May 12-18
MIYAMBO 13
Nyimbo Na. 34 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Musamapusitsike ndi “Nyale ya Anthu Oipa”
(10 min.)
Anthu oipa alibe tsogolo (Miy 13:9; it-2 196 ¶2-3)
Musamachite zinthu ndi anthu amene amaona kuti zoipa n’zabwino (Miy 13:20; w12 7/15 12 ¶3)
Yehova amadalitsa anthu olungama (Miy 13:25; w04 7/15 31 ¶6)
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
-
Miy 13:24—Kodi lembali likutichenjeza chiyani pa nkhani ya chikondi chosayenera? (it-2 276 ¶2)
-
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Miy 13:1-17 (th phunziro 10)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Pambuyo pokambirana nkhani imene yangochitika kumene, werengani naye lemba limene lingamusangalatse. (lmd phunziro 2 mfundo 5)
5. Ulendo Woyamba
(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Muitanireni kumisonkhano yathu. (lmd phunziro 2 mfundo 3)
6. Nkhani
(5 min.) lmd zakumapeto A mfundo 9—Mutu: Ana Omwe Amalemekeza ndi Kumvera Makolo Awo Zinthu Zimawayendera Bwino. (th phunziro 16)
Nyimbo Na. 77
7. “Kuwala kwa Nyale ya Anthu Olungama Kukuwonjezeka Kwambiri”
(8 min.) Nkhani yokambirana.
M’Mawu a Mulungu muli malangizo anzeru kwambiri. Tikamadalira Mawu a Mulungu kuti azititsogolera, zinthu zimatiyendera bwino ndipo timakhala osangalala. Zimenezi sitingazipeze kulikonse m’dzikoli.
Onerani VIDIYO yakuti Dziko Silingakupatse Zinthu Zimene Lilibe. Kenako funsani funso lotsatirali:
-
Kodi zimene zinachitikira Mlongo Gainanshina zikusonyeza bwanji kuti “nyale ya anthu olungama” imaposa “nyale ya anthu oipa”?—Miy 13:9
Musamataye nthawi yanu ndi kuganizira zinthu zam’dzikoli kapena kunong’oneza bondo chifukwa cha zimene munasankha n’cholinga choti mutumikire Yehova. (1Yo 2:15-17) M’malomwake, muziganizira ‘zinthu zamtengo wapatali’ zimene munapeza.—Afi 3:8.
8. Zofunika Pampingo
(7 min.)
9. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 26 ¶9-17