October 14-20
1 Petulo 1-2
Nyimbo Na. 29 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Khalani Oyera”: (10 min.)
[Onerani vidiyo ya Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la 1 Petulo.]
1 Pet. 1:14, 15—Khalidwe lathu komanso zomwe timaganiza ziyenera kukhala zoyera (w17.02 9 ¶5)
1 Pet. 1:16—Tiziyesetsa kutsanzira Mulungu wathu, amene ndi woyera (lvs 77 ¶6)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
1 Pet. 1:10-12—Kodi tingakhale bwanji akhama mofanana ndi aneneri komanso angelo? (w08 11/15 21 ¶10)
1 Pet. 2:25—Kodi woyang’anira wathu wamkulu ndi ndani? (it-2 565 ¶3)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) 1 Pet. 1:1-16 (th phunziro 10)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi.
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba. (th phunziro 1)
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire munthu amene wanena zinthu zina zomwe anthu amakonda kunena ngati sakufuna kuti tikambirane nawo.(th phunziro 3)
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Kenako mugawireni chilichonse cha zinthu zomwe timagwiritsa ntchito pophunzitsa.(th phunziro 9)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Khalani Bwenzi la Yehova—Uzikhala Waukhondo: (6 min.) Onerani vidiyoyi. Kenako itanani ana omwe munawasankhiratu kuti abwere kutsogolo ndipo muwafunse mafunso otsatirawa: Kodi Mulungu anaika bwanji chilichonse pamalo ake? N’chiyani chimathandiza kuti mvuwu zikhale zaukhondo? N’chifukwa chiyani muyenera kumakonza kuchipinda kwanu?
“Yehova Amakonda Anthu Aukhondo”: (9 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti, Mulungu Amakonda Anthu Aukhondo.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 55
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 124 ndi Pemphero