MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muzithandiza Anthu Osapembedza Kudziwa Mlengi Wawo
Kodi mumalephera kulalikira anthu osapembedza poganiza kuti mwina samvetsera uthenga wanu? Ngati ndi choncho, muzikumbukira kuti anthu ambiri amene sanali m’chipembedzo chilichonse, kuphatikizapo amene ankati kulibe Mulungu, anakhala a Mboni za Yehova. Nthawi zambiri anthu amenewa amangofunika kuwathandiza kupeza umboni woti kuli Mulungu.—Aro 1:20; 10:14.
ONERANI VIDIYO YAKUTI ANTHU OPANDA CHIKHULUPIRIRO AKHOZA KUSINTHA N’KUKHALA NDI CHIKHULUPIRIRO—ANTHU OSAPEMBEDZA, KENAKO YANKHANI FUNSO LOTSATIRALI:
Kodi zomwe zinachitikira Tommaso zakuthandizani bwanji kukhala ndi maganizo oyenera kuti muzilalikira kwa anthu osapembedza?