . .

□ Ndinasangalala

□ Ndinali ndi nkhawa

□ Ndinkaona kuti andilakwira

□ Ndinkadana ndi kholo londipezalo

□ Ndinkadziimba mlandu chifukwa ndinayamba kukonda kholo londipezalo

N’kutheka kuti munkadziimba mlandu chifukwa munkaona kuti mukufunika kumakondabe kholo lanu lomwe linachoka kapena kumwalira. Zimenezi zingakuchititseni kuti mulankhule kapena kuchita zinthu zomwe zingakuikeni m’mavuto.

Mwachitsanzo, mungamachite dala zinthu zovuta kuti muzisowetsa mtendere kholo lanu lokupezanilo. Mwina mungamawayambanitse dala makolo anuwo n’cholinga choti asiyane. Komatu mwambi wina umati: “Aliyense wochititsa nyumba yake kunyanyalidwa adzagwira mphepo,” kutanthauza kuti sangapindule chilichonse. (Miyambo 11:29) Si bwino kuti zimenezi zikuchitikireni. Pali zinthu zina zothandiza zomwe mungachite kuti mupirire. Taonani zina zomwe mungachite.

Vuto Loyamba: Kutsatira Zonena za Kholo Lokupezanilo

Kutsatira zonena za kholo lokupezani kumakhala kovuta. Akakuuzani kuti muchite zinazake mungamalakelake kungowauza kuti, ‘Inutu si bambo anga’ kapena ‘Inutu si mayi anga.’ N’zoona kuti mtima wanu ukhoza kukhala m’malo kwa kanthawi mukalankhula mawu amenewa koma zimasonyeza kuti mukuganiza mwachibwana.

Koma kutsatira zonena za kholo lokupezani kungasonyeze kuti mukutsatira mfundo ya m’Baibulo yakuti ‘mukhale aakulu msinkhu pa luntha la kuzindikira.’ (1 Akorinto 14:20) Choyenera kudziwa n’choti, kholo lanu lokupezanilo likugwira ntchito imene kholo lanu lenileni limayenera kugwira, choncho mufunika kulilemekeza.​—Miyambo 1:8; Aefeso 6:1-4.

Kholo lokupezanilo likamakulangizani nthawi zambiri umakhala umboni wakuti limakukondani komanso kukuderani nkhawa. (Miyambo 13:24) Yvonne, amene ali ndi zaka 18, anati: “Bambo athu otipeza amatilangiza ndipo ndimaona kuti n’zimene bambo aliyense ayenera kuchita. Choncho, ndimaona kuti ngati nditapanda kutsatira malangizo awo zingasonyeze kuti sindikuyamikira zimene akhala akuchita potisamalira mwakuthupi komanso mwauzimu.”

Komabe n’kutheka kuti pangakhale zifukwa zomveka zokupangitsani kukhumudwa ndi zochita zawo. Ngati ndi choncho, mungasonyeze kuti ndinu ‘wamkulu msinkhu’ potsatira zimene lemba la Akolose 3:13 limanena. Lembali limati: “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake.”

Lembani m’munsimu makhalidwe abwino awiri kapena angapo omwe kholo lanu lokupezanilo lili nawo.

․․․․․

Kodi kukumbukira makhalidwe abwino amene mayi kapena bambo anu okupezani ali nawo kungakuthandizeni bwanji kuti muziwalemekeza?

․․․․․

Vuto Lachiwiri: Kuphunzira Kuchita Zinthu ndi Banja Latsopanolo

Mnyamata wina wazaka 24, dzina lake Aaron, ananena kuti: “Bambo anga atakwatiranso kachiwiri, banja lawo linatha ndipo anakwatiranso. Ndinkavutika kuti ndiyambe kukonda mayi anga ondipezawo ndi ana awo. Poyamba ndinkachita nawo chilendo koma ankandikakamiza kuti ndiziwakonda. Zimenezi zinkandisokoneza maganizo.”

N’kutheka kuti inunso mukukumana ndi mavuto enaake. Mwachitsanzo, mwina poyamba mwana wamkulu m’banjamo munali inuyo kapena mwana munalipo nokha. Ngati ndinu mnyamata, n’kutheka kuti ndinu amene mwakhala mukutsogolera zinthu pakhomopo kwa nthawi yaitali koma tsopano udindo umenewu wakhala wa bambo okupezaniwo. Kapena mukukumana ndi vuto limene Yvonne anakumana nalo. Iye anati: “Bambo anga ondibereka sankacheza kwambiri ndi mayi anga ndiye mayi anga ankangocheza ndi ineyo basi. Koma mayi anga atakwatiwanso, bambo ondipezawo ankacheza nawo kwambiri. Nthawi zambiri ankakhala limodzi n’kumacheza ndipo ndinkaona kuti andilanda munthu amene ndinkacheza naye. Koma m’kupita kwa nthawi ndinazolowera.”

Kodi inuyo mungatani kuti muyambe kuchita zinthu bwinobwino ndi banja latsopanolo? Baibulo limatilangiza kuti: “Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.” (Afilipi 4:5) Mawu amene anawamasulira kuti ‘kulolera’ amanena za munthu amene sakakamira kwambiri ufulu wake. Kodi inuyo mungatsatire bwanji malangizo amenewa? (1) Musamaganizire kwambiri za moyo wanu wakale. (Mlaliki 7:10) (2) Mukhale okonzeka kugawana komanso kuchitira limodzi zinthu ndi anthu a m’banja latsopanolo. (1 Timoteyo 6:18) (3) Musamawaone ngati alendo.

Kodi inuyo mukuona kuti mukufunika kuyesetsa kutsatira mfundo iti pa mfundo zomwe tazitchula pamwambazi? ․․․․․

Vuto Lachitatu: Kuona Kuti Kholo Latsopanolo Likukondera Ana Ake

Mtsikana wina, dzina lake Tara, ananena kuti: “Bambo anga ondipeza ankakonda kwambiri ana awo kusiyana ndi mmene ankandikondera ineyo ndi mchemwali wanga. Ankawagulira chakudya chilichonse chomwe akufuna komanso kuwabwerekera mafilimu amene akufuna kuonera. Ankawachitira zambiri n’cholinga choti azisangalala.” Zimakhala zopweteka ngati kholo lokupezani likuchita zimenezi. Koma kodi n’chiyani chingakuthandizeni ngati mukukumana ndi vuto limeneli? Yesani kuganiza chifukwa chake kholo lokupezanilo likukonda kwambiri ana ake kuposa ana owapeza. N’kutheka kuti bambowo akuchita zimenezi chifukwa chakuti anawo akhala nawo limodzi kwa nthawi yaitali osati chifukwa chakuti ndi ana obereka yekha. Ndipotu n’kutheka kuti nanunso mumakonda kwambiri kholo lanu lokuberekani kuposa kholo lanu lokupezanilo.

Komanso n’kutheka kuti ngakhale kuti amakukondani mosiyana, nonse amakusamalirani bwinobwino. Munthu aliyense amakhala ndi khalidwe losiyana ndi mnzake komanso amasiyana pa zinthu zimene amafuna pa moyo wake. Choncho, m’malo moganizira kwambiri kuti kholo lanu lopezalo silikukondani kwambiri, ndi bwino kuganizira ngati limayesetsa kukupezerani zonse zomwe mumafunikira pa moyo wanu.

Kodi ndi zinthu ziti zofunikira pa moyo wanu zomwe kholo lanu lopeza limakupatsani?

․․․․․

Nanga ndi zinthu ziti zomwe mumaona kuti samakuchitirani?

․․․․․

Ngati mukuona kuti pali zinthu zina zofunika zomwe kholo lanulo silikuchitirani, mungachite bwino kukambirana nawo mwaulemu.

Kuona Maso a Nkhono N’kudekha

Nthawi zambiri pamapita zaka kuti anthu a m’banja lopeza ayambe kudalirana komanso kuchitira limodzi zinthu momasuka. Kenako amazolowerana makhalidwe n’kumachita zinthu bwinobwino. Choncho dekhani. Musaganize kuti zinthu zingangosintha kamodzin’kamodzi n’kuyamba kukondedwa komanso kuchita zinthu mogwirizana.

Mnyamata wina, dzina lake Thomas, anali ndi nkhawa mayi ake atakwatiwanso. Mayi ake anali ndi ana 4 pamene mwamuna amene anakwatiwa naye anali ndi ana atatu. Thomas ananena kuti: “Tinkamenyana, kukangana ndiponso kukwiyitsana.” Koma kodi n’chiyani chinawathandiza kuti m’kupita kwa nthawi ayambe kukhala mwamtendere? Iye anati: “Zinthu zinayamba kuyenda bwino chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo.”

M’MUTU WOTSATIRA

Kodi mungatani ngati mumayambana kwambiri ndi abale anu abere limodzi?

LEMBA

“Mapeto a chinthu amakhala bwino kuposa chiyambi chake, ndipo munthu woleza mtima ndi wabwino kuposa munthu wodzikuza.”​—Mlaliki 7:8.

MFUNDO YOTHANDIZA

Ngati ndinu mtsikana, kukhala limodzi ndi anyamata omwe siinu a bere limodzi n’kovuta. N’zotheka kuyamba kufunana, choncho muyenera kuphunzitsa maganizo anu kuti muziwaona ngati abale anu enieni. Muzichita zinthu komanso kuvala modzilemekeza.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

N’kutheka kuti ana a kholo lanu lokupezanilo nawonso akuvutika kuti azolowere moyo wa m’banja latsopanolo.

ZOTI NDICHITE

Ndikufuna kuti ndizilemekeza kwambiri bambo kapena mayi anga ondipeza pokumbukira zinthu zabwino zimene achitira banja lathu (lembani zinthu ziwiri zabwino zomwe achita): ․․․․․

Ngati abale anga ondipeza akundipewa ndingachite izi potsatira mfundo ya pa Aroma 12:21: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa kholo londibereka kapena londipeza pa nkhaniyi: ․․․․․

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

● Kodi kholo lanu lokupezani kapena abale anu okupezani angamaope zinthu ziti pamene akubwera kudzakhala nanu?

● N’chifukwa chiyani si bwino kuchitira chipongwe kholo kapena abale anu okupezani?

[Mawu Otsindika patsamba 38]

“Mayi anga atakwatiwa ndi mwamuna wina m’kupita kwa nthawi banjalo linathanso. Koma mpaka pano ndimagwirizana kwambiri ndi ana a bambo ondipezawo. Ndimanyadira kwambiri kuti ndinakhala ndi mwayi wodziwana nawo.”​—Anatero Tara

[Chithunzi patsamba 39]

Kuti mabanja awiri ayambe kukhalira limodzi bwinobwino zimatenga nthawi komanso zimafuna khama ngati mmene zimakhalira posakaniza madzi ndi simenti. Koma pamapeto pake mumapanga chinthu cholimba kwambiri