Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingapeze Bwanji Anzanga Abwino?

Kodi Ndingapeze Bwanji Anzanga Abwino?

Mutu 8

Kodi Ndingapeze Bwanji Anzanga Abwino?

“Ndikakwiya ndimafuna munthu woti ndimuuze mmene ndikumvera. Ndikakhumudwa ndimafuna munthu woti andilimbikitse. Ndikasangalala ndimafuna munthu amene angasangalale nane. Ineyo ndimaona kuti munthu aliyense amafunika kukhala ndi anzake.”​—Anatero Brittany.

PAMENE munali mwana munkafuna ana ena kuti muzisewera nawo. Koma panopo mumafuna mutakhala ndi mnzanu wapamtima, amene mukhoza kumacheza naye komanso kuchita naye zinthu limodzi.

Komanso Baibulo limanena kuti “bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo ilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.” (Miyambo 17:17) Zimenezi zikusonyeza kuti mnzanu wapamtima amakhala wapadera kwambiri.

Mfundo yofunika: Mukamakula mumafuna kukhala ndi anzanu omwe

1. Ali ndi makhalidwe abwino

2. Amatsatira mfundo zabwino pa moyo wawo

3. Akhoza kukuthandizani kuchita zinthu zabwino

Funso: Kodi mungapeze bwanji anzanu oti ali ndi zinthu zitatu zomwe tatchulazi? Tiyeni tikambirane chimodzi ndi chimodzi.

Choyamba: Makhalidwe Abwino

Zimene muyenera kudziwa. Sikuti aliyense amene amati ndi mnzanu amakhala mnzanu wapamtima, chifukwa ngakhale Baibulo limati: “Pali mabwenzi amene amafuna kuthyolana.” (Miyambo 18:24) Mwina mungaganize kuti lembali likukokomeza. Koma taganizirani izi: Kodi munakhalapo ndi mnzanu yemwe ankaoneka ngati amakukondani koma cholinga chake chinali choti angopeza zimene akufuna? Kapena munakhalapo ndi mnzanu woti ankakujedani kapena ankakakunenerani zinthu zabodza kwa anthu ena? Zimenezi zikhoza kukuchititsani kuti musamakhulupirirenso anzanu. * Ndiyetu nthawi zonse muzikumbukira kuti ndi bwino kukhala ndi anzanu ochepa odalirika kusiyana n’kukhala ndi anzanu ambiri koma osadalirika.

Zimene mungachite. Muzicheza ndi anthu amakhalidwe omwe mungakonde kutengera.

“Ndili ndi mnzanga, dzina lake Fiona. Aliyense amaona kuti ndi munthu wa makhalidwe abwino. Inenso ndimafuna kuti anthu aziona kuti ndine munthu wa makhalidwe abwino. Limeneli ndi khalidwe losiririka kwambiri.”​—Anatero Yvette, wazaka 17.

Tachitani izi.

1. Werengani Agalatiya 5:22, 23.

2. Dzifunseni kuti, ‘Kodi anzanga ali ndi “makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa”?’

3. Lembani m’munsimu mayina a anzanu amene mumacheza nawo kwambiri. Ndiyeno lembani khalidwe limene mnzanu aliyense amadziwika nalo.

Dzina Khalidwe

․․․․․ ․․․․․

Dziwani izi: Ngati anzanuwo amadziwika ndi makhalidwe oipa, pezani anzanu ena odziwika ndi makhalidwe abwino.

Chachiwiri: Mfundo Zabwino Zimene Amatsatira

Zimene muyenera kudziwa. Munthu akamafuna kupeza anzake ocheza nawo mwamsanga m’pamene amapeza anzake a makhalidwe oipa. Baibulo limanena kuti: “Wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.” (Miyambo 13:20) Mawu akuti “anthu opusa” sakutanthauza anthu amene sakhoza kusukulu kapena anthu opanda nzeru. Mawu amenewa amanena za anthu amene satsatira mwadala mfundo za makhalidwe abwino. Anthu oterewa sangakhale anzanu abwino.

Zimene mungachite. M’malo momangocheza ndi munthu wina aliyense, muzisankha anthu ocheza nawo. (Salimo 26:4) Koma zimenezi sizikutanthauza kuti muzichita zinthu mwatsankho. Pamene tikunena kuti muzisankha, tikutanthauza kuti muzitha kusiyanitsa “pakati pa munthu wolungama ndi woipa ndiponso pakati pa munthu amene akutumikira Mulungu ndi amene sanatumikirepo Mulungu.”​—Malaki 3:18.

“Ndikuthokoza kwambiri makolo anga kuti anandithandiza kupeza anzanga amsinkhu wanga amene amakonda zinthu zauzimu.”​—Anatero Christopher, wazaka 13.

Yankhani mafunso ali m’munsiwa:

Kodi ndikakhala ndi anzanga ndimachita mantha kuti andikakamiza kuchita zinthu zimene ndikudziwa kuti n’zoipa?

□ Inde

□ Ayi

Kodi sindifuna kupita ndi anzanga kunyumba chifukwa ndimaopa kuti makolo anga andiletsa kuti ndisamacheze nawo?

□ Inde

□ Ayi

Dziwani izi: Ngati mwayankha kuti inde pa mafunso ali pamwambawa, pezani anzanu amene amatsatira mfundo za makhalidwe abwino, omwe ndi Akhristu a chitsanzo chabwino.

Chachitatu: Kukuthandizani Kuchita Zinthu Zabwino

Zimene muyenera kudziwa. Baibulo limati: “Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.” (1 Akorinto 15:33) Mtsikana wina, dzina lake Lauren, ananena kuti: “Anzanga akusukulu ankagwirizana nane ndikamachita zimene iwowo akufuna. Nthawi imeneyo ndinkasowa wocheza naye ndiye ndinkangochita zimene akufuna kuti ndipeze ocheza nawo.” Lauren anazindikira kuti ukamangotsatira mfundo za anthu ena, umangokhala ngati kachidole kawo ndipo amakuseweretsa mmene akufunira. Koma si mmene ziyenera kukhalira.

Zimene mungachite. Siyani kucheza ndi anthu amene amakukakamizani kuti muzitsatira zimene iwowo amachita. N’zoona kuti mukachita zimenezi mukhoza kukhala ndi anzanu ochepa koma muzikhala osangalala. Ndipo mudzapeza anzanu abwino amene angakulimbikitseni kuchitanso zinthu zabwino.​—Aroma 12:2.

“Mnzanga wapamtima, dzina lake Clint, amaganiza bwino ndipo ndi munthu wachifundo. Chifukwa chakuti ali ndi makhalidwe amenewa amandilimbikitsa kwambiri.”​—Anatero Jason, wazaka 21.

Yankhani mafunso ali m’munsiwa:

Kodi ndimasintha kavalidwe, mmene ndimalankhulira kapena kuchita zinthu zoipa pongofuna kusangalatsa anzanga?

□ Inde

□ Ayi

Kodi ndimapita ndi anzanga kumalo okayikitsa amene pandekha sindikanapita?

□ Inde

□ Ayi

Dziwani izi: Ngati mwayankha kuti inde pamafunso amenewa pemphani makolo anu kapena munthu wachikulire amene mumamudalira kuti akuthandizeni. Ngati ndinu wa Mboni za Yehova, mungapite kwa m’bale yemwe ndi mkulu ndipo muuzeni kuti akuthandizeni kusankha anzanu omwe angakulimbikitseni kuchita zabwino.

WERENGANI ZAMBIRI PA NKHANIYI M’MUTU 9 M’BUKU LACHIWIRI

M’MUTU WOTSATIRA

Kodi mungatani kuti musamakopeke ndi mtima wanu kapena ndi zochita za anzanu?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Chifukwa chakuti ndife ochimwa aliyense amalakwitsa zinthu. (Aroma 3:23) Choncho, mnzanu akachita zinthu zokukhumudwitsani n’kupepesa kuchokera pansi pamtima, muzikumbukira mfundo yakuti: “Chikondi chimakwirira machimo ochuluka.”​—1 Petulo 4:8.

LEMBA

“Pali bwenzi limene limamatirira kuposa m’bale wako.”​—Miyambo 18:24.

MFUNDO YOTHANDIZA

Ngati mumatsatira mfundo za makhalidwe abwino pa moyo wanu, mumayamba kugwirizana ndi anthu amene amatsatiranso mfundo zomwezo ndipo amakhala anzanu apamtima.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Mulungu alibe tsankho komabe amasankha anthu amene angakhale ‘alendo m’chihema chake.’​—Salimo 15:1-5.

ZOTI NDICHITE

Ndichita zotsatirazi kuti ndipeze anzanga abwino: ․․․․․

Anthu ena, omwe ndi aakulu kwa ineyo, omwe ndikufuna ndizicheza nawo ndi ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

● Kodi mumafuna kuti mnzanu azikhala ndi makhalidwe ati ndipo chifukwa chiyani?

● Kodi ndi makhalidwe ati amene mukufunika kusintha kuti mukhale munthu wabwino?

[Mawu Otsindika patsamba 60]

“Nthawi ina makolo anga anandiletsa kucheza ndi anzanga enaake. Ndinkangoona ngati palibenso anthu ena omwe ndingamacheze nawo kupatulapo anzangawo. Makolo anga anandilangiza ndipo nditaganizira kwambiri zimene anandiuzazo, ndinazindikira kuti pali anthu ambiri omwe akhoza kukhalanso anzanga.”​—Anatero Cole.

[Bokosi patsamba 61]

Tayesani kuchita izi

Kambiranani ndi makolo anu. Afunseni kuti anali ndi anzawo otani ali msinkhu ngati wanuwo. Kodi panopa amadandaula kuti sanasankhe bwino anzawo ocheza nawo? Ngati amadandaula, amadandaula chifukwa chiyani? Afunseni zimene mungachite kuti mupewe mavuto amene iwowo anakumana nawo.

Makolo anu azidziwa anzanu amene mumacheza nawo. Ngati simufuna kuti makolo anu azidziwa anzanu amene mumacheza nawo, dzifunseni kuti, ‘N’chifukwa chiyani?’ Kodi pali zinazake zomwe anzanuwo amachita zimene makolo anu sangasangalale nazo? Ngati zilipo, muyenera kusankhanso anzanu ocheza nawo.

Muzimvetsera. Muzichita chidwi ndi zimene anzanu akuganiza, zimene zikuwachitikira komanso zimene zikuwadetsa nkhawa.​—Afilipi 2:4.

Muzikhululuka. Musamayembekezere kuti anzanu azichita zinthu zolondola nthawi zonse, chifukwa “tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.”​—Yakobo 3:2.

Muzipatsako anzanu mpata. Simufunika kumangowakakamira anzanu kulikonse komwe ali. Mnzako weniweni amakhalapo nthawi iliyonse yomwe akufunikira.​—Mlaliki 4:9, 10.

[Chithunzi patsamba 63]

Munthu akamangotsatira zimene anzake amachita amakhala ngati kachidole kawo ndipo amangomuseweretsa mmene akufunira