May 5-11
MIYAMBO 12
Nyimbo Na. 101 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Kugwira Ntchito Mwakhama Kumapindulitsa
(10 min.)
Musamawononge nthawi ndi zinthu zopanda ntchito (Miy 12:11)
Muzigwira ntchito mwakhama ndipo muzichita zonse zomwe mungathe (Miy 12:24; w16.06 31 ¶1)
Mukamagwira ntchito mwakhama, mudzapindula (Miy 12:14)
ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI: Kugwira ntchito mwakhama kumakhala kosangalatsa tikamaganizira mmene zomwe tikuchitazo zingathandizire anthu ena.—Mac 20:35; w15 2/1 5 ¶4-6.
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
-
Miy 12:16—Kodi mfundo ya palembali ingathandize bwanji munthu kukhala wopirira pamene akukumana ndi mavuto? (ijwyp nkhani na. 95 ¶10-11)
-
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Miy 12:1-20 (th phunziro 5)
4. Ulendo Woyamba
(2 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. (lmd phunziro 1 mfundo 4)
5. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. M’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo. (lmd phunziro 5 mfundo 4)
6. Ulendo Wobwereza
(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Sonyezani munthu amene ali ndi ana webusaiti yathu. (lmd phunziro 9 mfundo 3)
7. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira
(3 min.) Chitsanzo. ijwfq nkhani na. 3—Mutu: Kodi Mumakhulupirira Kuti Chipembedzo Cholondola N’chanu Chokha? (lmd phunziro 4 mfundo 3)
Nyimbo Na. 21
8. Yehova Amatithandiza Tikamakumana ndi Mavuto Azachuma
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Kodi mukuda nkhawa kuti mupeza bwanji ntchito kapena kuti ntchito yanu ikhoza kutha? Kapenanso mukuda nkhawa kuti muzipeza bwanji zofunika pa moyo panopa kapena mukadzakalamba? Chuma cha m’dzikoli ndi chosadalirika. Komabe, Yehova amatitsimikizira kuti ngati titamudalira, adzapitiriza kutipatsa zofunika pa moyo ngakhale zinthu zitasintha kwambiri pa nkhani ya zachuma.—Sl 46:1-3; 127:2; Mt 6:31-33.
Onerani VIDIYO yakuti Yehova Sanatisiye. Kenako funsani funso lotsatirali:
-
Kodi mwaphunzira chiyani kuchokera pa zimene zinachitikira M’bale Alvarado?
Werengani 1 Timoteyo 5:8. Kenako funsani funso lotsatirali:
-
Kodi lembali lalimbitsa bwanji chikhulupiriro chanu chakuti Yehova amathandiza atumiki ake kupeza zinthu zofunika pa moyo nthawi zonse?
Taganizirani mfundo za m’Baibulo zotsatirazi zomwe zingakuthandizeni kupirira mukamakumana ndi mavuto azachuma:
-
Muzikhala moyo wosalira zambiri. Muzipewa ngongole komanso kugula zinthu zosafunika.—Mt 6:22
-
Muzisankha ntchito komanso maphunziro amene angakuthandizeni kuika zinthu zauzimu pa malo oyamba.—Afi 1:9-11
-
Muzikhala odzichepetsa komanso muzivomereza zinthu zikasintha. Ngati mukufunafuna ntchito, muzigwira ntchito iliyonse imene ingapezeke ngakhale itaoneka yonyozeka n’cholinga choti muzikwanitsa kupezera banja lanu zinthu zofunika pa moyo.—Miy 14:23
-
Muzikhala ofunitsitsa kugawana ndi ena zimene muli nazo, ngakhale zitakhala zochepa.—Ahe 13:16
9. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 26 ¶1-8, bokosi patsamba 204 ndi 208