Chitsanzo Chabwino—Msulami
Chitsanzo Chabwino—Msulami
Mtsikana wachisulami ankadziwa kuti sayenera kungotengeka maganizo pankhani ya chikondi. Iye anauza anzake kuti: ‘Ndikulumbirirani . . . musautse, musagalamutse chikondi, chisanafune mwini.’ Msulamiyu anadziwa kuti munthu angalephere kuganiza bwino chifukwa chongotengeka maganizo. Mwachitsanzo, anazindikira kuti anthu ena akanatha kumulimbikitsa kukhala pachibwenzi ndi munthu amene sakuyenerana naye. Anazindikiranso kuti mtima wake ungamuchititsenso kusaganiza mwanzeru. Choncho Msulamiyu anapitiriza kukhala ngati “khoma.”—Nyimbo ya Solomo 8:4, 10.
Kodi ndinu wokhwima maganizo moti mumaona nkhani ya chikondi ngati mmene Msulami anali kuionera? Kodi mumayamba mwaganiza kaye musanachite zinthu kapena mumangotsatira zimene mtima wanu wafuna? (Miyambo 2:10, 11) Nthawi zina ena angakulimbikitseni kukhala pachibwenzi inuyo musanafike poti n’kuchita zimenezo. Zochita zanunso zingakulowetseni m’vuto limeneli. Mwachitsanzo, mukaona mnyamata ndi mtsikana akuyenda atagwirana manja, kodi nanunso mumalakalaka mutachita zimenezo? Kodi mungafune munthu amene si wachipembedzo chanu? Pankhani zachikondi, mtsikana wachisulami anali wokhwima maganizo. Inunso mungakhale wotero.