NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU November 2019
Zimene Tinganene
Zitsanzo za zimene tinganene zofotokoza cholinga chimene Mulungu analengera anthu komanso zomwe walonjeza m’tsogolomu.
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Musamakonde Dziko Kapena Zinthu za M’dziko
N’chiyani chimene tingachite kuti zinthu zam’dzikoli zisatilepheretse kutumikira Yehova?
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Musamatengere Maganizo a M’dzikoli Mukamakonzekera Ukwati
Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zomwe zingathandize anthu amene akufuna kukwatirana kukonzekera bwino tsiku la ukwati wawo kuti asadzadziimbe mlandu kapena kunong’oneza bondo?
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Tiyenera Kuchita Khama Kuti Tikhalebe m’Choonadi
Kodi tingatani kuti ‘tizimenya mwamphamvu nkhondo yachikhulupiriro’?
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Ndikudziwa Ntchito Zako”
Yesu amadziwa chilichonse chomwe chikuchitika mumpingo ndipo ndi amene amatsogolera mabungwe a akulu.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Yehova Amadziwa Zimene Timafunikira
N’chifukwa chiyani msonkhano wachigawo uliwonse umakhala wapanthawi yake? N’chiyani chimachititsa kuti misonkhano ya mkati mwa mlungu izikhala yolimbikitsa komanso yothandiza?
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Anthu 4 Okwera Pamahatchi
Masiku ano tikuona zotsatira za anthu 4 okwera pamahatchi otchulidwa m’buku la Chivumbulutso. Kodi okwera pamahatchi amenewa akuimira chiyani?
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Yehova Amakonda Munthu Wopereka Mokondwera
Kodi mungapereke bwanji ndalama zothandizira ntchito yomwe a Mboni za Yehova amagwira padziko lonse?