MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Pitirizani Kuganizira Zimenezi”
Kuganizira chiyani? Lemba la Afilipi 4:8 limati, tiziganizira zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambiri, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zachikondi, zilizonse zoyamikirika, khalidwe labwino lililonse, ndi chilichonse chotamandika. Komabe sikuti Akhristu amafunika kuti azingoganizira za Baibulo basi. Akhoza kumaganiziranso zinthu zina, koma ziyenera kukhala zimene Yehova angasangalale nazo. Sitiyenera kuganizira zinthu zomwe zingatichititse kuti tisiye kukhala okhulupirika kwa Yehova.—Sal. 19:14.
Nthawi zina zimakhala zovuta kuti tisamaganizire zinthu zoipa. Zili choncho chifukwa timalimbana ndi thupi lathu lochimwali komanso Satana yemwe ndi “mulungu wa nthawi ino.” (2 Akor. 4:4) Popeza Satana ndiye wolamulira wadzikoli, zinthu zambiri zomwe zimapezeka pa intaneti, m’mabuku komanso zimene zimaulutsidwa pawailesi kapena pa TV zimakhala zoipa. Ngati sitingasankhe bwino, zinthu zimenezi zikhoza kuwononga maganizo athu ndipo n’kupita kwa nthawi tingayambe kuchita zoipa.—Yak. 1:14, 15.
ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIPEWA ZINTHU ZIMENE ZINGAWONONGE KHALIDWE LANU LA KUKHULUPIRIKA—ZOSANGALATSA ZOSAYENERA. KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Kodi m’bale wa m’vidiyoyi amaonera zinthu zotani pafoni yake, nanga zinamukhudza bwanji?
-
Kodi lemba la Agalatiya 6:7, 8 ndi Salimo 119:37, linamuthandiza bwanji?