Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Indonesia

Indonesia

WERENGANI nkhani yosangalatsa yonena za Akhristu odzichepetsa amene anakhalabe olimba mtima pa nthawi imene ankakumana ndi mavuto. Iwo anakumana ndi mavutowa chifukwa cha kusintha kwa zinthu pa nkhani zandale, mikangano ya zipembedzo, komanso kuletsedwa kwa ntchito yawo kwa zaka 25 kumene atsogoleri azipembedzo anachititsa. Mupezanso nkhani ya m’bale amene dzina lake linali pa gulu la anthu omwe ankayenera kuphedwa ndi chipani cha Chikomyunizimu. Mulinso nkhani ya munthu wina yemwe poyamba anali mtsogoleri wa gulu lina la zigawenga koma panopa ndi Mkhristu wodalirika. Muwerenganso nkhani yosangalatsa ya atsikana awiri omwe ali ndi vuto losamva, amene anayamba kugwirizana kwambiri koma kenako anazindikira kuti ndi pachibale. Mudziwanso mmene ntchito ya anthu a Yehova ikuyendera pamene akulalikira uthenga wabwino kwa anthu ambiri omwe ndi achisilamu.

M'CHIGAWO ICHI

Mfundo Zachidule Zokhudza Dziko la Indonesia

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mfundo zachidule zokhudza dziko, anthu komanso chikhalidwe cha anthu a ku Indonesia. Dzikoli ndi lomwe lili ndi zilumba zambiri padziko lonse lapansi.

Malonda a Zokometsera Chakudya

M’zaka za m’ma 1500, malonda a zokometsera chakudya ndi amene ankabweretsa ndalama m’mayiko ambiri.

Ndikufuna Kukayambira Apa

Apainiya olimba mtima ochokera ku Australia anapirira mavuto ambiri pamene ankagwira ntchito yolalikira koyamba ku Indonesia.

Njira Zimene Poyamba Ankagwiritsa Ntchito Polalikira

Kulalikira pa wailesi ndi m’madoko kumene a Mboni za Yehova ankachita, kunakhumudwitsa anthu amene ankadana ndi choonadi ku Indonesia.

Kunayambika Kagulu Kenakake ka Chipembedzo

Poyamba anthu a m’kaguluka ankatsatira mfundo zimene ankawerenga m’mabuku a Mboni za Yehova. Koma patapita nthawi, anayamba kuyendera maganizo awo.

Ankaona Kuti Kukhala pa Ubwenzi ndi Yehova N’kofunika Kwambiri

Gulu la anthu olusa linathyola chitseko cha nyumba ya a Thio Seng Bie akuona. Anthuwa anatenga katundu wina n’kusiya katundu amene mwiniwake ankaona kuti ndi wamtengo wapatali.

Ntchito Yolalikira Inabala Zipatso ku West Java

A Mboni anapitiriza kulalikira mosamala kwambiri pa nthawi imene mabuku awo analetsedwa.

Ulamuliro Wankhanza wa Boma la Japan

Pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, a Mboni ena anapeza njira yodulira makadi mosalimbana ndi boma la Japan kapenanso mosalowerera ndale.

Mpainiya Wopanda Mantha

M’bale André Elias anatumikira kwa zaka 60 ndipo anakhalabe wokhulupirika pa nthawi imene ankafunsidwa mafunso komanso kuopsezedwa.

Amishonale Anayamba Kufika ku Indonesia

Amishonale oyambirira kufika m’dzikoli anathandiza kupititsa patsogolo ntchito yolalikira mofulumira kwambiri.

Ntchito Yolalikira Inafika Mpaka ku Zilumba Zakum’mawa

Kodi atsogoleri achipembedzo anakwanitsanso kulepheretsa ntchito yolalikira?

Amishonale Enanso Anafika

Chapakatikati pa zaka za m’ma 1970, zinthu zinayamba kusintha moti zinali zovuta kulalikira uthenga wabwino.

Ankachita Zinthu Ngati Sara Weniweni

Mlongo Titi Koetin ankalemekeza kwambiri mwamuna wake ndipo zimenezi zinathandiza kwambiri banja lake.

Msonkhano Wosaiwalika

Msonkhano wa mayiko wa mutu wakuti, “Uthenga Wabwino Wosatha” wa mu 1963, unachitikabe ngakhale kuti abale anakumana ndi mavuto osiyanasiyana.

Anachita Upainiya Wapadera kwa Zaka 50

M’chaka cha 1964 ku West Papua, m’busa wina wa tchalitchi cha Chipulotesitanti anayankhula mwaukali kuti: “Ndithetsa gulu la Mboni za Yehova ku Manokwari kuno.” Kodi iye anachitadi zimenezi?

Poyamba Anali Mtsogoleri wa Zigawenga Koma Kenako Anakhala Nzika Yabwino

Mkulu wa ofufuza milandu anafunsa a Mboni za Yehova kuti: Kodi a Mboni za Yehova amachita chiyani kwenikweni ku Indonesia kuno?

Anatsimikiza Mtima Kuti Sabwerera M’mbuyo

N’chiyani chinachititsa anthu ena kunena kuti, “A Mboni za Yehova ali ngati misomali”?

Sanasiye Kusonkhana

A Mboni za Yehova ataloledwanso kuti azigwira ntchito yawo mwaufulu, mkulu wina wa boma ananena kuti: “Sichikalatachi chimene chikukupatsani ufulu wopembedza.”

Amakondana Ngakhale pa Nthawi ya Mavuto

A Mboni za Yehova akuthandiza abale mwamsanga chivomezi chitawononga tauni ya Gunungsitoli ku Indonesia.

Sitinalole Kusiya Zimene Timakhulupirira

Daniel Lokollo amakumbukira mmene olondera ndende anamuzunzira.

Tinapulumuka Chifukwa Chotsatira Malangizo

Kumenyana kwa Asilamu ndi Akhristu ku Indonesia kunabweretsa mavuto kwa a Mboni za Yehova.

Ntchito Yathu Inayambanso Kuyenda Bwino

Ntchito yathu itavomerezedwanso, panachitika zinthu zikuluzikulu zitatu zomwe zinathandiza anthu ambiri.

Abale Ankalengeza za Yehova Molimba Mtima

Kodi a Mboni za Yehova anachita zotani kuti zinthu ngati chikhalidwe ndi zizolowezi zoipa zisawalepheretse kulalikira molimba mtima?

Ofesi ya Nthambi Yomwe Ili M’mwamba Kwambiri

Abale ndi alongo olalikira kumadera ofunika ofalitsa ambiri akhala akufunafuna gawo la anthu ofuna kudziwa choonadi ndipo alipeza.

“Yehova Anatichitira Zinthu Zoposa Zimene Tinkayembekezera”

Mpingo wa m’mudzi wa Tugala Oyo, ku Indonesia, unadalitsidwa kwambiri.

Tinasangalala Titadziwa Kuti Ndife Pachibale

Atsikana awiri apachibale m’dziko la Indonesia anawasiyanitsa wina ataperekedwa kuti akaleredwe ndi banja lina koma kuphunzira Baibulo kunawathandiza kuti akumanenso.