Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

INDONESIA

Ulamuliro Wankhanza wa Boma la Japan

Ulamuliro Wankhanza wa Boma la Japan

Kumayambiriro kwa chaka cha 1942, gulu la asilikali a ku Japan linalanda dziko la Indonesia n’kuyamba kulamulira mopondereza. Pa nthawiyi abale ambiri anamangidwa chifukwa chokana kumenya nawo nkhondo ndipo ankawagwiritsa ntchito yakalavulagaga. Nthawi zambiri ntchito yake inkakhala yokonza misewu ndi kukumba ngalande. Ena anawatsekera m’ndende zomwe zinali zauve komanso ankawazunza kwambiri moti abale atatu anafera kundende.

Mlongo Johanna Harp, ana ake awiri aakazi ndi mnzawo dzina lake Beth Godenze (yemwe ali pakati)

Kwa zaka ziwiri zoyambirira za nkhondoyo, mlongo wina wachidatchi, dzina lake Johanna Harp, sanamangidwe nawo. Iye ankakhala m’mudzi wina wakumapiri, womwe unali kwaokhaokha, ku East Java. Pa nthawiyi mlongoyu pamodzi ndi ana ake atatu anamasulira buku lakuti Salvation komanso magazini a Nsanja ya Olonda kuchoka m’Chingelezi kupita m’Chidatchi. * Zimene ankamasulirazo ankazikopera kenako n’kuzigawira kwa abale ndi alongo a ku Java mozemba.

Abale ndi alongo amene sanamangidwe pa nthawi ya nkhondoyi, ankasonkhana m’magulu ang’onoang’ono ndipo ankalalikira mosamala kwambiri. Mlongo Josephine Elias (yemwe poyamba anali Josephine Tan) ananena kuti: “Nthawi zonse ndinkafufuza mpata woti ndicheze ndi anthu, kwinaku ndikuwalalikira mosaonetsera. Nthawi zina ndinkanyamula kathabwa kamasewera a tchesi kuti anthu azingoganiza kuti ndikukasewera tchesi.” M’bale Felix Tan ndi mkazi wake Bola, ankanamizira kugulitsa sopo pamene ankalalikira khomo ndi khomo n’cholinga choti asagwidwe. M’baleyu ananena kuti: “Nthawi zambiri asilikali ankhanza a ku Japan omwe ankatchedwa Kempeitai ankatumiza anthu kuti azitilondola mwakabisira. Choncho kuti asatikayikire, tinkasinthasintha masiku komanso nthawi yochititsira maphunziro. Zimenezi zinathandiza kuti anthu 6 amene tinkaphunzira nawo pa nthawi ya nkhondoyi abatizidwe.”

Anasemphana Maganizo pa Nkhani ya Makadi ku Jakarta

Pa nthawi ya nkhondoyi abale anakumananso ndi vuto lina. Akuluakulu a boma la Japan analamula anthu onse ochokera m’mayiko ena kuti adule khadi losonyeza kuti azimvera ulamuliro wa boma la Japan. Lamuloli linkagwiranso ntchito kwa anthu a ku China omwe anali nzika za ku Indonesia. Anawalamulanso kuti khadili aziyenda nalo nthawi zonse. Lamuloli linachititsa abale kudzifunsa kuti, ‘Kodi tikalembetse n’kusainira khadili kapena tikane?’

Mlongo Josephine Elias ali ndi mchimwene wake Felix

M’bale Tan ananena kuti: “Abale amumzinda wa Jakarta anauza abale amene tinkakhala mumzinda wa Sukabumi kuti tikane kudula khadilo. Koma ife tinaganiza zoyankhula ndi akuluakulu a boma kuti atilole kusintha mawu ena pakhadipo. Tinawapempha kuti tisinthe mawu akuti, ‘Ndikulumbira kuti nthawi zonse ndizimvera boma la Japan,’ ndipo tinawapempha kuti palembedwe zoti, ‘Sindizilimbana ndi zochita za asilikali a boma la Japan.’ Tinadabwa kwambiri kuti anatilola ndipo tonse tinadula makadiwo. Koma abale a ku Jakarta atamva zimenezi, ananena kuti ndife ampatuko ndipo anasiya kuyankhulana nafe.”

Zinali zomvetsa chisoni kuti abale ambiri a ku Jakarta, omwe ankakhwimitsa zinthu kwambiri, anamangidwa ndipo anasiya choonadi. M’bale wina amene sankagwirizana ndi zosintha mawu a pakhadi aja, anamangidwa n’kuikidwa m’ndende imodzi ndi M’bale André Elias. M’bale Elias anati: “Tili m’ndendemo, ndinamufotokozera chifukwa chimene chinachititsa kuti abale a ku Sukabumi tidule makadi. Ndinamuthandizanso kuti ayambe kuona zinthu moyenera. M’baleyo anamvetsa ndipo anapepesa chifukwa chosiya kuyankhula nafe poganiza kuti ndife ampatuko. Pa nthawi yonse imene tinakhala limodzi ndi m’baleyo m’ndende, tinkalimbikitsana mpaka pamene anamwalira chifukwa cha nkhanza zimene ankatichitira.

Ankatikakamiza Kuti Tizinena Kuti Merdeka!

Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itatha m’chaka cha 1945, abale ndi alongo anapitiriza kugwira ntchito yolalikira mwakhama. M’bale wina amene anamangidwa komanso kuzunzidwa kwa zaka 4, analemba kalata yopita ku ofesi ya nthambi ku Australia. Iye anati: “Ngakhale kuti ndakhala m’ndende kwa zaka 4, ndidakali wolimba komanso sindinasinthe maganizo anga. Ndinakumana ndi mavuto komabe sindinaiwale abale anga. Ndikupempha kuti munditumizireko mabuku.”

Mabuku amene abalewa ankawafunitsitsa anayamba kufika pang’onopang’ono ndipo patapita nthawi anayamba kufika ambiri. Kenako kagulu ka abale okwana 10 a ku Jakarta kanayamba kumasulira mabuku m’Chiindoneziya.

Pa 17 August, 1945, atsogoleri a chipani chomenyera ufulu wa anthu m’dziko la Indonesia, analengeza kuti dziko la Indonesia ndi loima palokha. Zimenezi zinachititsa kuti kwa zaka 4 anthu a m’dzikoli azichita zipolowe polimbana ndi ulamuliro wopondereza wa atsamunda. Anthu ambiri anafa pa nthawiyi ndipo enanso oposa 7 miliyoni ankasowa pokhala.

Pa nthawi yovutayi, abale ndi alongo anapitiriza kulalikira kunyumba ndi nyumba. Mlongo Elias ananena kuti: “Achipani chomenyera ufulu wa anthu chija anatikakamiza kuti tizinena nawo mawu akuti ‘Merdeka,’ kutanthauza kuti ‘Ufulu.’ Koma tinawauza kuti ife sitilowerera ndale.” Kenako m’chaka cha 1949 boma la atsamunda lija linapereka ufulu wodzilamulira ku dziko la Indonesia. *

Pofika m’chaka cha 1950, ntchito yolalikira ku Indonesia inali itasokonezedwa ndi mavuto a zandale kwa zaka pafupifupi 10. Mavutowa atatha, abale anali ndi ntchito yaikulu yolalikira. Koma kodi akanakwanitsa bwanji kugwira ntchitoyi? Poyamba zinkaoneka ngati zosatheka. Koma chifukwa chodalira Yehova kuti ‘atumiza antchito kukakolola,’ abale anapitiriza kugwira ntchitoyi mwakhama. (Mat. 9:38) Ndipo Yehova anawathandizadi.

^ ndime 2 Nkhondoyo itatha, mmodzi wa ana aakazi a Mlongo Harp, dzina lake Hermine Mimi, analowa nawo m’Sukulu ya Giliyadi ndipo anabwerera ku Indonesia kukatumikira monga mmishonale.

^ ndime 4 Dziko la Netherlands linapitiriza kulamulira zilumba za West New Guinea mpaka m’chaka cha 1962. Panopa zilumbazi zimadziwika ndi dzina lakuti West Papua.