Muzipereka Zinthu Zabwino Kwambiri kwa Yehova
Yehova amasangalala ndi nsembe zathu zabwino ndipo amatidalitsa
TIKAKHALA PA UBWENZI NDI YEHOVA
-
Timapereka kwa Yehova nsembe zathu zomutamanda
-
Yehova amatikhululukira, amatikonda komanso timakhala naye pa ubwenzi
-
Timayamikira madalitso amene timapeza chifukwa chomvera malamulo a Yehova ndipo izi zimatithandiza kuti tizifunitsitsa kumutumikirabe
Kodi ndingatani kuti ndizipereka kwa Yehova zinthu zabwino kwambiri?