Chitsanzo Chabwino—Davide
Chitsanzo Chabwino—Davide
Davide ankakonda nyimbo. Iye anali ndi luso lopeka komanso kuimba nyimbo. Iye ankakonzanso yekha zida zake zoimbira. (2 Mbiri 7:6) Chifukwa cha luso la Davide, mfumu ya Isiraeli inamuitanitsa kuti azikaimba ku nyumba yake. (1 Samueli 16:15-23) Davide anavomera, koma sanalole kuti zimenezi zimuchititse kukhala wonyada, komanso kuti azingokhalira kuimba kokhakokha. M’malo mwake iye anagwiritsa ntchito luso lakelo kutamanda Yehova.
Kodi inuyo mumakonda nyimbo? Mwina simungakhale ndi luso loimba ngati Davide, komabe mungatsanzire chitsanzo chake. Kuti muchite zimenezi, musamangokhalira kumvetsera nyimbo nthawi zonse ndipo musalole kuti nyimbo zikusokonezeni maganizo n’kumachita zinthu zimene Mulungu amadana nazo. Koma muzimvetsera nyimbo n’cholinga choti musangalale. Luso lopeka komanso kusangalala ndi nyimbo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. (Yakobe 1:17) Davide ankagwiritsa ntchito luso limeneli kusangalatsa Yehova. Inunso mungathe kuchita zimenezi.