Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

INDONESIA

Poyamba Anali Mtsogoleri wa Zigawenga Koma Kenako Anakhala Nzika Yabwino

Hisar Sormin

Poyamba Anali Mtsogoleri wa Zigawenga Koma Kenako Anakhala Nzika Yabwino
  • CHAKA CHOBADWA 1911

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1952

  • MBIRI YAKE Poyamba anali mtsogoleri wa zigawenga koma patapita nthawi anakhala m’Komiti ya Nthambi.

PA NTHAWI ina, M’bale Sormin anaitanidwa kuti akaonekere pamaso pa mkulu wa ofufuza milandu.

Mkuluyo ananena kuti: “Iwe ndiwe nzika ya dziko lino, ndiye ndikufuna kuti undiuze zoona zokhazokha. Kodi a Mboni za Yehova amachita chiyani kwenikweni ku Indonesia kuno?”

M’bale Sormin anayankha kuti: “Bwanji choyamba ndikufotokozereni mbiri yanga. Poyamba ndinali mtsogoleri wa zigawenga zoopsa kwambiri koma panopa ndimaphunzitsa anthu Baibulo. Zimenezi n’zimene a Mboni za Yehova amachita ku Indonesia kuno. Amathandiza anthu omwe anali ndi makhalidwe oipa ngati ineyo, kuti asinthe n’kukhala nzika zabwino.”

Patapita nthawi, mkuluyo anauza anthu ena kuti: “Ndimamva anthu ambiri akudandaula za a Mboni za Yehova. Koma ndimadziwa kuti ndi chipembedzo chabwino chifukwa anathandiza anthu ngati Bambo Sormin kuti asinthe.”