Chitsanzo Chabwino—Mkazi Wamasiye Wosauka
Chitsanzo Chabwino—Mkazi Wamasiye Wosauka
Yesu ali pa kachisi anaona gulu la anthu olemera akuponya ndalama zawo moponyamo zopereka. Kenako, anaona mkazi wina wamasiye wosauka akuponya “timakobili tiwiri tating’ono.” (Luka 21:2) Yesu anamuyamikira kwambiri mkaziyo chifukwa cha kuwolowa manja kwake. Chifukwa chiyani? Anthu ena onsewo anaponyamo ‘zimene anatapa pa zochuluka zimene anali nazo, koma mayiyo, mu umphawi wake, anaponya zonse zimene anali nazo, inde zonse zochirikiza moyo wake.’—Maliko 12:44.
Kodi inu mumaona zinthu ngati mmene mayiyu ankaonera? Kodi ndinu wofunitsitsa kugwiritsa ntchito nthawi ndiponso ndalama zanu potumikira Mulungu? Mofanana ndi mkazi wamasiye wosaukayu, mungapereke ndalama kapena kugwira nawo ntchito yosamalira malo olambirira Yehova. Mungagwiritsenso ntchito nthawi ndi ndalama zanu pothandiza ena kuphunzira za Yehova Mulungu. Yehova anaona ndalama zochepa zimene mkazi wamasiyeyo anapereka kuti zithandize pantchito yake ndipo anasangalala nazo. Nanunso, Mulungu adzasangalala nanu ndiponso adzakuthandizani ngati cholinga chanu chachikulu pamoyo ndi kuchita chifuniro chake.—Mateyo 6:33.